Baibulo limanena kuti Yehova ndi mzimu. Iye analenganso angelo ambirimbiri omwe ali ndi matupi auzimu.​—Yohane 4:24; 2 Akorinto 3:17, 18.

Poyambirira, Yehova analipo yekha. Kenako anayamba kulenga angelo omwe ndi amphamvu komanso anzeru kuposa anthufe. Angelowa alipo ambirimbiri ndipo Danieli anaona m’masomphenya angelo okwana 100 miliyoni.​—Danieli 7:10; Aheberi 1:7.

Angelowa analengedwa dziko lapansili lisanalengedwe. (Yobu 38:4-7) Iwowa si anthu amene anamwalira padzikoli n’kupita kumwamba.

Yehova analenga angelo ambirimbiri