1. Kodi chipembedzo cha makolo chili ngati phiri m’njira yotani?

ZIMENE amakhulupirira m’zipembedzo za makolo mu Africa muno aziyerekeza ndi phiri. Mulungu, amene mphamvu zake zauzimu n’zazikulu, ali pamwamba pake penipeni. M’mbali mwakemu muli milungu yaing’ono, kapena mizimu imene imatumikira Mulungu. Makolo amene amakumbukira achibale awo omwe anawasiya padziko lapansi ndi kuwafunira zabwino alinso m’gulu lomweli. Zinthu zina zamizimu zochepa mphamvu monga matsenga, ula, ndi ufiti, zili m’tsinde mwenimweni mwa phiri.

2. Kodi mawu ena a mu Africa muno amasonyeza bwanji kuti zikhulupiriro za makolo n’zamphamvu m’zipembedzo zina?

2 Zikhulupiriro za makolo zimenezi zili ndi mphamvu yaikulu m’zipembedzo zina mu Africa muno. Pali mawu ena mu Africa muno akuti: “Kupembedza kwathu (kaya Chikristu kapena Chisilamu) sikutiletsa kulambira milungu ya makolo athu.”

3. Ngati tikufuna kudziŵa zoona zake za amene ali kudziko la mizimu, tingazipeze kuti?

3 Kodi zimene amakhulupirira m’zipembedzo za makolo mu Africa muno n’zoona? Baibulo limatiuza zoona zake za amene ali kudziko la mizimu.

Yehova, Mulungu Woona

4. Kodi zipembedzo zazikulu mu Africa muno zimagwirizana pankhani iti?

4 M’zipembedzo zazikulu zonse zitatu zimene zili mu Africa muno amakhulupirira kuti Mulungu aliko ndipo ndi wamkulu. Baibulo limafotokoza kuti iye “ndiye Mulungu wa milungu, ndi Mbuye wa ambuye; Mulungu wamkulu, wamphamvu, ndi woopsa.” (Deuteronomo 10:17) Asilamu amakhulupiriranso kuti Mulungu ndi mmodzi ndipo ndi wamkulu. Ponena za zipembedzo za makolo mu Africa muno, Pulofesa Geoffrey Parrinder akunena kuti: “Anthu ambiri mu Africa amakhulupirira Mulungu wamkulu, atate wa milungu ndi anthu, mlengi wa chilengedwe chonse.”

5. Kodi mayina ena amene amagwiritsa ntchito potchula Mulungu ndi ati?

5 Ngakhale kuti anthu ambiri amakhulupirira Mulungu, iwo sam’dziŵa bwinobwino kuti iye ndani. Tikafuna kudziŵa munthu wina, timayamba ndi dzina lake. Komano nkhani ya dzina la Mulungu m’zipembedzo ndi yosokoneza kwambiri. M’Matchalitchi Achikristu ambiri amangoti dzina lake ndi Mulungu. Ameneŵa ndi mawu aulemu otanthauza “Wamphamvu.” Asilamu amati Allah. A zipembedzo za makolo amagwiritsa ntchito mayina osiyanasiyana potchula Wamkulukuluyo malinga ndi zinenero zawo. M’buku lake lakuti Concepts of God in Africa, John S. Mbiti analembamo mayina enieni achifirika osiyanasiyana a Mulungu ndi mayina ake ena aulemu oposa 500. Mwachitsanzo, m’Chiyoruba (chinenero cha ku Nigeria) amati Mulungu ndi Olodumare; Akikuyu (ku Kenya) amati ndi  Ngai; ndipo Azulu (ku South Africa) amati ndi Unkulunkulu.

6, 7. Kodi dzina la Mulungu ndani, ndipo tikudziŵa bwanji?

6 Nanga Mulungu mwini amati chiyani pa dzina lake? Mulungu atauza Mose kutsogolera Aisrayeli kutuluka m’Aigupto, Mose anam’funsa kuti: “Pakufika ine kwa ana a Israyeli, ndi kunena nawo, Mulungu wa makolo anu wandituma kwa inu; ndipo akakanena ndi ine, Dzina lake ndani? Ndikanena nawo chiyani?”​—Eksodo 3:13.

7 Mulungu anam’yankha nati: “Ukatero ndi ana a Israyeli, Yehova, Mulungu wa makolo anu . . . anandituma kwa inu; ili ndi dzina langa nthaŵi yosatha, ichi ndi chikumbukiro changa m’mibadwomibadwo.” (Eksodo 3:15) Dzina la Mulungu limeneli limapezeka koposa 7,000 m’Baibulo ngakhale kuti ena olimasulira alichotsamo ndi kuikamo mawu aulemu monga “Mulungu” kapena “Ambuye.”

