Pitani ku nkhani yake

Pitani ku menyu yachiwiri

Pitani ku mitu ya nkhani

Mboni za Yehova

Chichewa

Mverani Mulungu Kuti Mudzapeze Moyo Wosatha

 CHIGAWO 14

Kodi Mungasonyeze Bwanji Kuti Ndinu Wokhulupirika kwa Yehova?

Kodi Mungasonyeze Bwanji Kuti Ndinu Wokhulupirika kwa Yehova?

Khalani kumbali ya Mulungu. 1 Petulo 5:6-9

Muzipewa kuchita nawo miyambo yosagwirizana ndi Baibulo. Munthu amafunika kulimba mtima kuti achite zimenezi.

Musamachite nawo ndale zadzikoli chifukwa sizigwirizana ndi zofuna za Yehova ndi Ufumu wake.

 Sankhani mwanzeru, mverani Mulungu. Mateyu 7:24, 25

Muzipita kumisonkhano ya Mboni za Yehova ndipo iwo adzakuthandizani kuti muyandikire Mulungu.

Pitirizani kuphunzira za Mulungu ndipo muziyesetsa kumvera malamulo ake.

Chikhulupiriro chanu chikalimba, muyenera kupereka moyo wanu kwa Yehova ndi kubatizidwa.—Mateyu 28:19.

Muzimvera Mulungu. Muziwerenga Baibulo, ndipo pemphani aliyense wa Mboni za Yehova kuti akuthandizeni kulimvetsa. Kenako, muzigwiritsa ntchito zimene mwaphunzirazo. Mukamachita zimenezi mudzapeza moyo wosatha.—Salimo 37:29.

Onaninso

UTHENGA WABWINO WOCHOKERA KWA MULUNGU

Kodi Pali Uthenga Wabwino Wotani Wokhudza Zipembedzo?

Kodi idzafika nthawi imene anthu onse adzagwirizana n’kumalambira Mulungu woona yekha?