“Pakuti inu ndinu kasupe wa moyo.”​—SALIMO 36:9.

1, 2. (a) Kodi Yehova anatipatsa mphatso yamtengo wapatali iti? (b) Kodi Yehova anatipatsa chiyani kuti tizitha kusankha bwino zochita?

YEHOVA anapatsa munthu aliyense mphatso yamtengo wapatali kwambiri. Mphatso imeneyi ndi moyo. (Genesis 1:27) Iye amafuna kuti tizisangalala kwambiri ndi moyo. Choncho anatipatsa mfundo za m’Mawu ake zomwe zingatithandize kuti tizisankha bwino zochita. Tiyenera kugwiritsa ntchito mfundo zimenezi kuti tizitha “kusiyanitsa choyenera ndi chosayenera.” (Aheberi 5:14) Tikamachita zimenezi, timasonyeza kuti tikufuna kuti Yehova azitiphunzitsa kuganiza bwino. Tikaona kuti mfundo za m’Baibulo zikutithandiza pa moyo wathu, timayamba kuona kuti mfundozi ndi zabwino kwambiri.

2 Koma masiku ano moyo ndi wovuta. Nthawi zina tingakumane ndi vuto lina ndipo tingapeze kuti m’Baibulo mulibe lamulo lenileni lofotokoza zoyenera kuchita. Mwachitsanzo, tingafunike kusankha pa nkhani yokhudza kuikidwa magazi. Kodi tingatani kuti tisankhe zinthu zimene zingasangalatse Yehova? M’Baibulo muli mfundo zimene zingatithandize kudziwa maganizo a Yehova pa nkhani ya moyo komanso magazi. Ngati titamvetsa bwino mfundo zimenezi, tingathe kusankha zoyenera ndipo  sitingawononge chikumbumtima chathu. (Miyambo 2:6-11) Tsopano tiyeni tikambirane zina mwa mfundo zimenezi.

KODI YEHOVA AMAONA BWANJI MOYO KOMANSO MAGAZI?

3, 4. (a) Kodi tikudziwa bwanji kuti Yehova amaona kuti magazi ndi opatulika? (b) Kodi magazi amaimira chiyani?

3 Baibulo limaphunzitsa kuti magazi ndi opatulika chifukwa amaimira moyo. Ndipotu Yehova amaona kuti moyo ndi wamtengo wapatali. Mwachitsanzo, Kaini atapha m’bale wake, Yehova anamuuza kuti: “Magazi a m’bale wako akundilirira munthaka.” (Genesis 4:10) Magazi a Abele ankaimira moyo wake. Choncho pamene Yehova ananena za magazi a Abele, ankatanthauza moyo wa Abeleyo.

4 Chigumula cha Nowa chitatha, Mulungu anauza anthu kuti angathe kumadya nyama. Koma anawauza mosapita m’mbali kuti: “Musadye nyama pamodzi ndi magazi ake, amene ndiwo moyo wake.” (Genesis 9:4) Lamulo limeneli linali lopita kwa ana onse a Nowa, kuphatikizapo ifeyo. Yehova amaona kuti magazi amaimira moyo. Ifenso tiyenera kuwaona choncho.​—Salimo 36:9.

5, 6. Kodi Chilamulo cha Mose chinasonyeza bwanji kuti Yehova amaona kuti magazi ndi opatulika?

5 M’Chilamulo cha Mose munali lamulo lakuti: “Munthu aliyense . . . akadya magazi alionse, ndidzam’kana ndipo ndidzamupha kuti asakhalenso pakati pa anthu amtundu wake. Pakuti moyo wa nyama uli m’magazi.”​—Levitiko 17:10, 11.

6 M’Chilamulochi munalinso lamulo lakuti munthu akamapha nyama yoti adye, azionetsetsa kuti wathira magazi a nyamayo pansi. Akatero zinali ngati akupereka moyo wa nyamayo kuti ubwererenso kwa Yehova, yemwe ndi Mlengi. (Deuteronomo 12:16; Ezekieli 18:4) Koma sikuti  Yehova ankayembekezera kuti Aisiraeliwo azichotsa magazi onse a nyamayo, osatsala ngakhale dontho. Ankangofunika kuchita zonse zimene akanatha poonetsetsa kuti achotsa magazi. Akatero ankadya nyamayo popanda kudziimba mlandu. Aisiraeli akamapewa kudya magazi a nyama, ankasonyeza kuti amalemekeza Yehova, yemwe ndi Mlengi wa zamoyo zonse. M’Chilamulo munalinso lamulo lakuti Aisiraeli azipereka nsembe za nyama kuti machimo awo akhululukidwe.​—Onani Mawu Akumapeto 19 ndi 20.

