Pitani ku nkhani yake

Pitani ku menyu yachiwiri

Pitani ku mitu ya nkhani

Mboni za Yehova

Chichewa

Mverani Mulungu Kuti Mudzapeze Moyo Wosatha

 CHIGAWO 4

Kodi Chinachitika N’chiyani Adamu ndi Hava Atamvera Satana?

Kodi Chinachitika N’chiyani Adamu ndi Hava Atamvera Satana?

Adamu ndi Hava sanamvere Mulungu, choncho anafa. Genesis 3:6, 23

Hava anamvera njoka ndipo anadya chipatso cha mtengo woletsedwawo. Atatero, anatengako chipatso china n’kukapatsa mwamuna wake Adamu, ndipo iyenso anadya.

Zimene anachitazo zinali zolakwika chifukwa linali tchimo. Zitatero Mulungu anawathamangitsa m’Paradaiso mmene iwo ankakhala.

Iwo pamodzi ndi ana awo anayamba kukhala moyo wovutika kwambiri. Kenako, iwo anakalamba n’kufa. Iwo atafa, sanapite kudziko lamizimu ayi, chifukwa mwa munthu mulibe chilichonse chimene chimapitiriza kukhala ndi moyo munthuyo akamwalira.

 Munthu akafa amangokhala ngati fumbi. Genesis 3:19

Tonsefe timafa chifukwa ndife ana a Adamu ndi Hava. Anthu akufa sangathe kuchita chilichonse monga kumva kapena kuona.​—Mlaliki 9:5, 10

Sichinali cholinga cha Yehova kuti anthu azifa. Choncho, posachedwapa iye adzaukitsa anthu onse amene anamwalira. Anthu amenewo akadzamvera Mulungu, adzakhala ndi moyo wosatha.

Onaninso

UTHENGA WABWINO WOCHOKERA KWA MULUNGU

Kodi Mulungu Ali ndi Cholinga Chotani Chokhudza Dziko Lapansili?

Baibulo limafotokoza chifukwa chake Mulungu analenga dzikoli, nthawi imene mavuto adzathe, mmene zinthu zidzakhalire padzikoli komanso anthu amene adzakhale m’dziko la paradaiso.

UTHENGA WABWINO WOCHOKERA KWA MULUNGU

Kodi Pali Chiyembekezo Chotani Chokhudza Anthu Amene Anamwalira?

Kodi chimachitika n’chiyani munthu akamwalira? Kodi abale athu amene anamwalira tidzawaonanso?