Posachedwapa Satana ndi ziwanda zake sazidzasocheretsanso anthu

Nthawi yoti Satana ndi ziwanda zake asocheretse anthu itha posachedwapa. Yehova anawathamangitsa kale kumwamba. (Chivumbulutso 12:9) Mtumwi Yohane anaona masomphenya osonyeza kuti posachedwapa Yehova athana ndi Satana ndi ziwanda. Iye analemba kuti: “Ndipo ndinaona mngelo akutsika kuchokera kumwamba ali ndi kiyi wa paphompho [dzenje lakuya kwambiri] ndi unyolo waukulu m’dzanja lake. Kenako anagwira chinjoka, njoka yakale ija, amene ndi Mdyerekezi ndiponso Satana, ndi kumumanga zaka 1,000. Ndipo anamuponyera m’phompho ndi kutseka pakhomo pa phompholo n’kuikapo chidindo kuti asasocheretsenso mitundu ya anthu kufikira zitatha zaka 1,000.” (Chiv. 20:1-3) Kenako Mdyerekezi pamodzi ndi ziwanda zake adzawonongedwa ndipo sadzakhalaponso.​—Chivumbulutso 20:10.

Anthu onse oipa adzawonongedwanso.​—Salimo 37:9, 10; Luka 13:5.

 Anthu Amene Anamwalira Adzakhalanso ndi Moyo

Anthu amene anamwalira adzaukitsidwa n’kumakhala padzikoli

Satana ndi ziwanda akadzawonongedwa, Yehova adzadalitsa kwambiri anthu. Yesu anayerekezera imfa ndi tulo. Izi zikutanthauza kuti munthu akafa sadziwa chilichonse ndipo amangokhala ngati wagona popanda kulota chilichonse. (Yohane 11:11-14) Yesu ananena zimenezi chifukwa ankadziwa kuti posachedwapa anthu amene anafa adzaukitsidwa. Paja iye anati: “Idzafika nthawi pamene onse ali m’manda achikumbutso . . . adzatuluka.”​—Yohane 5:28, 29; Yerekezerani ndi Machitidwe 24:15.

Anthu oukitsidwawo adzakhala padziko lomweli. M’malo molandira uthenga wa maliro, tizidzalandira mauthenga osangalatsa oti akutiakuti aja aukitsidwa. Zidzakhala zosangalatsa kwambiri kulandira anthu amene adzaukitsidwe.