“Munthu woyenda ndi anthu anzeru adzakhala wanzeru.”​—MIYAMBO 13:20.

1-3. (a) Kodi tikuphunzira chiyani palemba la Miyambo 13:20? (b) N’chifukwa chiyani tiyenera kusamala posankha anthu oti akhale anzathu?

KODI munaona zimene mwana amachita ngakhale asanayambe kulankhula? Amamvetsera komanso amayang’anitsitsa zimene makolo ake akuchita. Ndiyeno akamakula, amayamba kutsanzira makolo akewo pa chilichonse. Ndiyetu n’zosadabwitsa kuti ngakhalenso anthu akuluakulu amayamba kutengera zochita za anthu amene amakhala nawo nthawi zambiri.

2 Lemba la Miyambo 13:20 limati: “Munthu woyenda ndi anthu anzeru adzakhala wanzeru.” Palembali mawu akuti ‘kuyenda ndi,’ akunena za anthu amene timacheza nawo kwambiri kapenanso amene timakonda kuchita nawo zinthu limodzi. Mawuwa sakungonena za anthu amene tili nawo limodzi pamalo enaake koma aliyense akuchita zake. Katswiri wina wa Baibulo ananena kuti kuyenda ndi munthu kungatanthauzenso kukonda munthu komanso kumuona kuti ndi mnzako wapamtima. Anthufe timayamba kutengera zochita za anthu amene nthawi zambiri timakhala tili nawo limodzi, makamakanso ngati timawakonda kwambiri.

3 Anzathu angatichititse kuti tizichita zabwino kapena  zoipa. Lemba la Miyambo 13:20 lija limapitiriza kuti: “Wochita zinthu ndi anthu opusa adzapeza mavuto.” Mawu achiheberi amene anawamasulira kuti ‘kuchita zinthu ndi,’ angatanthauze “kugwirizana” ndi munthu kapena kukhala mnzake. (Miyambo 22:24; Oweruza 14:20) Anthu amene amakonda Mulungu angatithandize kuti tikhalebe okhulupirika. Koma kodi Yehova amasankha anthu otani kuti akhale anzake? Yankho la funsoli litithandiza kuti nafenso tizisamala tikafuna kusankha anthu oti akhale anzathu.

KODI MABWENZI A YEHOVA AMAKHALA OTANI?

4. (a) N’chifukwa chiyani tingati ndi mwayi waukulu kukhala bwenzi la Mulungu? (b) N’chifukwa chiyani Yehova anatchula Abulahamu kuti “bwenzi langa”?

4 Yehova, yemwe ndi Wolamulira Wamkulu wa chilengedwe chonse, amalola kuti anthufe tikhale anzake. Umenewutu ndi mwayi waukulu. Komabe Yehova amasankha mosamala anthu oti akhale anzake. Amasankha anthu okhawo amene amamukonda ndiponso amamukhulupirira. Taganizirani za Abulahamu. Iye ankachita chilichonse chimene Mulungu wamuuza. Nthawi zonse ankasonyeza kuti ndi wokhulupirika komanso womvera. Mulungu atamuuza kuti apereke nsembe mwana wake Isaki, iye sanakane chifukwa ankakhulupirira kuti “Mulungu ali ndi mphamvu zomuukitsa.” (Aheberi 11:17-19; Genesis 22:1, 2, 9-13) Abulahamu anali wokhulupirika komanso womvera ndipo Yehova anamutchula kuti, “bwenzi langa.”​—Yesaya 41:8; Yakobo 2:21-23.

5. Kodi Yehova amawaona bwanji anthu okhulupirika?

5 Yehova amaona kuti mabwenzi ake ndi amtengo wapatali. Mabwenzi a Yehova amaona kuti kukhala wokhulupirika kwa iye n’kofunika kwambiri kuposa chilichonse.  (Werengani 2 Samueli 22:26.) Anthuwa amakhala okhulupirika komanso omvera chifukwa choti amakonda Yehova. Baibulo limati Mulungu “amakonda anthu owongoka mtima,” amene amamumvera. (Miyambo 3:32) Yehova amaitana mabwenzi ake kuti akhale alendo “m’chihema” chake. Iye amawalola kuti azimulambira komanso azipemphera kwa iye nthawi iliyonse imene angafune.​—Salimo 15:1-5.

