“Nthawi zonse muzitsimikiza kuti chovomerezeka kwa Ambuye n’chiti.”​—AEFESO 5:10.

1. Kodi tiyenera kuchita chiyani kuti kulambira kwathu kuzisangalatsa Yehova, ndipo n’chifukwa chiyani?

YESU anati: “Olambira oona adzalambira Atate motsogoleredwa ndi mzimu ndi choonadi, pakuti Atate amafuna oterowo azimulambira.” (Yohane 4:23; 6:44) Tonsefe tiyenera ‘kumatsimikiza kuti chovomerezeka kwa Ambuye n’chiti.’ (Aefeso 5:10) Koma nthawi zina kuchita zimenezi kumakhala kovuta. Satana amayesetsa kutisocheretsa n’cholinga choti tizichita zinthu zimene Yehova sasangalala nazo.​—Chivumbulutso 12:9.

2. Fotokozani zimene zinachitikira Aisiraeli pafupi ndi phiri la Sinai.

2 Kodi Satana amatisocheretsa bwanji? Njira imodzi imene amachitira zimenezi ndi kutisokoneza kuti tisamathe kusiyanitsa chabwino ndi choipa. Taganizirani zimene zinachitikira Aisiraeli ali pafupi ndi phiri la Sinai. Mose anali atapita kuphiriro ndipo Aisiraeli ankamudikira. Koma atatopa ndi kudikira, anauza Aroni kuti awapangire mulungu woti azimulambira. Aroni anawapangira fano la mwana wa ng’ombe lagolide. Kenako anthuwo anayamba kuchita chikondwerero. Ankavina mozungulira mwana wa ng’ombeyo komanso ankamuweramira. Ankaganiza kuti akamaweramira mwana wa ng’ombeyo ndiye kuti akulambira Yehova. Zimene ankachitazi zinali zolakwika ngakhale kuti ankaona ngati akuchita “chikondwerero cha Yehova.” Yehova anaona  kuti anthuwo akulambira mafano ndipo ambiri anaphedwa. (Ekisodo 32:1-6, 10, 28) Kodi tikuphunzira chiyani pamenepa? Musamapusitsidwe. “Musakhudze chinthu chilichonse chodetsedwa” ndipo muzilola kuti Yehova azikuphunzitsani kusiyanitsa zabwino ndi zoipa.​—Yesaya 52:11; Ezekieli 44:23; Agalatiya 5:9.

3, 4. Kodi kudziwa mmene zikondwerero zotchuka zinayambira kutithandiza bwanji?

3 Pamene Yesu anali padzikoli anaphunzitsa atumwi ake kuti azikhala zitsanzo zabwino pa nkhani ya kulambira kovomerezeka. Yesu atafa, atumwiwo anapitiriza kuphunzitsa ophunzira atsopano mfundo za Yehova. Koma atumwi atafa, aphunzitsi onyenga anayamba kuphunzitsa mipingo mfundo zabodza komanso kulimbikitsa Akhristu kuti azichita miyambo ndi zikondwerero zachikunja. Ndipo anasintha mayina a zikondwerero zina kuti zizioneka ngati zachikhristu. (2 Atesalonika 2:7, 10; 2 Yohane 6, 7) Zina mwa zikondwerero zimenezi ndi zotchukabe mpaka pano ndipo zimapangitsa kuti anthu azikhulupirira mfundo zabodza komanso azikhulupirira zamizimu. *​—Chivumbulutso 18:2-4, 23.

4 Masiku ano anthu ambiri padziko lonse amaona kuti zikondwerero ndiponso maholide ndi zofunika kwambiri. Koma mukapitiriza kuphunzira mmene Yehova amaonera zinthu, mwina mungaone kuti muyenera kusintha mmene mumaonera zikondwerero zina. Zimenezi sizingakhale zophweka koma Yehova adzakuthandizani. Tiyeni tikambirane mmene zikondwerero zina zotchuka masiku ano zinayambira. Zimenezi zitithandiza kudziwa ngati Yehova amasangalala ndi zikondwerero zimenezi kapena ayi.

