KODI nthaŵi zina umamva chisoni kapena kuona ngati uli wekhawekha wopanda wina wokuthandiza?— Kodi nthaŵi zina umakayika ngati alipo munthu amene amakukonda?— Ana ena amamva choncho. Koma Mulungu amalonjeza kuti: ‘Ine sindingaiwale iwe.’ (Yesaya 49:15) Kodi si zosangalatsa kuganizira zimenezi?— Inde, Yehova Mulungu amatikondadi kwambiri!

Kodi ukuganiza kuti kankhosa aka kamene kasochera kakumva bwanji?

Munthu wina amene analemba Baibulo ananena kuti: “Pakuti wandisiya atate wanga ndi amayi wanga, koma Yehova anditola.” (Salmo 27:10) Kudziŵa mfundo imeneyi ndi kolimbikitsa kwambiri, kodi si choncho?— Eya, Yehova amatiuza kuti: ‘Usaope, pakuti Ine ndili pamodzi ndi iwe. Ine ndidzakuthandizadi iwe.’Yesaya 41:10.

Komabe nthaŵi zina Yehova amalola Satana kutivutitsa. Yehova amalola Satana kuyesa ngakhale atumiki Ake. Nthaŵi ina Mdyerekezi anachititsa Yesu kuvutika kwambiri mpaka Yesu anafuula kwa Yehova kuti: ‘Mulungu wanga, Mulungu wanga, ndi chifukwa chiyani mwandisiya?’ (Mateyu 27:46) Ngakhale kuti Yesu anali kuvutika, iye anadziŵa kuti Yehova amamukonda. (Yohane 10:17) Koma Yesu analinso kudziŵa kuti Mulungu amalola Satana kuyesa atumiki Ake ndiponso kuti amalola Satana kuwavutitsa. Tidzafotokoza m’mutu wina chifukwa chake Mulungu amalola Satana kuchita zimenezi.

Pamene tili aang’ono, nthaŵi zina sitichedwa kuchita mantha. Mwachitsanzo, kodi unayamba wasocherapo?— Kodi unaopa kwambiri?— Ana ambiri amaopa. Nthaŵi ina Mphunzitsi Waluso anasimba nkhani inayake yonena za kusochera. Komatu imene inasocherayo inali nkhosa osati mwana ngati iweyo.

Pambali ina iweyo uli ngati nkhosa. Motani? Nkhosa si nyama  zikuluzikulu kapenanso zamphamvu. Ndipo zimafuna kuti winawake azizisamalira ndi kuziteteza. Munthu amene amasamalira nkhosa amatchedwa mbusa.

Yesu mu nkhani yake anasimba za mbusa amene anali ndi nkhosa 100. Koma kenako imodzi inasochera. Mwina iyo inafuna kukaona zimene zinali kuseri kwa phiri. Koma mosakhalitsa nkhosayo inapita kutali kwambiri ndi zinzake. Kodi ukuganiza kuti nkhosayo inamva bwanji itaona kuti ili yokhayokha zinzake zonse zapita?—

Kodi mbusa akanatani ataona kuti nkhosa imodziyo panalibe? Kodi akananena kuti ndi zosadandaulitsa inalakwa ndi nkhosayo? Kapena kodi nkhosa 99 zinazo akanazisunga pamalo abwino ndi kupita kukayang’ana imodziyo? Kodi nkhosa imodzi yokha ingafunike kuivutikira chonchi?— Iweyo ukanakhala nkhosa yosocherayo, kodi ukanafuna kuti mbusa akuyang’ane?—

Who is like the shepherd that has rescued his sheep?

Mbusa uja nkhosa zake zonse anali kuzikonda kwambiri, kuphatikizapo imene inasoŵayo. Choncho anapita kukayang’ana yosoŵayo. Tsono taganizira mmene nkhosa yosocherayo inasangalalira itaona mbusayo akubwera! Ndipo Yesu ananena kuti mbusayo anasangalala kuti anapeza nkhosa yake. Anasangalala kwambiri ndi nkhosa imeneyo kuposa mmene anasangalalira  ndi nkhosa 99 zija zomwe sizinasochere. Ndiyeno, kodi ndani amene ali ngati mbusa ameneyu wa mu nkhani ya Yesu? Ndani amene amatisamalira kwambiri mofanana ndi mmene mbusayu anasamalirira nkhosa zake?— Yesu ananena kuti Atate ake akumwamba ndiwo amatisamalira choncho. Ndipo Atate ake ndi Yehova.

