Mavuto amene akuchitika padzikoli akusonyeza kuti posachedwapa, Ufumu wa Mulungu uyamba kulamulira padziko lapansi. Luka 21:10, 11; 2 Timoteyo 3:1-5

Baibulo linaneneratu zinthu zambiri zimene zikuchitika masiku ano. Linaneneratu kuti anthu adzakhala okonda ndalama, osamvera makolo, oopsa ndiponso okonda zosangalatsa.

Linanenanso kuti kudzakhala zivomezi zamphamvu, nkhondo, njala ndiponso miliri. Zinthu zimenezi zikuchitika masiku ano.

Yesu ananenanso kuti uthenga wabwino wonena za Ufumu udzalalikidwa padziko lonse lapansi.​—Mateyu 24:14.

 Ufumu umenewu udzachotsa zinthu zonse zoipa. 2 Petulo 3:13

Posachedwapa, Yehova awononga anthu oipa.

Satana ndi ziwanda zake adzalangidwa.

Anthu amene amamvera Mulungu adzapulumuka n’kulowa m’dziko latsopano lolungama. M’dziko limeneli anthu adzakhala mopanda mantha ndipo azidzakhulupirirana ndi kukondana kwambiri.