 KODI KHIRISIMASI INAYAMBA BWANJI?

5. Kodi pali umboni wotani wosonyeza kuti Yesu sanabadwe pa 25 December?

5 Anthu a m’mayiko ambiri amakondwerera Khirisimasi pa 25 December, ndipo ambiri amaganiza kuti limeneli ndi tsiku limene Yesu anabadwa. Baibulo silitiuza tsiku kapena mwezi umene Yesu anabadwa koma limangotiuza zinthu zina zomwe zimatithandiza kudziwa nthawi imene anabadwa. Luka analemba kuti pamene Yesu ankabadwa ku Betelehemu, abusa “anali kugonera kubusa akuyang’anira nkhosa zawo.” (Luka 2:8-11) M’mwezi wa December, ku Betelehemu kumakhala nyengo yozizira kwambiri ndiponso kumagwa mvula, choncho sizikanatheka kuti abusa azigona kunja usiku ndi ziweto zawo. Kodi pamenepa tikuphunzirapo chiyani? Tikuphunzira kuti Yesu sanabadwe nthawi yozizira kapena yamvula, zomwe zikusonyeza kuti sanabadwe mu December. Baibulo ndiponso mbiri yakale zimasonyeza kuti Yesu anabadwa pakati pa mwezi wa September ndi October.

6, 7. (a) Kodi miyambo yambiri imene imachitika pa Khirisimasi inayamba bwanji? (b) Kodi tiyenera kupereka mphatso kwa anthu chifukwa chiyani?

6 Ndiye kodi Khirisimasi inayamba bwanji? Inachokera ku zikondwerero zachikunja. Chimodzi mwa zikondwerero zimenezi ndi cha Aroma chotchedwa Saturnalia chomwe ankachitira mulungu wa ulimi wotchedwa Saturn. Buku lina limati: “Miyambo yambiri imene imachitika pa Khirisimasi inachokera ku chikondwerero cha Aroma chotchedwa Saturnalia chomwe chinkachitika m’katikati mwa mwenzi wa December. Ina mwa miyambo imene inachokera pa zimene anthu ankapanga pa chikondwererochi ndi kuchita phwando, kupatsana mphatso komanso kuyatsa makandulo.” (The Encyclopedia Americana) Chikondwerero chinanso chimene chinkachitika pa 25 December ndi chokumbukira kubadwa kwa mulungu wa dzuwa wa ku Perisiya wotchedwa Mithra.

 7 Komabe anthu ambiri amene amakondwerera Khirisimasi masiku ano saganizira za miyambo yachikunja imene anthu amene anayambitsa chikondwererochi ankachita. Iwo amangoona kuti nyengo ya Khirisimasi ndi nthawi yosangalala limodzi ndi achibale, kudya zakudya zabwino komanso kupatsana mphatso. N’zosachita kufunsa kuti timakonda anzathu komanso achibale athu. Nayenso Yehova amafuna kuti atumiki ake azigawana zinthu. Koma lemba la 2 Akorinto 9:7 limati: “Mulungu amakonda munthu wopereka mokondwera.” Zimenezi zikusonyeza kuti Yehova  safuna kuti tizipatsa ena mphatso pa zochitika zapadera zokha. Atumiki a Mulungu amasangalala kupereka mphatso kapena kucheza ndi achibale kapena anzawo pa nthawi iliyonse ndipo sayembekezera kuti anthuwo awabwezere kenakake. Amapereka mphatso chifukwa choti amakonda ena.​—Luka 14:12-14.

Kudziwa mmene zikondwerero zinayambira kungatithandize kudziwa zikondwerero zomwe tiyenera kupewa