6. Kodi tingasonyeze bwanji kuti timakonda Yesu?

6 Yesu anati: ‘Ngati munthu amandikonda, adzasunga mawu anga ndipo Atate wanga adzamukonda.’ (Yohane 14:23) Choncho kuti tikhale mabwenzi a Yehova tiyeneranso kukonda Yesu komanso kuchita zimene iye anatiuza. Mwachitsanzo, tiyenera kumvera lamulo lake loti tizilalikira uthenga wabwino komanso tiziphunzitsa anthu kuti akhale ophunzira ake. (Mateyu 28:19, 20; Yohane 14:15, 21) Popeza timakonda Yesu, timatsatira “mapazi ake mosamala kwambiri.” (1 Petulo 2:21) Yehova amasangalala akaona kuti tikuyesetsa kutsanzira Mwana wake pa zonse zimene timalankhula komanso kuchita.

7. N’chifukwa chiyani anzathu ayenera kukhala anthu omwe ndi mabwenzi a Yehova?

7 Taona kuti mabwenzi a Yehova amakhala okhulupirika, omvera komanso amakonda Yesu. Kodi inunso anthu amene mumasankha kuti akhale anzanu amachita zimenezi? Ngati anzanu amatsanzira Yesu ndipo amakonda kuphunzitsa ena za Ufumu wa Mulungu, angakuthandizeni kuti muzichita zabwino. Angakuthandizeninso kuti mukhalebe okhulupirika kwa Yehova.

ZITSANZO ZA M’BAIBULO

8. Kodi n’chiyani chikukuchititsani chidwi ndi ubwenzi wa Naomi ndi Rute?

8 M’Baibulo muli zitsanzo zambiri za anthu amene  ankagwirizana kwambiri. Mwachitsanzo, timawerenga za Rute ndi apongozi ake, dzina lawo a Naomi. Anthu amenewa anali osiyana mayiko, chipembedzo ndiponso chikhalidwe. Komanso Naomi anali wamkulu kwambiri poyerekeza ndi Rute. Koma azimayi amenewa ankagwirizana kwambiri chifukwa onse ankakonda Yehova. Pamene Naomi ankachoka ku Mowabu kubwerera kwawo ku Isiraeli, ‘Rute anaumirira’ kuti apita nawo. Anauza apongozi akewo kuti: “Anthu a mtundu wanu adzakhala anthu a mtundu wanga, ndipo Mulungu wanu adzakhala Mulungu wanga.” (Rute 1:14, 16) Rute ankawakonda kwambiri apongozi akewa moti atafika ku Isiraeli ankagwira ntchito mwakhama kuti aziwasamalira. Naomi nayenso ankamukonda kwambiri Rute ndipo anamupatsa malangizo abwino. Rute anatsatira malangizowo ndipo zotsatira zake zinali zakuti iye ndi apongozi akewo anadalitsidwa.​—Rute 3:6.

9. N’chiyani chikukuchititsani chidwi ndi ubwenzi wa Davide ndi Yonatani?

9 Chitsanzo china ndi cha Davide ndi Yonatani. Nawonso ankagwirizana kwambiri ndipo onse anali okhulupirika kwa Yehova. Koma Yonatani anali wamkulu poyerekeza ndi Davide moti ankasiyana zaka 30. Komanso Yonatani anali wa m’banja lachifumu, moti iye ndi amene ankayenera kudzalowa ufumu wa bambo ake. (1 Samueli 17:33; 31:2; 2 Samueli 5:4) Komabe atamva kuti Yehova anasankha Davide kuti ndiye adzakhale mfumu ya Isiraeli, sanachite nsanje kapena kuyamba mtima wampikisano. M’malomwake, anachita chilichonse chimene akanatha kuti athandize Davide. Mwachitsanzo, pamene moyo wa Davide unali pangozi, Yonatani anapita kumene Davideyo anathawira ndipo ‘anamulimbikitsa kudalira Yehova.’ Iye anaika moyo wake pachiswe pofuna kuthandiza  Davide. (1 Samueli 23:16, 17) Nayenso Davide anali wokhulupirika kwa mnzakeyu. Mwachitsanzo, analonjeza kuti adzasamalira anthu a m’banja la Yonatani. Davide anakwaniritsa lonjezo lakeli ngakhale kuti Yonatani anali atamwalira.​—1 Samueli 18:1; 20:15-17, 30-34; 2 Samueli 9:1-7.

