1, 2. Ndi fanizo lotani limene likusonyeza kuti pafunika muyezo pogamula nkhani za chipembedzo?

KODI tingatani kuti tim’dziŵe Mulungu? Kodi tifunika kufufuza zonse zimene zipembedzo zambiri zimaphunzitsa? Zimenezo sizingatheke. Ngakhale tikanatha kuchita zimenezi, kodi tikanadziŵa bwanji kuti zimene akuphunzitsazo zili zolondola?

2 Ndithudi, popeza anthu onse amasemphana maganizo pankhani ya Mulungu, tifunika njira imene ingatithandize kudziŵa zoona, inde, muyezo umene anthu angavomereze. Taonani fanizo ili: Tinene kuti anthu akukangana pamsika za kutalika kwa nsalu. Wogulitsa akuti nsaluyo ndi fili mita, wogula akuti siikukwana. Kodi atani kuti mkanganowo uthe? Apime nsaluyo.

3. N’chifukwa chiyani analemba Baibulo?

3 Nanga bwanji pankhani za chipembedzo? Kodi pali chopimira, kapena muyezo umene ungatithandize kugamula? Inde, ulipo. Umenewo ndi Baibulo. Mulungu anakonza kuti Baibulo lilembedwe kuti anthu kulikonse akadziŵe zoona ponena za iye. Mabaibulo mamiliyonimamiliyoni asindikizidwa. Alitembenuza lonse kapena mbali zake m’zinenero zoposa 2,100. Pafupifupi aliyense atha kuŵerenga zoona ponena za Mulungu m’Baibulo la chinenero chake.

4. Kodi m’Baibulo muli zotani?

4 Baibulo ndi mphatso yamtengo wapatali yochokera kwa Mulungu. Limafotokoza zinthu  zimene chipanda ilo, sitikanazidziŵa. Limafotokoza amene amakhala kumalo a mizimu. Limavumbula maganizo a Mulungu, mtima wake, ndi zolinga zake. Limanena zimene anachita ndi anthu pazaka zikwi zambiri. Limanenanso zimene zichitike m’tsogolomu. Ndipo limatisonyeza mmene tingapezere njira ya ku moyo wosatha.

Zifukwa Zimene Mungakhulupirire Baibulo

5. Ndi chitsanzo chiti chimene chikusonyeza kuti Baibulo limagwirizana ndi sayansi?

5 Zilipo zifukwa zambiri zimene tingakhulupirire kuti Baibulo ndi Mawu a Mulungu mosapeneka. Chifukwa chimodzi n’chakuti limagwirizana ndi sayansi. Kalekale, anthu padziko lonse anali kukhulupirira kuti pali chimene chimachirikiza dziko lapansi. Mwachitsanzo, Kumadzulo kwa Africa anthu ankakhulupirira kuti njoka yodzizerenga ka 3,500 pamwamba pa dziko lapansi ndi ka 3,500 pansi pake inali kuchirikiza dzikoli. Koma polemba Baibulo zaka zoposa 3,500, wina analemba zogwirizana ndi sayansi kuti Mulungu “alenjeka dziko pachabe.”​—Yobu 26:7.

6. Kodi umboni woposa maumboni onse wakuti Baibulo linachokera kwa Mulungu ndi uti?

6 Umboni woposa maumboni onse wakuti Baibulo linachokeradi kwa Mulungu ndiwo kulosera kwake za m’tsogolo mosaphonyetsa. Kusiyana ndi alauli aumunthu, Mulungu ndiye amadziŵadi za m’tsogolo; zonse zimene wanena zimachitika.

7. Kodi maulosi ena m’Baibulo amene anakwaniritsidwa kalelo ndi ati?

7 Maulosi a m’Baibulo mazana ambiri anakwaniritsidwa kalelo. Mwachitsanzo, zaka 700 Yesu asanabadwe, Baibulo linanena molondola kuti adzabadwira m’mudzi wa Betelehemu ndipo zinachitikadi. (Mika 5:2; Mateyu 2:3-9) Kuwonjezera pa maulosi ena ambiri okhudza Yesu, Baibulo linaloseranso kuti adzabadwa kwa namwali ndipo adzaperekedwa ndi ndalama 30 za siliva. Maulosi ameneŵanso anachitika. Kunena zoona, kulibe munthu amene akanalosera zinthu ngati zimenezi!​—Yesaya 7:14; Zekariya 11:12, 13; Mateyu 1:22, 23; 27:3-5.

8. Kodi maulosi ena m’Baibulo amene akukwaniritsidwa masiku ano ndi ati, ndipo akutsimikiza chiyani?

8 Maulosi ambiri m’Baibulo akukwaniritsidwa  nthaŵi yathu ino. Nawa ochepa chabe:

  • “Mtundu wa anthu udzaukira pa mtundu wina [m’nkhondo], ndipo ufumu pa ufumu wina: ndipo kudzakhala zivomezi zazikulu, ndi njala ndi miliri m’malo akutiakuti.”​—Luka 21:10, 11.

  • ‘Kusaweruzika kudzachuluka.’​—Mateyu 24:12.

  • “Masiku otsiriza . . . anthu adzakhala odzikonda okha, okonda ndalama, . . . osamvera akuwabala, . . . osakhoza kudziletsa, aukali, osakonda abwino, . . . otukumuka mtima, okonda zokondweretsa munthu, osati okonda Mulungu.”​—2 Timoteo 3:1-5.

Kodi simukuvomereza kuti zimenezi zikuchitika masiku ano? Maulosi a m’Baibulo ali oona ndi olondola ndipo zimenezi zikungosonyeza kuti Baibulo si buku ŵamba koma kuti ndi Mawu a Mulungu amene iye anawauzira!​—2 Timoteo 3:16.

Kodi Baibulo Alisintha?

9, 10. N’chiyani chikusonyeza kuti Mulungu sanawalole anthu kusintha Baibulo?

9 Tinene kuti muli ndi fakitale yanuyanu ndipo mwakhoma malamulo pabolodi kuti antchito anu aziwatsatira. Ndiye mdani wanu wasintha zimene munalembazo. Mudzatani? Kodi simudzakonza zimene wasintha zija? Mulungunso salola anthu kusintha choonadi cha m’Baibulo, Mawu ake.

10 Anthu amene ayesa kusintha zimene Mawu a Mulungu amaphunzitsa alephera. Tikayerekeza Baibulo limene tili naloli ndi makope ake akalekale, zimafanana. Zimenezi zikungosonyeza kuti Baibulo sanalisinthe pa zaka zonse zimene lakhalapo.