8. Kodi okhulupirira nyenyezi anapatsa Yesu mphatso atangobadwa kumene? Fotokozani.

8 Pofuna kuikira kumbuyo mfundo yoti kupatsana mphatso pa Khirisimasi n’koyenera, anthu ambiri amanena kuti anzeru atatu anapita kukapatsa Yesu mphatso ali wakhanda komanso ali mukhola. N’zoona kuti azibambo ena anapita kukaona Yesu ndipo anamupatsa mphatso. Kale anthu ankakonda kupereka mphatso kwa munthu amene ankamuona kuti ndi wofunika kwambiri. (1 Mafumu 10:1, 2, 10, 13) Koma kodi mukudziwa kuti Baibulo limanena kuti anthu amenewa anali okhulupirira nyenyezi, anthu omwe ankachita zamatsenga ndipo sankalambira Yehova? Komanso anthuwa sanapite kukaona Yesu atangobadwa kumene kapenanso ali m’khola. Baibulo limanena kuti pamene anthuwa anapita kukaona Yesu, anapeza “mwanayo ndi mayi ake” ali m’nyumba.​—Mateyu 2:1, 2, 11.

ZIMENE BAIBULO LIMANENA PA NKHANI YOKUMBUKIRA TSIKU LOBADWA

9. Kodi Baibulo limatchula zikondwerero zokumbukira masiku obadwa a anthu ati?

9 Tsiku limene mwana wabadwa limakhala lachisangalalo. (Salimo 127:3) Koma zimenezi sizikutanthauza kuti tiyenera kuchita mwambo wokondwerera tsiku lobadwa. Taganizirani mfundo iyi: Baibulo limatchula zikondwerero za masiku obadwa a anthu awiri okha. Wina anali Farao wa ku Iguputo ndipo wina anali Mfumu Herode Agiripa. (Werengani Genesis 40:20-22; Maliko 6:21-29.) Koma mafumu awiri onsewa sanali atumiki a Yehova. Ndipotu m’Baibulo  mulibe mavesi amene amanena za mtumiki wa Yehova aliyense amene ankakondwerera tsiku lobadwa.

10. Kodi Akhristu a m’nthawi ya atumwi ankaona bwanji zikondwerero zokumbukira tsiku lobadwa?

10 Buku lina linanena kuti: Akhristu a m’nthawi ya atumwi “ankaona kuti mwambo wokumbukira tsiku lobadwa ndi wachikunja.” (The World Book Encyclopedia) Mwambo umenewu ndi wochokera ku zikhulupiriro zabodza. Mwachitsanzo, anthu a ku Girisi ankakhulupirira kuti munthu aliyense amatetezedwa ndi mzimu umene unalipo pa nthawi imene munthuyo ankabadwa. Ankakhulupiriranso kuti pamakhala mgwirizano pakati pa mzimuwo ndi mulungu amene anabadwa pa tsiku limene munthuyo anabadwa. Kuwonjezera pamenepa, zikondwerero zokumbukira masiku obadwa ndi zogwirizana ndi kukhulupirira nyenyezi.

11. Kodi Yehova amafuna kuti tizikhala opatsa kwa anzathu pa tsiku limene anabadwa lokha?

11 Anthu ambiri amaona kuti tsiku lawo lobadwa ndi lapadera kwambiri ndipo pa tsikuli payenera kuchitika zinthu zosonyeza kuti amakondedwa komanso amayamikiridwa. Komatu tiyenera kusonyeza chikondi kwa anzathu chaka chonse, osati pa tsiku limene anabadwa lokha. Yehova amafuna kuti tizikhala okoma mtima komanso opatsa nthawi zonse. (Werengani Machitidwe 20:35.) Timamuthokoza tsiku lililonse chifukwa choti anatipatsa moyo, osati pa tsiku limene tinabadwa lokha.​—Salimo 8:3, 4; 36:9.

Akhristu oona amapereka mphatso chifukwa chokonda ena

12. Kodi tsiku lomwalira limaposa bwanji tsiku lobadwa?

12 Lemba la Mlaliki 7:1 limati: “Mbiri yabwino imaposa mafuta onunkhira, ndipo tsiku lomwalira limaposa tsiku lobadwa.” Kodi tsiku lomwalira limaposa bwanji tsiku lobadwa? Munthu akangobadwa kumene amakhala kuti alibe mbiri iliyonse, kaya yabwino kapena yoipa. Koma tikamatumikira Yehova komanso kuchitira ena zabwino, timapanga “mbiri yabwino” ndipo tikamwalira Yehova amatikumbukirabe. (Yobu 14:14, 15) Anthu a Yehova sakumbukira tsiku  lobadwa, kaya lawo kapena la Yesu. Ndipotu mwambo wokha umene Yesu anatilamula kuti tizichita ndi wokumbukira imfa yake.​—Luka 22:17-20; Aheberi 1:3, 4.