10. Pa nkhani ya mabwenzi, kodi tikuphunzira chiyani pa chitsanzo cha anyamata atatu achiheberi?

10 Sadirake, Mesake ndi Abedinego anali Aheberi ndipo anatengedwa kwawo ali anyamata n’kupita nawo ku ukapolo. Kumeneko anyamatawa ankathandizana kuti akhalebe okhulupirika kwa Yehova. Atakula, chikhulupiriro chawo chinayesedwa pamene Mfumu Nebukadinezara inawalamula kuti alambire fano lagolide. Koma anakana ndipo anauza mfumuyo kuti: “Ife sititumikira milungu yanu, ndipo sitilambira fano limene mwaimika.” Sadirake, Mesake ndi Abedinego ankagwirizana kwambiri ndipo atayesedwa anakhalabe okhulupirika kwa Mulungu.​—Danieli 1:1-17; 3:12, 16-28.

11. Kodi tikudziwa bwanji kuti Paulo ndi Timoteyo ankagwirizana kwambiri?

11 Mtumwi Paulo atakumana ndi Timoteyo, anamuona kuti ankakonda Yehova. Anaonanso kuti ankakonda anthu a mumpingo ndipo ankafuna kuti mpingowo uziyenda bwino. Pa nthawiyo n’kuti Timoteyo ali mnyamata. Choncho Paulo anamuphunzitsa kuti azitha kuthandiza abale ndi alongo am’madera osiyanasiyana. (Machitidwe 16:1-8; 17:10-14) Timoteyo ankagwira ntchito mwakhama moti Paulo anati: “Watumikira monga kapolo limodzi ndi ine kupititsa patsogolo uthenga wabwino.” Paulo ankadziwa kuti Timoteyo ‘angasamaledi moona mtima’ abale ndi alongo ake. Paulo ndi Timoteyo ankagwira ntchito limodzi mwakhama potumikira Yehova, ndipo izi  zinachititsa kuti azigwirizana kwambiri.​—Afilipi 2:20-22; 1 Akorinto 4:17.

KODI MUNGASANKHE BWANJI ANZANU ABWINO?

12, 13. (a) N’chifukwa chiyani tiyenera kusamala posankha anzathu, ngakhale mumpingo? (b) N’chifukwa chiyani mtumwi Paulo anapereka chenjezo la pa 1 Akorinto 15:33?

12 Timaphunzira zambiri kwa abale ndi alongo athu amumpingo, ndipo timathandizana kuti tikhalebe okhulupirika. (Werengani Aroma 1:11, 12.) Koma tiyenera kusamala tikamasankha anthu oti akhale anzathu apamtima,  ngakhale mumpingo. Mumpingo mumakhala abale ndi alongo a zikhalidwe zosiyanasiyana ndipo mbiri yawo imakhalanso yosiyana. Komanso ena ndi atsopano, pomwe ena atumikira Yehova kwa zaka zambiri. Monga zilili kuti pamatenga nthawi kuti chipatso chipse, pamatenganso nthawi kuti ubwenzi wathu ndi Yehova ulimbe. Choncho tiyenera kukhala oleza mtima pochita zinthu ndi abale ndi alongo athu. Tiyeneranso kusankha anzathu mwanzeru.​—Aroma 14:1; 15:1; Aheberi 5:12–6:3.

