Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Njira ya ku Moyo Wosatha—Kodi Mwaipeza?

Padzikoli pali zipembedzo ziwiri zokha. Chipembedzo china chothandiza anthu kuti adzapeze moyo wosatha koma china chidzachititsa anthu kuti awonongedwe. Kabukuka kangakuthandizeni kuti mupeze njira yokuthandizani kuti mudzapeze moyo wosatha.

Mawu Oyamba

Moyo wathu panopo komanso mtsogolo umadalira Mulungu Wamphamvuyonse. Choncho ndi zofunika kuti kulambira kwathu kukhale kovomerezeka kwa iye.

CHIGAWO 1

Kodi Zipembedzo Zonse Zimaphunzitsa Zoona?

Anthu azipembedzo amasiyana zikhulupiriro. Kodi zimene amakhulupirirazo zimagwirizana ndi zimene Mawu a Mulungu amaphunzitsa?

CHIGAWO 2

Kodi Mungatani Kuti Mudziŵe Zoona Ponena za Mulungu?

Kodi chipembedzo chiyenera kutsatira mfundo ziti kuti anthu adziwe kuti chimaphunzitsa zoona?

CHIGAWO 3

Ali Kudziko la Mizimu Ndani?

Zimene miyambo ya makolo imanena zokhudza dziko la mizimu zimasokoneza anthu ambiri. Koma kodi miyamboyi ndi yoona? Tingapeze mayankho a mafunsowa m’Baibulo.

CHIGAWO 4

Kodi Makolo Athu Ali Kuti?

Anthu amakhulupirira kuti munthu akafa, amakakhalabe ndi moyo kudziko la mizimu. Koma kodi Baibulo limati chiyani pa nkhaniyi?

CHIGAWO 5

Zoona Zake za Matsenga ndi Ufiti

Ziwanda ndi zamphamvu komanso zoopsa koma ndi zotheka kulimbana nazo.

CHIGAWO 6

Kodi Mulungu Amavomereza Zipembedzo Zonse?

Anthu ena amaganiza kuti Mulungu amavomereza zipembedzo zonse. Koma kodi Baibulo limaphunzitsadi zimenezi?

CHIGAWO 7

Kodi Amene Ali ndi Chipembedzo Choona Ndani?

Baibulo lingatithandize kudziwa anthu amene amachita chifuniro cha Mulungu.

CHIGAWO 8

Siyani Chipembedzo Chonyenga; Tsatani Chipembedzo Choona

Yesu ananena kuti: “Amene sali kumbali yanga ndi wotsutsana ndi ine.” Kodi tingasonyeze bwanji kuti tili kumbali ya Yesu?

CHIGAWO 9

Mutha Kupindula ndi Chipembedzo Choona Kosatha!

Mukamalambira Yehova, adzakudalitsani panopa komanso m’tsogolo.