‘Munthu aliyense asangalale chifukwa choti wagwira ntchito mwakhama.’​—MLALIKI 3:13.

1-3. (a) Kodi anthu ambiri amamva bwanji akaganizira ntchito imene amagwira? (b) Kodi tikambirana mafunso ati?

ANTHU padziko lonse amagwira ntchito mwakhama kuti azidzisamalira komanso kuti azisamalira mabanja awo. Komabe ambiri sakonda ntchito yawo ndipo ena tsiku lililonse amapita kuntchito monyinyirika. Ngati nanunso zimenezi zimakuchitikirani, kodi mungatani kuti muzisangalala ndi ntchito yanu?

2 Yehova amatiuza kuti: “Munthu aliyense adye ndi kumwa ndi kusangalala ndi zinthu zabwino, chifukwa choti wagwira ntchito mwakhama. Imeneyi ndi mphatso yochokera kwa Mulungu.” (Mlaliki 3:13) Yehova anatipatsa mtima wofuna kugwira ntchito. Zimenezi zikusonyeza kuti amafuna kuti tizisangalala ndi ntchito imene timagwira.​—Werengani Mlaliki 2:24; 5:18.

3 Ndiye kodi n’chiyani chingatithandize kuti tizisangalala ndi ntchito yathu? Nanga ndi ntchito ziti zimene Akhristu sayenera kugwira? Kodi tingatani kuti ntchito yathu isamatilepheretse kulambira Yehova? Nanga ntchito yofunika kwambiri imene tiyenera kugwira ndi iti?

YEHOVA NDI YESU AMAGWIRA NTCHITO MWAKHAMA

4, 5. Kodi Yehova amaona bwanji ntchito?

4 Yehova amakonda kugwira ntchito. Lemba la Genesis  1:1 limati: “Pa chiyambi, Mulungu analenga kumwamba ndi dziko lapansi.” Mulungu atamaliza kulenga dziko komanso zinthu zonse zapadziko ananena kuti zimene analengazo zinali “zabwino kwambiri.” (Genesis 1:31) Izi zikusonyeza kuti Mlengi wathu anasangalala ndi zimene analenga.​—1 Timoteyo 1:11.

5 Yehova sanasiye kugwira ntchito. Yesu anati: “Atate wanga akugwirabe ntchito mpaka pano.” (Yohane 5:17) Ngakhale kuti sitidziwa zinthu zonse zodabwitsa zimene Yehova wachita, pali zina zimene timadziwa. Mwachitsanzo, iye wasankha anthu amene adzalamulire limodzi ndi Mwana wake Yesu Khristu mu Ufumu wa kumwamba. (2 Akorinto 5:17) Yehova amagwiranso ntchito mwakhama posamalira anthu ake komanso kuwatsogolera pa ntchito yolalikira. Ntchitoyi yachititsa kuti anthu mamiliyoni ambiri adziwe Yehova komanso akhale ndi chiyembekezo chodzakhala kwamuyaya m’Paradaiso.​—Yohane 6:44; Aroma 6:23.

6, 7. Kodi Yesu ankagwira bwanji ntchito yake?

6 Nayenso Yesu amakonda kugwira ntchito. Asanabwere padzikoli anali “mmisiri waluso” wa Mulungu ndipo analenga nawo zinthu zonse zakumwamba ndi zapadziko lapansi. (Miyambo 8:22-31; Akolose 1:15-17) Pamene anali padzikoli, anapitiriza kugwira ntchito mwakhama. Ali mnyamata, anaphunzira ntchito ya ukalipentala ndipo ayenera kuti ankadziwanso kumanga nyumba. Yesu ankagwira mwaluso ntchito yakeyi moti ankadziwika kuti anali “mmisiri wamatabwa.”​—Maliko 6:3.

7 Koma ntchito yofunika kwambiri kwa Yesu inali yolalikira ndi kuphunzitsa anthu za Yehova. Iye ankafunika kumaliza ntchito yake pa zaka zitatu ndi hafu ndipo ankagwira ntchitoyi kuyambira m’mawa mpaka usiku. (Luka 21:37, 38; Yohane 3:2) Yesu ankayenda maulendo  ataliatali m’misewu yafumbi ndipo ankayesetsa kuti alalikire uthenga wabwino kwa anthu ambiri.​—Luka 8:1.