13 Nthawi zina mumpingo mungakhale vuto lina lalikulu, ndipo zikatere tiyenera kusamala kwambiri. Mwina m’bale kapena mlongo wina angakhale kuti akuchita zinazake zolakwika. Apo ayi, munthu wina angayambe mtima wodandaula zilizonse, umene ungasokoneze mpingo. Zimenezi siziyenera kutidabwitsa chifukwa ngakhalenso mu nthawi ya atumwi nthawi zina mumpingo munkakhala mavuto. Ndipotu mtumwi Paulo anachenjeza Akhristu kuti: “Musasocheretsedwe. Kugwirizana ndi anthu oipa kumawononga makhalidwe abwino.” (1 Akorinto 15:12, 33) Paulo anachenjezanso Timoteyo kuti azisamala posankha anzake. Nafenso tiyenera kuchita chimodzimodzi.​—Werengani 2 Timoteyo 2:20-22.

14. Kodi chingachitike n’chiyani ngati sitinasankhe bwino anthu ocheza nawo?

14 Tiyenera kuteteza ubwenzi wathu ndi Yehova chifukwa ndi wofunika kwambiri kuposa chilichonse. Kuti zimenezi zitheke, tizipewa kugwirizana ndi aliyense amene angachititse kuti chikhulupiriro chathu chifooke kapena ubwenzi wathu ndi Yehova usokonekere. Tikaika thonje m’madzi akuda, sitingayembekezere kuti litulukamo loyera. Mofanana ndi zimenezi, ngati timacheza ndi anthu a makhalidwe oipa, zingakhale zovuta kuti ifeyo tizichita  zabwino. Choncho tiyenera kusamala posankha anzathu.​—1 Akorinto 5:6; 2 Atesalonika 3:6, 7, 14.

N’zotheka kupeza anzanu abwino amene amakonda Yehova

15. Kodi mungatani kuti mupeze anzanu abwino mumpingo?

15 Mumpingo muli anthu ambiri amene amakondadi Yehova. Anthu amenewa akhoza kukhala anzanu apamtima. (Salimo 133:1) Anzanu asamakhale a msinkhu wanu okha kapena amene ali ndi mbiri yofanana ndi yanu basi. Kumbukirani kuti Yonatani anali wamkulu poyerekeza ndi Davide, komanso Rute anali wamng’ono poyerekeza ndi Naomi. Muzitsatira malangizo a m’Baibulo akuti: “Futukulani mtima wanu.” (2 Akorinto 6:13; werengani 1 Petulo 2:17.) Ndipotu mukamatsanzira kwambiri Yehova, anthu ambiri azifuna kuti mukhale mnzawo.

PAKAKHALA MAVUTO

16, 17. Ngati munthu wina wamumpingo watikhumudwitsa, kodi sitiyenera kuchita chiyani?

16 M’banja lililonse mumakhala anthu osiyana makhalidwe, maganizo komanso mmene amaonera zinthu. N’chimodzimodzinso mumpingo. Zimenezi zili ndi ubwino wake, ndipo tingaphunzire zambiri kwa ena. Koma nthawi zina kusiyana kumeneku kungachititse kuti pakhale kusamvana ndipo tingayambe kuona kuti zochita za abale kapena alongo ena zayamba kutitopetsa. Mwinanso tingakhumudwe kwambiri chifukwa cha zolankhula zawo. (Miyambo 12:18) Koma kodi ndi bwino kusiya kusonkhana kapena kuchita zinthu zina ndi mpingo chifukwa cha mavuto amenewa?

17 Ayi. Tisamasiye kusonkhana kapena kuchita zinthu zina ndi mpingo chifukwa choti wina watikhumudwitsa. Tizikumbukira kuti amene watikhumudwitsa si Yehova. Iye anatipatsa moyo ndiponso zinthu zina zambiri. Choncho tiyenera kumukonda komanso kukhala wokhulupirika.  (Chivumbulutso 4:11) Tingati mpingo wathu ndi mphatso yochokera kwa Yehova ndipo umatithandiza kuti tikhale ndi chikhulupiriro cholimba. (Aheberi 13:17) Choncho sitiyenera kukana mphatso imeneyi chifukwa choti wina watikhumudwitsa.​—Werengani Salimo 119:165.

18. (a) N’chiyani chingathandize kuti abale ndi alongo athu akhale anzathu? (b) N’chifukwa chiyani tiyenera kukhululukira ena?