Yehova Mulungu ndi Mbusa Wamkulu wa anthu ake. Iye amakonda aliyense amene amamutumikira, kuphatikizapo ana monga iweyo. Safuna kuti wina aliyense wa ife apweteke kapena awonongeke. Ndithudi ndi zolimbikitsa kwambiri kudziŵa kuti Mulungu amatisamalira kwambiri moteromo!—Mateyu 18:12-14.

Kodi umaona kuti Yehova alipodi, monga mmene umaonera atate ako kapena munthu wina?

Kodi iwe Yehova Mulungu umamukhulupiriradi?— Kodi umaona kuti iye alipodi?— Ndi zoona kuti Yehova sitingamuone. Sitingamuone chifukwa iye ndi Mzimu. Ali ndi thupi losaoneka ndi maso athu. Komatu iye ndi munthudi woti alipo, ndipo amationa. Amadziŵa kuti tikufunika thandizo. Ndipo tingalankhule naye m’pemphero, mofanana ndi mmene  timalankhulira ndi munthu wina padziko lapansi pano. Yehova amafuna kuti tizichita zimenezi.

Ndiye ngati utati ukumva chisoni kapena ukuona ngati uli wekhawekha wopanda wokuthandiza, kodi uyenera kuchita chiyani?— Uyenera kulankhula ndi Yehova. Uzimuyandikira, ndipo iye adzakutonthoza ndi kukuthandiza. Uzikumbukira kuti Yehova amakukonda, ngakhale pamene ukuona ngati uli wekhawekha. Tatenga Baibulo. Taona zimene Salmo 23 likutiuza, kuyambira pa vesi 1: “Yehova ndiye mbusa wanga; sindidzasoŵa. Andigonetsa ku busa lamsipu: anditsogolera ku madzi odikha.”

Tsopano ona zimene wolembayu ananena mu vesi 4: “Inde, ndingakhale ndiyenda mu chigwa cha mthunzi wa imfa, sindidzaopa choipa; pakuti Inu muli ndi ine: chibonga chanu ndi ndodo yanu, izi zindisangalatsa ine.” Umu ndi mmene amamvera anthu amene Mulungu wawo ndi Yehova. Amatonthozedwa akakhala pamavuto. Kodi iwenso umamva chonchi?—

Monga mmene mbusa wokonda nkhosa zake amazisamalira bwino, Yehovanso amasamalira bwino kwambiri anthu ake. Iye amawasonyeza njira yabwino yoti ayendemo, ndipo iwo amamutsatira mosangalala. Iwo safunika kuopa ngakhale akhale pakati pa mavuto. Mbusa amagwiritsa ntchito chibonga chake kapena ndodo yake poteteza  nkhosa ku nyama zolusa. Baibulo limatiuza mmene mbusa wachinyamata Davide anatetezera nkhosa zake ku mkango ndi chimbalangondo. (1 Samueli 17:34-36) Ndipo anthu a Mulungu amadziŵa kuti naye Yehova adzawateteza. Amaona kuti ndi otetezeka chifukwa Mulungu ali nawo.

Mofanana ndi mbusa amene akuteteza nkhosa zake, kodi ndani amene angatithandize tikakhala pamavuto?

Yehova amakonda nkhosa zake kwambiri, ndipo amazisamalira bwino. Baibulo limanena kuti: ‘Iye adzadyetsa nkhosa zake ngati mbusa. Adzasonkhanitsa ana a nkhosa ndi manja ake.’—Yesaya 40:11.

Kodi sukusangalala kuti wadziŵa kuti ndimo mmene Yehova alili?— Kodi iwe ukufuna kukhala nkhosa yake?— Nkhosa zimamvera mawu a mbusa wawo. Zimayandikana naye. Kodi iwe Yehova umamumvera?— Kodi umayandikana naye?— Ndiye kuti sufunika kuchita mantha. Yehova adzakuthandiza.

Yehova amakonda ndi kusamalira anthu amene amamutumikira. Tiye tiŵerengere limodzi zimene Baibulo limanena pankhaniyi, pa Salmo 37:25; 55:22; ndi Luka 12:29-31.