7. Kodi Davide anasonyeza bwanji kuti ankaona kuti magazi ndi opatulika?

7 Tingathenso kuona kuti magazi ndi opatulika tikaona zimene Davide anachita pamene ankamenyana ndi Afilisiti. Anthu amene anali ndi Davide ataona kuti iye ali ndi ludzu, anaika moyo wawo pachiswe popita kudera la adani awo kukamutungira madzi. Koma atabweretsa madziwo, Davide anakana kumwa ndipo “anawapereka kwa Yehova mwa kuwathira pansi.” Iye anati: “Sindingachite zimenezo inu Yehova! Kodi ndimwe magazi a amuna amene anaika miyoyo yawo pangozi kuti akatunge madziwa?” Davide ankadziwa kuti Mulungu amaona kuti moyo komanso magazi ndi zinthu zopatulika.​—2 Samueli 23:15-17.

8, 9. Kodi Akhristu amawaona bwanji magazi?

8 Akhristu oyambirira sankafunika kuti azipereka nsembe za nyama. Koma ankayenerabe kuona kuti magazi ndi opatulika. Panali malamulo ochepa amene Yehova ankafuna kuti Akhristu azitsatira, ndipo limodzi mwa malamulo amenewa linali lakuti apitirize “kupewa . . . magazi.” Kupewa magazi kunali kofunika kwambiri mofanana ndi kupewa dama komanso kulambira mafano.​—Machitidwe 15:28, 29.

Kodi ndingafotokoze bwanji zimene ndasankha zokhudza tizigawo ta magazi?

9 N’chimodzimodzinso masiku ano. Akhristufe timadziwa kuti Yehova ndi kasupe wa moyo, ndipo moyo wa  chinthu chilichonse ndi wake. Timadziwanso kuti magazi ndi opatulika ndipo amaimira moyo. Choncho timaganizira mfundo za m’Baibulo tikauzidwa kuti thandizo lachipatala limene akufuna kutipatsa limaphatikizapo kuika magazi.

KODI NDI BWINO KUIKIDWA MAGAZI?

10, 11. (a) Kodi a Mboni za Yehova amaiona bwanji nkhani ya kuikidwa magazi kapena zigawo 4 zikuluzikulu za magazi? (b) Kodi ndi pa nkhani ziti pamene Mkhristu aliyense amafunika kusankha yekha?

10 A Mboni za Yehova amadziwa kuti lamulo lakuti ‘tizipewa magazi’ silitanthauza kuti tizingopewa kudya ndi kumwa magazi basi. Lamuloli limatanthauzanso kuti sitiyenera kuikidwa magazi a munthu wina, sitiyenera kupereka magazi komanso sitiyenera kuikidwa magazi athu omwe amene anachotsedwa m’thupi mwathu n’kuwasunga penapake. Zikutanthauzanso kuti sitiyenera kuikidwa zigawo zikuluzikulu 4 za magazi, zomwe ndi maselo ofiira, maselo oyera, maselo othandiza magazi kuundana komanso madzi a m’magazi.

11 Nthawi zina zigawo zimenezi zimagawidwanso m’tizigawo tina ting’onoting’ono. Mkhristu aliyense amafunika kusankha yekha ngati angalandire tizigawo timeneti kapena ayi. Mkhristu aliyense ayeneranso kusankha yekha ngati angalandire njira zogwiritsa ntchito magazi ake omwe. Komanso ayenera kusankha yekha mmene magazi ake angagwiritsidwire ntchito pa nthawi ya opaleshoni, pomuyeza matenda kapena pomupatsa chithandizo chilichonse.​—Onani Mawu Akumapeto 21.

12. (a) N’chifukwa chiyani tinganene kuti Yehova amaona kuti zimene timasankha tokha mogwirizana ndi chikumbumtima chathu ndi zofunika? (b) Kodi tingatani kuti tisankhe zoyenera pa nkhani ya thandizo la mankhwala?