8, 9. N’chiyani chinachititsa kuti Yesu azisangalala ndi ntchito yake?

8 Kwa Yesu, kugwira ntchito imene Mulungu anamupatsa kunali ngati chakudya chifukwa inkamupatsa mphamvu. Masiku ena Yesu ankagwira ntchito mwakhama kwambiri moti sankapeza nthawi yoti adye. (Yohane 4:31-38) Iye ankagwiritsa ntchito mpata uliwonse kuthandiza anthu kuti adziwe za Atate wake. N’chifukwa chake anauza Yehova kuti: “Ndakulemekezani padziko lapansi, popeza ndatsiriza kugwira ntchito imene munandipatsa.”​—Yohane 17:4.

9 Zonsezi zikusonyeza kuti Yehova ndi Yesu amalimbikira ntchito ndipo amasangalala ndi ntchito yawo. Timafunitsitsa kuti ‘tizitsanzira Mulungu’ komanso ‘tizitsatira mapazi a [Yesu] mosamala kwambiri.’ (Aefeso 5:1; 1 Petulo 2:21) N’chifukwa chake timayesetsa kugwira ntchito mwakhama.

KODI NTCHITO YANU MUYENERA KUIONA BWANJI?

10, 11. N’chiyani chingatithandize kuti tikhale ndi maganizo oyenera okhudza ntchito yathu?

10 Atumiki a Yehovafe timagwira ntchito mwakhama kuti tizidzisamalira komanso tizisamalira mabanja athu. Timafuna kuti tizisangalala ndi ntchito yathu, komabe nthawi zina zimakhala zovuta. Ndiye kodi mungatani ngati simusangalala ndi ntchito imene mumagwira?

Ngati titakhala ndi maganizo oyenera, tingathe kumasangalala ndi ntchito iliyonse imene timagwira

11 Muzikhala ndi maganizo oyenera. Mwina simungathe kusintha ntchito imene mumagwira komanso kumene mumagwirira ntchitoyo. Komabe mungathe kusintha n’kuyamba kukhala ndi maganizo oyenera okhudza ntchito yanuyo. Kuganizira zimene Yehova amafuna kuti  tizichita kungatithandize. Mwachitsanzo, Yehova amafuna kuti mwamuna azichita zonse zimene angathe posamalira banja lake. Ndipotu Baibulo limati aliyense amene amalephera kusamalira banja lake ndi “woipa kuposa munthu wosakhulupirira.” (1 Timoteyo 5:8) Ngati ndinu mutu wa banja muyenera kuti mumagwira ntchito mwakhama kuti muzisamalira banja lanu. Kaya ntchito yanuyo mumaikonda kapena ayi, muyenera kudziwa kuti mukamasamalira banja lanu ndiye kuti mukusangalatsa Yehova.

12. Kodi kugwira ntchito molimbika komanso kuchita zinthu mwachilungamo kumatithandiza bwanji?

12 Muzigwira ntchito molimbika komanso muzichita zinthu mwachilungamo. Zimenezi zingakuthandizeni kuti muzisangalala ndi ntchito yanu. (Miyambo 12:24; 22:29) Zingapangitsenso kuti okulembani ntchitoyo azikukhulupirirani. Anthu amafuna kulemba ntchito anthu okhulupirika chifukwa sangawabere ndalama, katundu kapenanso nthawi. (Aefeso 4:28) Komanso chofunika kwambiri n’chakuti mukamagwira ntchito molimbika ndiponso kuyesetsa kuchita zinthu mwachilungamo, Yehova amaona. Mumakhalanso ndi “chikumbumtima choona” chifukwa choti mukudziwa kuti mukusangalatsa Mulungu amene mumamukonda.​—Aheberi 13:18; Akolose 3:22-24.

13. N’chiyani chingachitike tikamachita zinthu mwachilungamo?

13 Muzikumbukira kuti khalidwe lanu labwino limachititsa kuti anthu azilemekeza Yehova. Chimenechi ndi chifukwa chinanso chomwe chimatithandiza kuti tizisangalala ndi ntchito yathu. (Tito 2:9, 10) Khalidwe lanu labwino likhoza kupangitsa munthu wina yemwe mumagwira naye ntchito kufuna kuphunzira Baibulo.​—Werengani Miyambo 27:11; 1 Petulo 2:12.

 KODI NDINGASANKHE BWANJI NTCHITO YABWINO?

