Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

 Mutu 13

Amene Anakhala Ophunzira a Yesu

Amene Anakhala Ophunzira a Yesu

Kodi munthu uyu ndani, nanga anakhala wophunzira wa Yesu motani?

KODI ukuganiza kuti ndani amene anali mtumiki wa Mulungu wabwino kuposa onse?— Wayankha bwino, anali Yesu Kristu. Nanga ukuganiza kuti ife tikhoza kukhala ngati iyeyo?— Eya, Baibulo limanena kuti iye anatipatsa chitsanzo choti titsatire. Ndipo iye amatiuza kuti tikhale ophunzira ake.

Kodi ukudziŵa zimene zimafunika kuti munthu akhale wophunzira wa Yesu?— Pamafunikatu zinthu zambiri. Choyamba, tiyenera kuphunzira kwa iye. Koma si zokhazo ayi. Tiyeneranso kukhulupiriradi zimene iye amanena. Tikamazikhulupirira ndiye kuti tidzachita zimene iye amatiuza.

Anthu ambiri amanena kuti amakhulupirira Yesu. Kodi ukuganiza kuti anthu onsewo alidi ophunzira ake?— Ayi, ambiri a iwo si ophunzira ake. Inde mwina iwo amapita ku tchalitchi. Komatu ochuluka sanayambe akhalapo ndi nthaŵi yophunzira zimene Yesu anaphunzitsa. Ndithudi, ophunzira a Yesu ndi okhawo amene amatsatira chitsanzo chake.

Tiye tikambirane za anthu ena amene anali ophunzira a Yesu pamene iye anali munthu padziko lapansi. Mmodzi wa oyambirira kukhala ophunzira ake anali Filipo. Filipo anapita kukauza mnzake Natanayeli (yemwe anali kutchedwanso kuti Bartolomeyo). Natanayeli ndi uyu ali patsinde pa mtengo pa chithunzi ichi. Pamene Natanayeli anafika kwa Yesu, Yesu anati: ‘Onani munthu woona  mtima, Mwisrayeli weniweni.’ Natanayeli anadabwa moti anafunsa kuti: “Munandidziŵira kuti?”

Kodi Yesu akuitana ndani kuti akhale ophunzira ake?

Yesu anati: ‘Ndinakuona Filipo asanakuitane muja unakhala pansi pa mtengo wa mkuyu paja.’ Natanayeli anadabwa kwambiri kuti Yesu anadziŵa malo enieni amene iye anali. Motero Natanayeli ananena kuti: “Inu ndinu Mwana wa Mulungu, ndinu Mfumu ya Israyeli.”—Yohane 1:49.

Yudasi Isikariyoti, Yudasi (yemwe ankadziwikanso kuti Tadeyo), Simoni

Filipo ndi Natanayeli anakhala ophunzira a Yesu patapita tsiku limodzi anthu ena atakhala kale ophunzira ake. Anthu ameneŵa anali Andreya ndi mkulu wake Petro, ndiponso Yohane ndi mwinamwake mkulu wake wa Yohaneyo, Yakobo. (Yohane 1:35-51) Komabe patapita kanthaŵi kochepa, anthu folo ameneŵa anakayambiranso ntchito yawo ya kupha nsomba. Ndiyeno tsiku lina pamene Yesu anali kuyenda m’mbali mwa nyanja ya Galileya, anaona Petro ndi Andreya akuponya ukonde wawo wophera nsomba m’nyanja. Yesu anawaitana nati: ‘Tiyeni muzinditsata.’

Yakobo (mwana wa Alifeyo), Tomasi, Mateyu

 Atayenda pang’ono, Yesu anaona Yakobo ndi Yohane. Anali kusoka maukonde awo ophera nsomba ali m’boti limodzi ndi atate awo. Yesu anawaitananso kuti azimutsatira. Kodi iweyo ungatani Yesu atakuitana? Kodi ukhoza kumutsatira nthaŵi yomweyo?— Anthu aŵatu Yesu anali kumudziŵa bwino. Anali kudziŵa kuti Mulungu ndiye anamutuma. Choncho nthaŵi yomweyo anasiya ntchito yawo yopha nsomba ndi kutsatira Yesuyo.—Mateyu 4:18-22.

