Pitani ku nkhani yake

Pitani ku menyu yachiwiri

Pitani ku mitu ya nkhani

Mboni za Yehova

Chichewa

Mverani Mulungu Kuti Mudzapeze Moyo Wosatha

 CHIGAWO 3

Kodi Moyo Unali Wotani m’Paradaiso?

Kodi Moyo Unali Wotani m’Paradaiso?

Yehova anapatsa Adamu ndi Hava zinthu zambiri zabwino. Genesis 1:28

Yehova anapanga mkazi woyamba, Hava, ndipo anam’pereka kwa Adamu kuti akhale mkazi wake.​—Genesis 2:21, 22.

Yehova anawalenga ndi thupi ndiponso maganizo angwiro.

Iwo ankakhala m’Paradaiso m’munda wa Edeni umene unali wokongola kwambiri. M’mundawu munali mtsinje, mitengo ya zipatso ndi nyama.

Yehova ankalankhula nawo ndiponso ankawaphunzitsa. Iwo akanamvera Mulungu, akanakhala ndi moyo wosatha m’Paradaiso padziko lapansi.

 Mulungu anawauza kuti asadye zipatso za mtengo umodzi m’mundamo. Genesis 2:16, 17

Yehova anasonyeza Adamu ndi Hava mtengo umodzi wa zipatso m’mundamo ndipo anawauza kuti akadzadya zipatso za mtengo umenewo, adzafa.

Mngelo mmodzi anagalukira Mulungu. Mngelo woipa ameneyu ndi Satana Mdyerekezi.

Satana sanafune kuti Adamu ndi Hava amvere Yehova. Choncho, kudzera mwa njoka anauza Hava kuti iwo akadya chipatso cha mtengo umene Mulungu anawauza kuti asadye, sadzafa, koma adzafanana ndi Mulungu. Limenelitu linali bodza lenileni.​—Genesis 3:1-5.