18 Timakonda kwambiri abale ndi alongo athu ndipo timafuna kuti akhale anzathu. Yehova sayembekezera kuti mabwenzi ake akhale angwiro. Ifenso tisamaganize kuti abale ndi alongo athu ayenera kukhala angwiro kuti akhale anzathu. (Miyambo 17:9; 1 Petulo 4:8) Tonse timalakwitsa zinthu zina. Koma chikondi chingatithandize kuti tipitirize “kukhululukirana ndi mtima wonse.” (Akolose 3:13) Chikondi chingachititsenso kuti tisamakulitse nkhani yaing’ono mpaka kukhala vuto lalikulu. N’zoona kuti wina akatikhumudwitsa, zimavuta kuti tisiye kuganizira nkhaniyo. Ndipotu n’zosavuta kukwiya kapenanso kumusungira zifukwa. Komabe zimenezi zingangochititsa kuti tisamasangalale. Koma tikakhululukira munthu amene watilakwira, timakhala ndi mtendere wamumtima komanso mumpingo mumakhala mgwirizano. Chofunika kwambiri n’chakuti timakhala pa ubwenzi wolimba ndi Yehova.​—Mateyu 6:14, 15; Luka 17:3, 4; Aroma 14:19.

MUNTHU WINA AKACHOTSEDWA

19. N’chiyani chingachititse kuti tisiye kuchita zinthu ndi munthu wina wamumpingo?

19 M’banja lachikondi, aliyense amachita mbali yake kuti onse azisangalala. Koma nthawi zina wina angayambe kuchita zinthu zosonyeza kuti sakufunanso kugwirizana ndi ena. Aliyense angayese kumuthandiza koma n’kupezeka kuti sakutheka. Mwina angasankhe kuchoka  pakhomo kapena bambo wa m’nyumbamo angamuuze kuti achoke. Zoterezi zingachitikenso mumpingo. Munthu wina angayambe kuchita zinthu zokwiyitsa Yehova komanso zosokoneza mpingo. Angakane kusintha ndipo angasonyeze kuti sakufunanso kukhala mumpingomo. Mwina angasankhe kuchoka mumpingo, apo ayi angachotsedwe. Zikatere, Baibulo limati tiyenera ‘kuleka kuyanjana’ naye. (Werengani 1 Akorinto 5:11-13; 2 Yohane 9-11) Zimakhala zopweteka kwambiri ngati munthuyo ndi mnzathu kapena m’bale wathu. Koma zoterezi zikachitika, tiyenera kukhala okhulupirika kwa Yehova osati kwa munthuyo.​—Onani Mawu Akumapeto 8.

20, 21. (a) N’chifukwa chiyani tinganene kuti kuchotsa anthu osalapa n’kuwakonda? (b) N’chifukwa chiyani tiyenera kusamala posankha anthu oti akhale anzathu?

20 Mfundo yoti anthu osalapa azichotsedwa imasonyeza kuti Yehova amatikonda. Imathandiza kuti anthu amene satsatira mfundo za Yehova asakhale mumpingo n’kumasokoneza zinthu. (1 Akorinto 5:7; Aheberi 12:15, 16) Tikamatsatira malangizo okhudza anthu ochotsedwa timasonyeza kuti timakonda Yehova, dzina lake komanso mfundo zake za makhalidwe abwino. (1 Petulo 1:15, 16) Komanso kuchotsa munthu osalapa, ndi kumukonda. Tikutero chifukwa zimenezi zingachititse kuti munthuyo azindikire kulakwa kwake, n’kusintha. Ambiri amene anachotsedwapo, anabwerera ndipo anthu a mumpingo anawalandira ndi manja awiri.​—Aheberi 12:11.

21 Taona kuti anthu amene timacheza nawo angachititse kuti tizichita zabwino kapena zoipa. Choncho tiyenera kusamala tikamasankha anthu oti akhale anzathu. Tingachite bwino kusankha anthu amene Yehova amawakonda. Anthu amenewa angatithandize kuti tikhale okhulupirika kwa Yehova mpaka kalekale.