Pali Mulungu woona mmodzi yekha ndipo dzina lake ndi Yehova. (Salimo 83:18) Iye ndi Mzimu ndipo sitingathe kumuona. Iye amatikonda ndipo amafuna kuti ifenso tizimukonda komanso tizikonda anthu anzathu. (Mateyu 22:35-40) Iye ndi Wamkulukulu ndiponso ndi Mlengi wa zinthu zonse.

Poyambirira Mulungu analenga munthu wauzimu wamphamvu kwambiri amene kenako anadzatchedwa Yesu Khristu. Komanso Yehova analenga angelo.

Yehova analenga zinthu zonse zakumwamba . . . ndi zapadziko lapansi. Chivumbulutso 4:11

 Yehova Mulungu analenga nyenyezi, dziko lapansi ndi zonse zimene zili padzikoli.​—Genesis 1:1.

Anaumba Adamu, munthu woyamba, kuchokera kufumbi lapansi.​—Genesis 2:7.