8. Kodi Yehova ndi wotani, ndipo tifunika kuchita chiyani kuti atiyanje?

8 Kodi Yehova ndi wotani kwenikweni? Iye ndi mzimu, ndi wamphamvuyonse, ndi waulemerero. Ali wamkulukulu, wosayerekezeka. Safanana ndi wina aliyense. (Deuteronomo 6:4; Yesaya 44:6) Yehova anauza Mose kuti: “Ine Yehova Mulungu wako ndili Mulungu wansanje.” Kunena kwina, tifunika kulambira Yehova yekhayo ngati tikufuna kuti atiyanje. Safuna kuti tizilambira wina aliyense kapena zina zilizonse.​—Eksodo 20:3-5.

Yesu Kristu, Mfumu ya Ufumu wa Mulungu

9. N’chifukwa chiyani titha kunena kuti Yesu salingana ndi Yehova?

9 Nkhani yoti Yesu ndani imasokoneza anthu ambiri lerolino. Ambiri m’Matchalitchi Achikristu amakhulupirira kuti iye ali mbali ya Utatu “Woyera.” Komatu Baibulo siliphunzitsa kuti Mulungu ali atatu mwa mmodzi. Ndipo siliphunzitsa kuti Yesu ndi wolingana ndi Yehova ayi. Yesuyo ananena kuti: “Atate ali wamkulu ndi Ine.”​—Yohane 14:28.

10. Kodi Yesu anali kuti asanadze padziko lapansi?

10 Baibulo limaphunzitsa kuti Yesu asanadzakhale padziko lapansi monga munthu, anali kumwamba monga mzimu wamphamvu. Yehova analenga mizimu ina kumwambako monganso analengera Adamu ndi Hava padziko lapansi pano. Pa mizimu yonse imene Yehova analenga, Yesu anali woyamba kulengedwa.​—Yohane 17:5; Akolose 1:15.

11. Kodi zinatheka bwanji kuti Yesu abadwe ngati munthu?

11 Zaka ngati 2,000 zapitazo, Yehova anasamutsa moyo wa mzimu ameneyu kuuloŵetsa m’mimba mwa namwali dzina lake Mariya. Mngelo Gabrieli anauza mkaziyu kuti: “Udzakhala ndi pakati, nudzabala mwana wamwamuna, nudzamutcha dzina lake Yesu. Ndipo Iye adzachita ufumu, . . . ndipo ufumu wake sudzatha.”​—Luka 1:31, 33. *

12. Kodi chifukwa choyamba chimene Yesu anadzera padziko lapansi n’chiyani?

12 Choncho, Yesu anabadwa, kukula, ndi kuphunzitsa anthu za chifuniro cha Yehova ndi zolinga zake. Polankhula kwa bwanamkubwa wachiroma, iye anati: “Ndinabadwira ichi Ine, ndipo ndinadzera ichi kudza ku dziko lapansi, kuti ndikachite umboni ndi choonadi.” (Yohane 18:37) Mwa kusinkhasinkha zimene Yesu anaphunzitsa, tingadziŵe zoona za chifuniro cha Mulungu ndi zolinga zake. Tingadziŵe zochita kuti Mulungu atiyanje.

13. Kodi chachiŵiri chimene Yesu anadzera padziko lapansi n’chiyani?

13 Chachiŵiri chimene Yesu anadzera padziko lapansi chinali chakuti apereke moyo wake waumunthu dipo m’malo mwa anthu. (Mateyu 20:28) Anachita zimenezi kuti ife timasuke ku uchimo umene tinalandira kwa  kholo lathu Adamu. Izi zidzatheketsanso kuti ife tikhale ndi moyo wosatha. Mtumwi Yohane analemba kuti: “Mulungu anakonda dziko lapansi kotero, kuti anapatsa Mwana wake wobadwa yekha, kuti yense wakukhulupirira Iye asatayike, koma akhale nawo moyo wosatha.”​—Yohane 3:16.

14. (a) Chinam’chitikira Yesu n’chiyani atamwalira monga munthu? (b) Kodi Yesu panopo ali ndi udindo wanji kumwamba?