Nataniyeli, Filipo, Yohane

Kodi anthu ameneŵa atayamba kutsatira Yesu, ndiye kuti basi kenako anali kuchita zinthu zabwino nthaŵi zonse?— Ayi. Iwe ukukumbukira kuti anthu aŵa anafika ngakhale pokangana kuti anali wamkulu ndani pakati pawo. Koma iwo anamvera Yesu ndipo anafunitsitsa kusintha maganizo awo ndi khalidwe lawo. Ngati ife tikufunitsitsa kusintha, nafenso tingakhale ophunzira a Yesu.

Yakobo (mkulu wake wa Yohane), Andireya, Petulo

Yesu anauza anthu osiyanasiyana kuti akhale ophunzira ake. Tsiku lina, wolamulira winawake wachinyamata wolemera kwambiri anakafunsa Yesu mmene angapezere moyo wosatha. Wolamulira wolemerayo atanena kuti wakhala akusunga malamulo a Mulungu kuyambira ali mwana, Yesu anamuuza kuti: ‘Bwera kuno, unditsate Ine.’ Kodi ukudziŵa chimene chinachitika kenako?—

Eya, munthuyu atauzidwa kuti kukhala wophunzira wa Yesu ndi chinthu chofunika kwambiri kuposa kukhala wolemera, sanasangalale m’pang’ono pomwe. Iye sanakhale wophunzira wa Yesu chifukwa ndalama zake anali kuzikonda kwambiri kuposa mmene anali kukondera Mulungu.—Luka 18:18-25.

Yesu atalalikira kwa pafupifupi chaka chimodzi ndi hafu, anasankha ophunzira 12 kuti akhale atumwi ake. Atumwi anali amuna amene iye anali kuwatuma kukagwira ntchito yapadera. Kodi mayina awo ukuwadziŵa?— Tiye tiyese kuwaphunzira. Ona zithunzi zawo izi, ndipo yesa kutchula mayina awo. Kenako uyese kunena mayinaŵa pamtima.

Kodi akazi aŵa ndani amene anathandiza Yesu pamene anapita kolalikira?

M’kupita kwa nthaŵi, mmodzi wa atumwi 12 ameneŵa anakhala woipa. Ameneyu anali Yudasi Isikariote. Pambuyo pake wophunzira  wina anasankhidwa kukhala mtumwi. Kodi ukudziŵa kuti anali ndani?— Anali Matiya. Kenako Paulo ndi Barnaba nawonso anakhala atumwi, koma sanali m’gulu la atumwi 12 aja.—Machitidwe 1:23-26; 14:14.

Ungakumbukire kuti m’Mutu 1 wa buku lino tinaphunzira kuti Yesu anali kukonda kucheza ndi ana. Paja n’chifukwa chiyani anali kuchita zimenezi?— Ndi chifukwa chakuti anadziŵa kuti iwonso akhoza kukhala ophunzira ake. Ndipotu nthaŵi zambiri ana amanena zinthu ndi mawu amene amachititsa ngakhale anthu akuluakulu kumvetsera ndi kufuna kuphunzira zambiri za Mphunzitsi Waluso.

Panalinso akazi ambiri amene anakhala ophunzira a Yesu. Akazi ena anali kutsagana naye popita  kukalalikira ku midzi ina. Ena a iwo anali Mariya Magadalene, Yohana, ndi Susana. Mwina iwo anali kumuthandizanso pophika zakudya ndi kuchapa zovala zake.—Luka 8:1-3.

Kodi iwe ukufuna kukhala wophunzira wa Yesu?— Tsonotu kumbukira kuti sitikhala ophunzira ake mwa kungonena kuti ndife ophunzira a Yesu. Kulikonse kumene tingakhale, tiyenera kuchita zinthu mosonyeza kuti ndife ophunzira ake, osati pamene tili pa misonkhano yachikristu pokha. Tandiuza malo ena amene iwe ukuganiza kuti ndi pofunika kuti tizichita zinthu monga ophunzira a Yesu.—

Inde, tizichita zimenezi tikakhala panyumba. Komanso kwina ndi kusukulu. Chimene iweyo ndi ine sitiyenera kuiwala ndi chakuti kuti tikhale ophunzira enieni a Yesu, m’pofunika kuti tsiku lililonse kuyambira m’mawa mpaka madzulo, ndiponso kwina kulikonse kumene tingakhale, tizichita zinthu monga mmene iye anachitira.

Kodi ndi kuti kumene ife tifunika kuchita zinthu monga ophunzira a Yesu?

Tsopano nonse ŵerengani zimene Baibulo limanena za ophunzira a Yesu pa Mateyu 28:19, 20; Luka 6:13-16; Yohane 8:31, 32; ndi 1 Petro 2:21.