14-16. Kodi tiyenera kuganizira mfundo ziti tikamasankha ntchito?

14 M’Baibulo mulibe mndandanda wa ntchito zomwe Mkhristu ayenera kugwira kapena zimene sayenera kugwira. Komabe muli mfundo zomwe zingatithandize kusankha ntchito yabwino. (Miyambo 2:6) Poganizira mfundo za m’Baibulo, tiyenera kudzifunsa mafunso otsatirawa:

Muyenera kupeza ntchito imene sitsutsana ndi mfundo za Yehova

15 Kodi ntchitoyi izichititsa kuti ndizipanga zinthu zimene Yehova amati ndi zoipa? M’bukuli taphunzira makhalidwe amene Yehova amadana nawo, monga kunama  komanso kuba. (Ekisodo 20:4; Machitidwe 15:29; Aefeso 4:28; Chivumbulutso 21:8) Choncho timayesetsa kupewa ntchito iliyonse imene imatsutsana ndi mfundo za Yehova.​—Werengani 1 Yohane 5:3.

16 Kodi ntchitoyi imalimbikitsa khalidwe lomwe Yehova amadana nalo? Mwachitsanzo, kodi mungatani ngati patapezeka ntchito yolandira alendo kuchipatala chochotsa mimba? Ntchito yolandira alendo si yolakwika. Komabe mukudziwa maganizo a Yehova pa nkhani yochotsa mimba. Choncho ngakhale kuti inuyo simuzigwira ntchito yochotsa mimba, kodi Yehova sangaone kuti mukuthandiza nawo kuchotsa mimbako?​—Ekisodo 21:22-24.

17. N’chiyani chingatithandize kuti tizisankha zinthu zomwe zingakondweretse Mulungu?

17 Mfundo za m’Baibulo zingatithandize kuti tikhale ngati anthu amene atchulidwa palemba la Aheberi 5:14 “amene pogwiritsa ntchito mphamvu zawo za kuzindikira, aphunzitsa mphamvuzo kusiyanitsa choyenera ndi chosayenera.” Dzifunseni kuti: ‘Kodi anthu ena angakhumudwe ataona kuti ndayamba ntchito imeneyi? Kodi ntchitoyi ichititsa kuti ndisiye banja langa n’kupita kudziko lina? Nanga zimenezi zingakhudze bwanji banja langa?’

“MUZITSIMIKIZIRA KUTI ZINTHU ZOFUNIKA KWAMBIRI NDI ZITI”

18. N’chifukwa chiyani nthawi zina zimakhala zovuta kuti tiziika zinthu zokhudza kulambira pamalo oyamba?

18 ‘M’masiku otsiriza komanso ovuta’ ano, nthawi zina zimakhala zovuta kuti tiziika zinthu zokhudza kulambira pamalo oyamba. (2 Timoteyo 3:1) Zingakhale zovuta kwambiri kupeza ntchito komanso kukhalabe pa ntchitoyo. Timayenera kusamalira banja lathu koma timadziwa kuti zinthu zokhudza kulambira ziyenera kukhala pamalo oyamba.  Sitiyenera kulola kuti ndalama kapena chuma zikhale zinthu zofunika kwambiri pa moyo wathu. (1 Timoteyo 6:9, 10) Ndiye kodi tingatani kuti ‘tizitsimikizira kuti zinthu zofunika kwambiri ndi ziti,’ koma n’kumasamaliranso banja lathu?​—Afilipi 1:10.

19. Kodi kukhulupirira Yehova kumatithandiza bwanji kuti tisamangokhalira kugwira ntchito?

19 Muzidalira kwambiri Yehova. (Werengani Miyambo 3:5, 6.) Tikudziwa kuti Mulungu amadziwa zomwe timafunikira ndipo amatidera nkhawa. (Salimo 37:25; 1 Petulo 5:7) Mawu ake amatiuza kuti: “Moyo wanu ukhale wosakonda ndalama, koma mukhale okhutira ndi zimene muli nazo pa nthawiyo. Pakuti Mulungu anati: ‘Sindidzakusiyani kapena kukutayani ngakhale pang’ono.’” (Aheberi 13:5) Yehova safuna kuti tizingokhalira kuda nkhawa kuti tisamalira bwanji banja lathu. Iye wakhala akusonyeza kuti angathe kusamalira atumiki ake. (Mateyu 6:25-32) Kaya zinthu zili bwanji, timayesetsa kuti tizipeza nthawi yophunzira Mawu a Mulungu, kulalikira uthenga wabwino komanso kupezeka pamisonkhano.​—Mateyu 24:14; Aheberi 10:24, 25.