14 Atamwalira monga munthu, Yesu anaukitsidwa kupita kumwamba kumene anayambiranso moyo wake monga mzimu wamphamvu. (Machitidwe 2:32, 33) Patapita nthaŵi, Yehova anam’patsa iye “ulamuliro, ndi ulemerero, ndi ufumu, kuti anthu onse, ndi mitundu yonse ya anthu, ndi a manenedwe onse, am’tumikire.” (Danieli 7:13, 14) Iye wapanga Yesu kukhala Mfumu yamphamvu; ndiye Mfumu ya boma la kumwamba la Yehova. Posachedwapa adzaonetsa mphamvu yake padziko lonse lapansi.

Angelo, Atumiki a Mulungu

15. Kodi angelo anawalenga liti ndipo analengedwa kuti?

15 Yehova ndi Yesu si okhawo amene ali kudziko la mizimu. Yehova analenga mizimu ina, angelo. Mmodzi mwa iwo ndi Gabrieli, mngelo uja amene analankhula ndi Mariya. Kuti iwo akhale ndi moyo monga angelo, sanayambe monga anthu padziko lapansi. M’malo mwake anachita kuwalenga kumwamba zaka zambirimbiri asanalenge anthu padziko lapansi. (Yobu 38:4-7) Angelo amenewo alipo mamiliyonimamiliyoni.​—Danieli 7:10.

Angelo okhulupirika safuna kuti anthu aziwalambira

16. N’chifukwa chiyani anthu sayenera kulambira angelo?

16 Angelo okhulupirika safuna kuti ife tiziwalambira. Pamene mtumwi Yohane anayesa kuwalambira, iwo anam’dzudzula kaŵiri konse kuti: “Tapenya, usatero; . . . lambira Mulungu.”​—Chivumbulutso 19:10; 22:8, 9.

17. N’chiyani chikusonyeza kuti angelo atha kuteteza atumiki a Mulungu, nanga n’chifukwa chiyani zimenezi zili zolimbikitsa?

17 Anthu a Mulungu padziko lapansi satha kuonanso angelo ngati mmene zinalili pamene angelo anatulutsa atumwi a Yesu m’ndende. (Machitidwe 5:18, 19) Ngakhale zili choncho, ngati tilambira Yehova mogwirizana ndi Baibulo Mawu ake, ndiye kuti makamu a angelo ake amphamvu komanso osaonekawo adzatiteteza mosalephera. Baibulo limati: “Mngelo wa Yehova azinga kuwachinjiriza iwo akuopa Iye, nawalanditsa iwo.” (Salmo 34:7; 91:11) Tsono n’chifukwa chiyani zimenezi zikutilimbikitsa? Chifukwa chakuti kudziko la mizimu kulinso adani athu amene akufuna kutiwononga!

Satana, Mdani wa Mulungu

18. (a) N’chifukwa chiyani mngelo wina anapandukira Mulungu? (b) Kodi mngelo wopandukayu anam’patsa mayina otani?

18 Si angelo onse amene anakhala okhulupirika kwa Mulungu. Ena anam’pandukira. Anadziyesa okha adani a Mulungu ndi adani a anthu padziko lapansi. Nanga zinatani  kuti zimenezi zichitike? Angelo onse amene Yehova analenga anali olungama ndi abwino. Koma wina mwa ana auzimu angwiro ameneŵa anafuna kuti anthu azim’lambira ndipo anatsata zolinga zake zoipa zimenezo. Mzimu ameneyo anapatsidwa dzina lakuti Satana, kutanthauza “Wotsutsa [Mulungu].” Amatchedwanso Mdyerekezi, kutanthauza “Woneneza,” chifukwa chakuti mwanjiru amaneneza Yehova zabodza.

19. N’chifukwa chiyani Satana anazunza Yobu ndipo anam’zunza motani?

19 Satana amasonkhezera anthu kuti agwirizane naye kupandukira Mulungu. Taganizani zimene anachita kwa Yobu, mtumiki wokhulupirika wa Mulungu. Yobu anali munthu wolemera kwambiri. Anali ndi nkhosa 7,000, ngamila 3,000, ng’ombe 1,000, ndi abulu aakazi 500. Analinso ndi ana khumi ndi antchito ambiri. Poyamba, Satana anapha zoŵeta za Yobu ndi antchito ake. Kenako, anautsa “mphepo yaikulu” imene inagwetsa nyumba ndi kupha ana ake onse. Zitatero, Satana anazunza Yobu ndi “zilonda zoŵaŵa, kuyambira kuphazi lake kufikira pakati pa mutu pake.”​—Yobu 1:3-19; 2:7.

20. (a) Kodi Yobu analandira mphoto yotani chifukwa cha kukhulupirika kwake? (b) Ngakhale kuti Yobu anakhulupirika kwa Mulungu, kodi Satana watani kwa anthu ambiri?