KODI ISITALA INAYAMBA BWANJI?

13, 14. Kodi Isitala ndi yogwirizana ndi chiyani?

13 Anthu ambiri akamachita chikondwerero cha Isitala amakhulupirira kuti akukondwerera kuuka kwa Yesu. Koma  zoona ndi zakuti chikondwerero cha Isitala ndi chogwirizana ndi mulungu wamkazi wa m’bandakucha ndi nyengo ya kumapeto kwa dzinja, dzina lake Eostre. Buku lina linafotokoza kuti ameneyu analinso mulungu wobereketsa. (The Dictionary of Mythology) Miyambo ina ya pa Isitala ndi yogwirizana kwambiri ndi zimenezi. Mwachitsanzo, buku linanso linanena kuti mazira “akhala akudziwika monga zizindikiro za moyo woyamba kumene komanso kuuka.” (Encyclopædia Britannica) Komanso akalulu akhala akugwiritsidwa ntchito pa kulambira konyenga ngati zizindikiro za kubereketsa. Apa n’zoonekeratu kuti Isitala siyogwirizana ndi kuuka kwa Yesu.

14 Kodi Yehova amasangalala akaona kuti anthu akuphatikiza miyambo ya zipembedzo zonyenga ndi kuuka kwa Mwana wake? Ayi. (2 Akorinto 6:17, 18) Ndipotu Yehova sanatilamule kuti tizikumbukira kuuka kwa Yesu.

KODI KUKONDWERERA CHAKA CHATSOPANO KUNAYAMBA BWANJI?

15. Kodi chikondwerero cha chaka chatsopano chinayamba bwanji?

15 Zimene anthu amachita pokondwerera chaka chatsopano zimasiyanasiyana. Koma m’madera ambiri pa 31 December anthu amachezera ndi cholinga choti aone kutha kwa chaka, komanso kuyamba kwa chaka chatsopano. Usiku umenewu anthu amaledzera, kuchita chiwerewere, kupatsana mphatso komanso kulonjeza zinthu zosiyanasiyana zimene akufuna kuchita m’chaka chatsopanocho. Zinthu zimene anthu ambiri amachita usiku umenewu ndi zogwirizana ndi miyambo yachikunja. Komanso anthu amaphulitsa makombola ndipo amati amachita zimenezi pofuna kuthamangitsa mizimu yoipa. Buku lina linati: “Anthu a ku Roma ankaona kuti tsiku loyamba la chaka ndi tsiku lolemekeza Janus yemwe anali mulungu wa mageti, zitseko komanso chiyambi ndi mapeto. . . . M’chaka cha 487 A.D., tsiku  loyamba la chaka linakhazikitsidwa kuti ndi tsiku la Chikondwerero cha Mdulidwe ndipo matchalitchi anayamba kuona kuti tsikuli ndi loyera. Poyamba anthu sankaloledwa kuchita maphwando pa tsikuli chifukwa choti anthu achikunja ndi amene ankachita zimenezo. Koma pang’ono ndi pang’ono zimenezi zinasintha ndipo anthu anayamba kumachita maphwando pa tsikuli.”​—The 1966 World Book Encyclopedia, Volume 14, tsamba 237.

UKWATI UMENE MULUNGU AMASANGALALA NAWO

16, 17. Kodi tiyenera kuganizira chiyani tikamakonzekera kupanga ukwati?

16 Ukwati ndi mwambo wosangalatsa. Padziko lonse anthu amapanga mwambowu mosiyanasiyana. Ndipo nthawi zambiri saganizira mmene miyambo yomwe imachitika pa ukwati inayambira, choncho sadziwa kuti miyambo ina inachokera ku miyambo yachikunja. Koma Akhristu omwe akukonzekera kupanga ukwati ayenera kuonetsetsa kuti phwando la ukwati wawo ndi losangalatsa Yehova. Akadziwa mmene miyambo ina ya ukwati inayambira, angathe kusankha zinthu zoyenera kuchita pa ukwati wawo.​—Maliko 10:6-9.