12 Kodi Yehova amaona kuti zimene timasankha tokha mogwirizana ndi chikumbumtima chathu ndi zofunika?  Inde. Yehova amachita chidwi ndi zimene timaganiza komanso zolinga zathu. (Werengani Miyambo 17:3; 24:12.) Choncho tisanasankhe thandizo la mankhwala, tiyenera kupemphera kaye kuti Yehova atitsogolere kenako n’kufufuza kuti tidziwe zambiri za thandizolo. Tikatero tizisankha mogwirizana ndi chikumbumtima chathu chophunzitsidwa Baibulo. Tisamafunse ena zimene akanachita vutolo likakhala kuti lagwera iwowo, n’cholinga choti ifenso tichite zomwezo. Komanso anthu ena sayenera kutisankhira zochita. Mkhristu aliyense “ayenera kunyamula katundu wake.”​—Agalatiya 6:5; Aroma 14:12.

MALAMULO A YEHOVA AMASONYEZA KUTI AMATIKONDA

13. Kodi malamulo a Yehova ndiponso mfundo za m’Mawu ake zokhudza magazi zimasonyeza chiyani?

13 Zonse zimene Yehova amatiuza kuti tizichita, ndi zothandiza ndipo zimasonyeza kuti amatikonda. (Salimo 19:7-11) Koma sikuti timamvera Yehova chifukwa choti malamulo ake ndi othandiza basi. Timamumvera chifukwa choti timamukonda. Choncho timakana kuikidwa magazi chifukwa choti timakonda Yehova. (Machitidwe 15:20) Kusaikidwa magazi kumathandizanso kuti tikhale ndi moyo wathanzi. Masiku ano anthu ambiri amadziwa mavuto amene angakhalepo chifukwa choikidwa magazi. Komanso madokotala ambiri amaona kuti opaleshoni yopanda magazi ndi yabwino kwambiri kwa wodwala. Apatu n’zoonekeratu kuti malamulo a Yehova ndi othandiza komanso amasonyeza kuti iye amatikonda.​—Werengani Yesaya 55:9; Yohane 14:21, 23.

14, 15. (a) Kodi Yehova anapatsa anthu ake malamulo ati? (b) Kodi mungatani posonyeza kuti mumatsatira mfundo za m’malamulo amenewa?

14 Kuyambira kale, Yehova amapatsa anthu ake malamulo  othandiza. Mwachitsanzo, Aisiraeli akale anawapatsa malamulo amene ankawathandiza kupewa ngozi. Limodzi mwa malamulo amenewa linali lakuti munthu aliyense azimanga kampanda kuzungulira denga la nyumba yake kuti munthu asagwe kuchokera padengapo. (Deuteronomo 22:8) Panalinso lamulo lokhudza ziweto. Munthu akakhala ndi ng’ombe yolusa, ankafunika kuisamalira kuti isagunde kapena kupha munthu. (Ekisodo 21:28, 29) Aliyense wosamvera lamuloli, ankakhala ndi mlandu ng’ombe yakeyo ikapha munthu.

15 Malamulo amenewa akusonyeza kuti Yehova amaona kuti moyo ndi wamtengo wapatali. Ifenso tiyenera kumauona chimodzimodzi. Mwachitsanzo, tiyenera kusamalira bwino nyumba komanso galimoto yathu, tiyenera kuyendetsa bwino galimoto komanso tiyenera kupewa masewera oika moyo pangozi. Anthu ena, makamaka achinyamata, amaganiza kuti palibe chimene chingawachitikire. Choncho amachita zinthu zimene zimaika moyo wawo pachiswe. Koma Yehova safuna kuti tizichita zimenezi. Amafuna tiziona kuti moyo wathu komanso wa anthu ena ndi wofunika kwambiri.​—Mlaliki 11:9, 10.

16. Kodi Yehova amagwirizana ndi zoti anthu azichotsa mimba?

16 Yehova amaona kuti moyo wa munthu aliyense ndi wofunika kwambiri. N’chimodzimodzinso moyo wa mwana wosabadwa. M’Chilamulo cha Mose munali lamulo lakuti munthu akavulaza mwangozi mayi woyembekezera, mayiyo kapena mwanayo n’kumwalira, munthuyo aziimbidwa mlandu wopha munthu. Ngakhale kuti sichinali cholinga chake kuti aphe munthu, wopalamulayo ankayenera kuphedwa polipira moyo wa wophedwayo. (Werengani Ekisodo 21:22, 23.) Izi zikusonyeza kuti Mulungu amaona kuti nayenso mwana wosabadwa ndi munthu.  Ndiye kodi mukuganiza kuti iye amagwirizana ndi zoti anthu azichotsa mimba? Nanga mukuganiza kuti amamva bwanji akamaona ana osabadwa mamiliyoni ambirimbiri akuphedwa chaka chilichonse chifukwa cha kuchotsa mimba?

