Pitani ku nkhani yake

Pitani ku menyu yachiwiri

Pitani ku mitu ya nkhani

Mboni za Yehova

Chichewa

Mverani Mulungu Kuti Mudzapeze Moyo Wosatha

 CHIGAWO 6

Kodi Tikuphunzirapo Chiyani pa Zimene Zinachitika Nthawi ya Chigumula?

Kodi Tikuphunzirapo Chiyani pa Zimene Zinachitika Nthawi ya Chigumula?

Mulungu anawononga anthu oipa koma anapulumutsa Nowa ndi banja lake. Genesis 7:11, 12, 23

Mvula inagwa kwa masiku 40 usana ndi usiku ndipo madzi anadzaza dziko lonse lapansi. Anthu onse oipa anafa.

Angelo amene anagalukira Mulungu aja anavula matupi awo n’kuvalanso matupi auzimu ndipo anakhala ziwanda.

Anthu amene anali m’chingalawa aja anapulumuka. Ngakhale kuti patapita nthawi Nowa ndi anthu onse a m’banja lake anamwalira, Mulungu adzawaukitsa ndipo adzakhala ndi mwayi wokhala ndi moyo wosatha.

 Mulungu adzawononganso anthu oipa ndi kupulumutsa anthu abwino. Mateyu 24:37-39

Satana ndi ziwanda akupitiriza kusocheretsa anthu.

Monga mmene zinalili m’nthawi ya Nowa, masiku ano anthu ambiri safuna kutsatira malangizo amene Yehova akupereka mwachikondi. Posachedwapa Yehova awononga anthu onse oipa.​—2 Petulo 2:5, 6.

Anthu ena ali ngati Nowa. Iwo amamvetsera ndi kuchita zimene Mulungu akunena. Anthu amenewa ndi Mboni za Yehova.

Onaninso

UTHENGA WABWINO WOCHOKERA KWA MULUNGU

Kodi Chipembedzo Choona Mungachidziwe Bwanji?

Kodi chipembedzo choona chilipo chimodzi chokha? Taonani zinthu 5 zomwe zingakuthandizeni kudziwa chipembedzo choona.