17 Anthu ena amakhulupirira kuti miyambo ina ya ukwati imabweretsa ‘mwayi’ kwa amene akukwatiranawo. (Yesaya 65:11) Mwachitsanzo, m’madera ena anthu amawaza akwati mpunga kapena zinthu zina. Amakhulupirira kuti kuchita zimenezi kumachititsa okwatiranawo kukhala ndi ana, kukhala osangalala, kukhala ndi moyo wautali komanso kutetezedwa ku mizimu yoipa. Koma Akhristu amapewa miyambo iliyonse yogwirizana ndi chipembedzo chonyenga.​—Werengani 2 Akorinto 6:14-18.

18. Kodi ndi mfundo za m’Baibulo ziti zomwe tiyenera kuziganizira pokonzekera ukwati?

18 Akhristu amafuna kuti phwando la ukwati wawo likhale losangalatsa komanso lolemekezeka. Amafunanso kuti  anthu omwe abwera asangalale. Anthu omwe aitanidwa ku ukwati sayenera kulankhula mawu onyoza, olaula komanso mawu omwe angachititse manyazi akwati ndiponso anthu ena. (Miyambo 26:18, 19; Luka 6:31; 10:27) Mkhristu sayenera kupanga ukwati ‘modzionetsera ndi zimene munthu ali nazo pa moyo wake.’ (1 Yohane 2:16) Ngati mukukonzekera kupanga ukwati, onetsetsani kuti tsiku la ukwati wanu lidzakhale tsiku loti mukamadzalikumbukira muzidzasangalala.​—Onani Mawu Akumapeto 28.

MMENE MWAMBO WOWOMBANITSA KAPENA KUKWEZA M’MWAMBA MATAMBULA UNAYAMBIRA

19, 20. Kodi mwambo wowombanitsa kapena kukweza m’mwamba matambula unayamba bwanji?

19 Mwambo wina wodziwika kwambiri umene umachitika pa maukwati komanso zikondwerero zina ndi mwambo wowombanitsa kapena kukweza m’mwamba matambula. Pa mwambowu, munthu mmodzi amafunira zabwino akwati ndipo anthu ena amakweza matambula awo m’mwamba. Koma kodi Akhristu ayenera kuona bwanji mwambo umenewu?

20 Buku lina limati: “Mwambo wokweza matambula m’mwamba unachokera ku mwambo wachikunja wopereka nsembe kwa milungu. Nsembe zake zinkakhala magazi kapena vinyo ndipo ankapereka nsembe zimenezi popempha madalitso. Ankapereka pemphero lachidule lakuti ‘moyo wautali’ kapena ‘mukhale ndi thanzi labwino.’” (International Handbook on Alcohol and Culture) Anthu akale ankakweza matambula m’mwamba popempha madalitso kwa milungu yawo. Koma Yehova sapereka choncho madalitso.​—Yohane 14:6; 16:23.

“INU OKONDA YEHOVA DANANI NACHO CHOIPA”

21. Kodi Akhristu ayenera kupewa zikondwerero zina ziti?

21 Musanasankhe kuti mupange nawo chikondwerero  chinachake kapena ayi, muziganizira kaye khalidwe komanso maganizo amene chikondwererocho chimalimbikitsa. Mwachitsanzo, zikondwerero zina zimaphatikizapo kuvina modzutsa chilakolako chogonana, ndipo pachikondwererocho anthu amamwa kwambiri mowa komanso amachita chiwerewere. Ndipo zikondwererozi zingalimbikitsenso anthu kukhala ndi mtima wokonda kwambiri dziko lawo kapena khalidwe logonana pakati pa amuna kapena akazi okhaokha. Ngati timapanga nawo zikondwererozi, kodi tikudanadi ndi zimene Yehova amadana nazo?​—Salimo 1:1, 2; 97:10; 119:37.