17. Kodi ndi mfundo iti imene ingalimbikitse mayi amene anachotsa mimba asanaphunzire za Yehova?

17 Nanga bwanji ngati mayi anachotsa mimba asanaphunzire zoti Yehova amadana ndi kuchotsa mimba? Ayenera kudziwa kuti Yehova angathe kumukhululukira pogwiritsa ntchito nsembe ya Yesu. (Luka 5:32; Aefeso 1:7) Munthu amene anachita tchimo limeneli asanaphunzire za Yehova, koma panopa analapa kuchokera pansi pa mtima, sayenera kumadziimbabe mlandu. Baibulo limati: “Yehova ndi wachifundo ndi wachisomo . . . Monga mmene kum’mawa kwatalikirana ndi kumadzulo, momwemonso, watiikira kutali zolakwa zathu.”​—Salimo 103:8-14.

MUSAMASUNGE CHIDANI MUMTIMA MWANU

18. N’chifukwa chiyani tiyenera kuyesetsa kuti tichotse maganizo achidani mumtima mwathu?

18 Nkhani yoona kuti moyo ndi wamtengo wapatali imayambira mumtima. Imakhudzanso mmene timaonera anthu ena. Mtumwi Yohane analemba kuti: “Aliyense amene amadana ndi m’bale wake ndi wopha munthu.” (1 Yohane 3:15) Nthawi zina mtima wosakonda munthu umayamba pang’onopang’ono, koma kenako umakula n’kukhala chidani. Chidani chingapangitse kuti tisamalemekeze munthu, tiziuza ena zabodza zokhudza munthuyo komanso mwina kuyamba kulakalaka munthuyo atangofa. Ngati mumtima mwathu timadana ndi munthu wina, Yehova amadziwa zimenezo. (Levitiko 19:16; Deuteronomo 19:18-21; Mateyu 5:22) Choncho ngati pali aliyense  amene timadana naye, tiyenera kuyesetsa kuti tichotse maganizo amenewo mumtima mwathu.​—Yakobo 1:14, 15; 4:1-3.

19. Kodi mfundo yoti Yehova amadana ndi chiwawa iyenera kutikhudza bwanji?

19 Pali njira inanso yomwe tingasonyezere kuti timaona kuti moyo ndi wamtengo wapatali. Lemba la Salimo 11:5 limanena kuti Yehova “amadana kwambiri ndi aliyense wokonda chiwawa.” Tikamakonda zosangalatsa zachiwawa ndiye kuti timakonda chiwawa. Ngati timadana ndi chiwawa sitingalole kuti mawu achiwawa komanso zithunzi zachiwawa zikhazikike m’maganizo mwathu. M’malomwake tiyenera kuyesetsa kuti tiziganizira zinthu zabwino komanso zamtendere.​—Werengani Afilipi 4:8, 9.

MUZIPEWA MAGULU AMENE AMASONYEZA KUTI SALEMEKEZA MOYO

20-22. (a) Kodi Yehova amawaona bwanji anthu a m’dziko la Satanali? (b) Kodi anthu a Mulungu angasonyeze bwanji kuti sali “mbali ya dzikoli”?

20 Anthu a m’dziko la Satanali salemekeza moyo. Choncho Yehova amawaona kuti ali ndi mlandu wa magazi. Maboma a m’mayiko ambiri akhala akuchititsa kuti anthu mamiliyoni ambirimbiri, kuphatikizapo atumiki a Yehova, aphedwe. M’Baibulo maboma amenewa amawayerekezera ndi zilombo zolusa. (Danieli 8:3, 4, 20-22; Chivumbulutso 13:1, 2, 7, 8) Masiku ano bizinezi yogulitsa zida za nkhondo ndi yaikulu komanso yotentha. Anthu amapanga ndalama zambiri chifukwa chogulitsa zida zoopsa zophera anthu. Zimenezi zikutsimikizira kuti “dziko lonse lili m’manja mwa woipayo.”​—1 Yohane 5:19.

21 Koma Akhristu oona sali “mbali ya dzikoli.” Iwo salowerera ndale komanso samenya nawo nkhondo. Akhristu  oona sapha anthu komanso sathandiza gulu lililonse limene limapha anthu. (Yohane 15:19; 17:16) Akhristuwa akamazunzidwa, sachita zachiwawa pofuna kubwezera. Yesu anati tizikonda anthu onse, ngakhalenso adani athu.​—Mateyu 5:44; Aroma 12:17-21.

