MULUNGU WAMPHAMVUYONSE ndiye Mbuye wa chilengedwe chonse. Moyo umene tili nawo panopa ndiponso wa m’tsogolo umadalira iyeyo. Ali ndi mphamvu yopatsa mphoto munthu ndiponso ali ndi mphamvu yolanga. Alinso ndi mphamvu yopatsa moyo munthu ndiponso ali ndi mphamvu yolanda. Akatiyanja, zinthu zimakhala bwino; koma akapanda kutiyanja, zimaipa. Ndiye chifukwa chake m’pofunika kuti iye avomereze kulambira kwathu.

Anthufe timalambira mosiyanasiyana. Titati zipembedzo zili ngati njira, kodi Mulungu amayanja njira za chipembedzo zonsezo? Ayi, saziyanja. Yesu mneneri wa Mulungu ananena kuti pali njira ziŵiri zokha basi. Anati: “Njira yakumuka nayo kukuwonongeka ili yotakata; ndipo ali ambiri amene aloŵa pa [iyo]. Pakuti chipata chili chopapatiza, ndi ichepetsa njirayo yakumuka nayo kumoyo, ndimo akuchipeza chimenecho ali oŵerengeka.”—Mateyu 7:13, 14.

Pali zipembedzo ziŵiri zokha basi: china chimapita kumoyo, chinacho kuchiwonongeko. Bukuli lakonzedwa kuti likuthandizeni kupeza njira ya ku moyo wosatha.