22. Kodi n’chiyani chingathandize Mkhristu kusankha ngati angachite nawo chikondwerero chinachake kapena ayi?

22 Akhristu ayenera kusamala kuti asamachite nawo zikondwerero zimene zimapangitsa kuti anthu asamalemekeze Mulungu. Mtumwi Paulo analemba kuti: “Kaya mukudya kapena kumwa kapena mukuchita china chilichonse, chitani zonse kuti zibweretse ulemerero kwa Mulungu.” (1 Akorinto 10:31; onani see Mawu Akumapeto 29.) N’zoona kuti pali zikondwerero zina zomwe sizimakhudzana ndi zachiwerewere, chipembedzo chonyenga kapena kukonda kwambiri dziko lako. Ngati chikondwerero chinachake sichisemphana ndi mfundo za m’Baibulo, tiyenera kusankha tokha ngati tingachite nawo kapena ayi. Komabe tiyeneranso kuganizira mmene zimene tingasankhezo zingakhudzire anthu ena.

ZOLANKHULA KOMANSO ZOCHITA ZANU ZIZILEMEKEZA YEHOVA

23, 24. Kodi tingafotokozere bwanji achibale athu omwe si Mboni zomwe tasankha pa nkhani ya zikondwerero zosiyanasiyana?

23 Pofika pano muyenera kuti munasiya kale kuchita nawo zikondwerero zimene Yehova amadana nazo. Koma n’kutheka kuti achibale anu amene si Mboni amaona kuti mukuchita zimenezi chifukwa choti munasiya kuwakonda kapena simukufunanso kumachita nawo zinthu. Mwina amaona  kuti maholide ngati amenewa ndi nthawi yokhayo imene achibale onse amakumana pamodzi n’kumacheza. Ngati zili choncho, kodi mungatani? Pali njira zambiri zowatsimikizira kuti mumawakonda komanso mumawaona kuti ndi ofunika kwambiri. (Miyambo 11:25; Mlaliki 3:12, 13) Mukhoza kuwaitana pa zochitika zina kuti mucheze nawo.

24 Ngati abale anu akufuna kudziwa chifukwa chake munasiya kukonda maholide enaake, mukhoza kufufuza m’mabuku athu ndiponso pa jw.org kuti mupeze mfundo zothandiza. Musakambirane nawo m’njira yoti aziona ngati mukungofuna kuwina mkangano kapena mukufuna kuwakakamiza kuti aziyendera mfundo zanu. Athandizeni achibalewo kudziwa kuti munaganizira mofatsa mfundo zambiri zokhudza chikondwererocho kenako n’kusankha zomwe mukuona kuti n’zoyenera kwa inuyo. Muyenera kukambirana nawo mofatsa ndipo “nthawi zonse mawu anu azikhala achisomo, okoma ngati kuti mwawathira mchere.”​—Akolose 4:6.

25, 26. Kodi makolo angathandize bwanji ana awo kukonda mfundo za Yehova?

25 Tonse tiyenera kumvetsa chifukwa chake timaona kuti si bwino kuchita nawo zikondwerero zinazake. (Aheberi 5:14) Cholinga chathu ndi kusangalatsa Yehova. Ndipo ngati ndife makolo, tiyenera kupeza nthawi yothandiza ana athu kumvetsa ndiponso kukonda mfundo za m’Baibulo. Akayamba kuona kuti Yehova ndi weniweni, adzafunitsitsa kuchita zimene zingamusangalatse.​—Yesaya 48:17, 18; 1 Petulo 3:15.

26 Yehova amasangalala akaona kuti tikuyesetsa kumulambira moyenera ndiponso mopanda chinyengo. (Yohane 4:23) Koma anthu ambiri amaganiza kuti n’zosatheka kuti munthu achite zinthu mopanda chinyengo m’dziko lachinyengoli. Kodi zimenezi ndi zoona? Tikambirana zimenezi m’mutu wotsatira.

^ ndime 3 Ngati mukufuna kudziwa zambiri zokhudza zikondwerero zina, onani Watch Tower Publications Index, Buku la Mboni za Yehova Lofufuzira Nkhani kapena pitani pa webusaiti ya jw.org.