Mulungu amamva mapemphero athu. 1 Petulo 3:12

Yehova ndi “Wakumva pemphero.” (Salimo 65:2) Iye amafuna kuti tizimuuza zakukhosi kwathu.

Muzipemphera kwa Yehova yekha osati kwa wina aliyense.

 Pali zinthu zambiri zimene tingatchule popemphera. 1 Yohane 5:14

Muzipemphera kuti chifuniro cha Mulungu chichitike kumwamba komanso padziko lapansi pano.

Muzipemphera m’dzina la Yesu, kuti musonyeze kuti mumayamikira zimene iye anakuchitirani.

Pemphani Yehova kuti akuthandizeni kuchita zinthu zabwino. Mungapemphe zinthu monga chakudya, ntchito, nyumba, zovala ndiponso thanzi labwino.