22 Zipembedzo zapangitsa kuti anthu ambirimbiri aphedwe. Ponena za Babulo Wamkulu, kapena kuti zipembedzo zonse zonyenga, Baibulo limati: “Mwa iye munapezeka magazi a aneneri, a oyera, ndi a onse amene anaphedwa padziko lapansi.” Ndiyetu mpake kuti Yehova amatiuza kuti: “Tulukani mwa iye anthu anga.” Anthu amene amalambira Yehova sakhala mbali ya zipembedzo zonyenga.​—Chivumbulutso 17:6; 18:2, 4, 24.

23. Kodi munthu amene akufuna ‘kutulukadi’ mu Babulo Wamkulu ayenera kuchita chiyani?

23 Kuti munthu ‘atulukedi’ mu Babulo Wamkulu, ayenera kuchita zinthu zosonyeza kuti wasiya kukhala membala wa chipembedzo chonyenga. Mwachitsanzo, ayenera kufufutitsa dzina lake kutchalitchi chake chakale. Ayeneranso kudana ndi zinthu zoipa zimene zipembedzo zimachita. Zipembedzo zonyenga zimalola kuti anthu ake azichita ndale komanso zimalimbikitsa chiwerewere ndi dyera. (Werengani Salimo 97:10; Chivumbulutso 18:7, 9, 11-17) Zimenezi zaphetsa anthu ambiri.

24, 25. Kodi kulambira Yehova kungatithandize bwanji kuti tikhale ndi mtendere wamumtima komanso chikumbumtima chabwino?

24 Tisanayambe kulambira Yehova, tonsefe mwa njira inayake tinkachita nawo zinthu zoipa zimene anthu a dziko la Satanali amachita. Koma panopa tinasintha. Tinaphunzira kuti dipo la Yesu lingatithandize ndipo tinadzipereka kwa Mulungu. Tingati tinalandira “nyengo zotsitsimutsa . . . kuchokera kwa Yehova.” Panopa tili ndi mtendere wamumtima komanso chikumbumtima chabwino  chifukwa chodziwa kuti tikusangalatsa Mulungu.​—Machitidwe 3:19; Yesaya 1:18.

25 Ngakhale anthu amene poyamba anali m’chipembedzo kapena m’gulu limene sililemekeza moyo, Yehova angawakhululukire pogwiritsa ntchito dipo la Yesu. Timayamikira kwambiri mphatso ya moyo imene Yehova anatipatsa. Tingasonyeze kuti timayamikira mphatso imeneyi pothandiza ena kuti adziwe Yehova, akhale naye pa ubwenzi wolimba komanso asiye kugwirizana ndi dziko la Satanali.​—2 Akorinto 6:1, 2.

MUZIUZA ENA ZA UFUMU WA MULUNGU

26-28. (a) Kodi Yehova anapatsa Ezekieli ntchito yapadera iti? (b) Kodi ndi ntchito iti imene Yehova akufuna kuti tizigwira masiku ano?

26 Kale ku Isiraeli, Yehova anauza mneneri Ezekieli kuti achenjeze anthu kuti Yerusalemu awonongedwa. Anamuuzanso kuti aphunzitse anthuwo zimene angachite kuti adzapulumuke. Ezekieli akanapanda kuchenjeza anthuwo, akanakhala ndi mlandu wa magazi. (Ezekieli 33:7-9) Koma Ezekieli anasonyeza zoti ankaona kuti moyo ndi wamtengo wapatali, ndipo anayesetsa kuuza anthuwo uthenga wofunika umenewu.

27 Ifenso Yehova watipatsa ntchito yoti tichenjeze anthu kuti posachedwapa dziko loipali liwonongedwa. Tiyeneranso kuwathandiza kuti adziwe zoyenera kuchita kuti adzapulumuke. (Yesaya 61:2; Mateyu 24:14) Tiziyesetsa kuuza anthu uthenga umenewu. Tikatero tidzatha kunena zofanana ndi zimene Paulo ananena. Iye anati: “Ine ndine woyera pa mlandu wa magazi a anthu onse. Pakuti sindinakubisireni kanthu, koma ndinakuuzani chifuniro chonse cha Mulungu.”​—Machitidwe 20:26, 27.

28 Koma pali zinanso zimene tingachite kuti tikhale oyera, ndipo tidzakambirana zimenezi m’mutu wotsatira.