20 Ngakhale kuti Yobu anayesedwa koopsa, anakhulupirikabe kwa Mulungu. Choncho Yehova anam’chiritsa “nachulukitsa zake zonse za Yobu mpaka kuziŵirikiza.” (Yobu 42:10) Satana analephera kuswa chikhulupiriro cha Yobu, koma wakhoza kupandutsa anthu ambiri kuwachotsa kwa Mulungu. Baibulo limati: “Dziko lonse lapansi ligona mwa woipayo.”​—1 Yohane 5:19.

21. (a) Kodi Satana anaonetsa bwanji kuti amafuna kum’lambira? (b) Nanga n’chifukwa chiyani Yesu anakana kulambira Satana?

21 Satana amafuna kuti tizim’lambira. Zimenezi zinaonekeratu pamene anayesa Yesu zaka ngati 2,000 zapitazo. Baibulo limati: “Mdyerekezi anamuka naye [Yesu] kuphiri lalitali, namuonetsa mayiko onse a dziko lapansi, ndi ulemerero wawo; nati kwa iye, Zonse ndikupatsani Inu, ngati mudzagwa pansi ndi kundigwadira ine.” Yesu anakana, ndipo anati: “Choka Satana, pakuti kwalembedwa, Ambuye Mulungu wako udzam’gwadira, ndipo iye yekhayekha udzam’lambira.” (Mateyu 4:8-10) Yesu anali kulidziŵa bwino lamulo la Yehova, ndipo sanachite zimene Satana anafuna.

Ziŵanda, Mizimu Yoipa

22. Kodi ziŵanda zachita zotani kwa anthu?

22 Ena mwa angelo anagwirizana ndi Satana napandukira Mulungu. Angelo ameneŵa, ziŵanda, ndi adani a anthu padziko lapansi. Ndi ankhanza komanso olusa. Kale, anachititsa anthu ena kusalankhula ndiponso khungu. (Mateyu 9:32, 33; 12:22) Anadwalitsanso ena kapena kuwachititsa misala. (Mateyu 17:15, 18; Marko 5:2-5) Anazunza ndi ana omwe.​—Luka 9:42.

23. (a) Kodi mizimu yoipa imafuna kuti anthu azitani? (b) Kodi Satana ndi ziŵanda zake anyenga anthu kuti azitani?

23 Monga Satana, mizimu yoipa imeneyi imafunanso kuilambira. M’malo moti ikane anthu akafuna kuilambira​—pozindikira kuti Yehova yekha ndiye ayenera kum’lambira​—imalakalaka kuti anthu ailambire ndipo imawalimbikitsa kutero. Mwa kugwiritsa ntchito chinyengo, mabodza, ndi kuopseza, Satana ndi ziŵanda zake akakamiza anthu kuwalambira. Kunena zoona, anthu ambiri sadziŵa kuti akulambira Satana ndi ziŵanda zake. Iwo akhoza kudabwa akadziŵa kuti chipembedzo chawo chimalemekeza Satana. Koma Baibulo limatichenjeza kuti: “Zimene amitundu apereka nsembe azipereka kwa ziŵanda [osati kwa Mulungu, NW].”​—1 Akorinto 10:20.

24. Kodi Satana amagwiritsa ntchito njira yotani kunyengera anthu?

24 Satana ndi ziŵanda zake amafalitsa zikhulupiriro zolakwika zokhudza akufa. Imeneyi ndi njira imodzi imene amanyengera nayo anthu kuti aziwalambira. Ndiye tiyeni tione zimene Baibulo limaphunzitsa pankhaniyi.

^ ndime 11 Koran imatchulanso za kubadwa kwa Yesu mozizwitsa pa Surah 19 (Mariya). Imati: ‘Tinatumiza kwa [Mariya] mzimu Wathu ngati munthu wamkulu kale. Ndipo mkaziyo atamuona anati: “Wachifundoyo anditeteze kwa inu! Ngati mumaopa Ambuye, dzipitani mundichokere.” Iyeyo anayankha nati: “Ine ndine mthenga wochokera kwa Mbuye wako ndipo ndadza kudzakupatsa mwana wamwamuna wopatulika.” “Zitheka bwanji ine kukhala ndi mwana mmene ndililimu, namwali wosakhudzidwa ndi mwamuna?” anatero mkaziyo. “Ndi zimene Ambuye akufuna,” anayankha choncho. “Zimenezo n’zapafupi kwa Iye. ‘Adzakhala chizindikiro kwa anthu,’ akutero Ambuye, ‘komanso dalitso lochokera kwa Ife. Izi n’zimene Ife talamula.’”’