20. Kodi tingatani kuti tizikhala moyo wosalira zambiri?

20 Tizikhala ndi diso lolunjika pa chinthu chimodzi. (Werengani Mateyu 6:22, 23.) Izi zikutanthauza kuti tiziyesetsa kukhala moyo wosalira zambiri kuti maganizo athu azikhala pa kutumikira Yehova. Tikudziwa kuti kungakhale kupusa kulola kuti zinthu monga ndalama, moyo wofewa kapena zipangizo zamakono zikhale zofunika kwambiri kwa ife kuposa ubwenzi wathu ndi Yehova. Ndiye kodi tingatani kuti zinthu zofunika kwambiri zizikhala pamalo oyamba? Tiziyesetsa kuti tisamakhale ndi ngongole. Ngati muli nazo kale, yesetsani kuti zichepe kapenanso zithe. Titapanda kusamala, tingamawononge nthawi ndi mphamvu pa zinthu zosafunika kwambiri  n’kumalephera kupeza nthawi yopemphera, kuphunzira Baibulo ndiponso kulalikira. M’malo motanganidwa ndi kusaka chuma, tiyenera kumakhutira ndi zinthu zimene tili nazo monga ‘chakudya ndi zovala.’ (1 Timoteyo 6:8) Kaya zinthu zili bwanji pa moyo wathu, ndi bwino kuti nthawi ndi nthawi tiziganizira zimene tingachite kuti tizipeza nthawi yambiri yotumikira Yehova.

21. N’chifukwa chiyani tiyenera kusankha zinthu zoyenera kukhala pamalo oyamba pa moyo wathu?

21 Zinthu zofunika kwambiri zizikhala pamalo oyamba. Tiyenera kugwiritsa ntchito mwanzeru nthawi yathu,  mphamvu zathu komanso chuma chathu. Titapanda kusamala, tingamawononge nthawi yambiri pa zinthu zosafunika kwenikweni, monga maphunziro kapena kusaka ndalama. Yesu anati: “Pitirizani kufunafuna ufumu choyamba.” (Mateyu 6:33) Zinthu zimene timachita tsiku lililonse, zolinga zathu komanso zimene timasankha ndiponso kukonda, zimasonyeza zinthu zimene timaona kuti n’zofunika kwambiri pa moyo wathu.

NTCHITO YOFUNIKA KWAMBIRI YOMWE TIYENERA KUGWIRA

22, 23. (a) Kodi ntchito yofunika kwambiri imene Akhristu ayenera kugwira ndi iti? (b) Kodi n’chiyani chingatithandize kuti tizisangalala ndi ntchito yathu?

22 Ntchito yofunika kwambiri imene tiyenera kugwira ndi kutumikira Yehova komanso kulalikira uthenga wabwino. (Mateyu 24:14; 28:19, 20) Mofanana ndi Yesu, timafunitsitsa kuti tizichita zonse zimene tingathe pogwira ntchitoyi. Ena asamukira kumadera kumene kukufunika olalikira Ufumu ambiri. Enanso aphunzira chilankhulo china n’cholinga choti azilalikira anthu a chilankhulocho. Mungalankhule ndi anthu ngati amenewa n’kuwafunsa zimene anachita kuti akwanitse zimenezi. Anthu amenewa angakuuzeni kuti panopa akusangalala kwambiri.​—Werengani Miyambo 10:22.

Ntchito yofunika kwambiri imene tiyenera kugwira ndi kutumikira Yehova

23 Masiku ano ambirife timafunika kugwira ntchito maola ambiri kapenanso kugwira ntchito zingapo kuti tizitha kusamalira banja lathu. Yehova amadziwa zimenezi ndipo amayamikira chilichonse chimene timachita posamalira banja lathu. Kaya timagwira ntchito yanji, tiyeni tonse tizitsanzira Yehova ndi Yesu pogwira ntchito molimbika. Koma tizikumbukira kuti ntchito yofunika kwambiri ndi kutumikira Yehova komanso kulalikira uthenga wa Ufumu wa Mulungu. Tikamachita zimenezi timakhala osangalala.