Pitani ku nkhani yake

Pitani ku menyu yachiwiri

Pitani ku mitu ya nkhani

Mboni za Yehova

Chichewa

Mverani Mulungu Kuti Mudzapeze Moyo Wosatha

Mawu Oyamba

Mawu Oyamba

Mulungu ali ngati bambo amene amakonda kwambiri ana ake. 1 Petulo 5:6, 7

Mulungu ndi Mlengi wathu, ndipo amatisamalira mwachikondi. Mofanana ndi bambo wanzeru komanso wachikondi amene amalangiza ana ake, Mulungu amaphunzitsa anthu ake padziko lonse zoyenera kuchita kuti akhale ndi moyo wabwino.

Mulungu amatiphunzitsa choonadi chamtengo wapatali chimene chimatisangalatsa ndiponso kutipatsa chiyembekezo.

Mukamamvera Mulungu, adzakutsogolerani ndi kukutetezani, ndiponso adzakuthandizani kuti muthane ndi mavuto amene mukukumana nawo.

Kuwonjezera pamenepo, mudzakhala ndi moyo wosatha.

 Mulungu akutiuza kuti: “Bwerani kwa ine. Mvetserani ndipo mudzakhalabe ndi moyo.” Yesaya 55:3