Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

 CHIGAWO 12

Kodi Mungatani Kuti Aliyense M’banja Mwanu Azisangalala?

Kodi Mungatani Kuti Aliyense M’banja Mwanu Azisangalala?

Chikondi n’chofunika kwambiri kuti aliyense m’banja akhale wosangalala. Aefeso 5:33

Zimene Mulungu amafuna pa nkhani ya ukwati n’zakuti mwamuna akhale ndi mkazi mmodzi komanso mkazi akhale ndi mwamuna mmodzi.

Mwamuna wachikondi amakomera mtima mkazi wake ndiponso amamumvetsa.

Mkazi ayenera kuchita zinthu mogwirizana ndi mwamuna wake.

Ana ayenera kumvera makolo awo.

 Khalani okoma mtima ndiponso okhulupirika, osati ankhanza. Akolose 3:5, 8-10

Mawu a Mulungu amanena kuti mwamuna azikonda mkazi wake ngati mmene amakondera thupi lake, ndiponso kuti mkazi azilemekeza kwambiri mwamuna wake.

Kugonana ndi munthu amene si mkazi kapena mwamuna wanu n’kulakwa. Kukwatira mitala n’kulakwanso.

Mawu a Yehova ali ndi mfundo zimene zingathandize mabanja kukhala osangalala.