Hava atamvera zimene Satana ananena, anasonyeza kuti wagwirizana ndi Satanayo poukira Mulungu

Angelo onse amene Yehova analenga anali abwino. Kenako mngelo mmodzi anasintha n’kukhala woipa. Dzina lake ndi Satana Mdyerekezi. Iye ankafuna kuti anthu padzikoli azilambira iyeyo osati Yehova. Tiyeni tione zimene zinachitika.

M’munda wa Edeni munali mitengo yambiri ya zipatso zokoma. Yehova anauza Adamu ndi Hava kuti angathe kudya zipatsozo. Koma panali mtengo umodzi umene Mulungu anawauza kuti asadye zipatso zake. Iye anawauza kuti akadzadya, adzafa ndithu.​—Genesis 2:9, 16, 17.

Tsiku lina Hava ali yekha anamva njoka ikumulankhula. Koma anali Satana Mdyerekezi amene anachititsa kuti njokayo ikhale ngati ikulankhuladi. Iye anauza Hava kuti akadya zipatso za mtengo umene Mulungu ananena kuti asadye, adzafanana ndi Mulungu ndipo sadzafa. Zimene Satana ananenazi zinali zabodza, koma Hava anazikhulupirira n’kudya chipatsocho. Kenako anam’patsa Adamu ndipo nayenso anadya.​—Genesis 3:1-6.

Nkhaniyi imatiphunzitsa kuti Satana ndi wotsutsa komanso wabodza. Iye ananamiza Hava kuti sangafe ngati samvera Mulungu. Koma onse Adamu ndi Hava anafa. Satana sanafe nthawi yomweyo koma adzafa chifukwa anachimwa. Iye akupitirizabe kusocheretsa anthu. Ndipo amafuna kuti anthu asamamvere malamulo a Mulungu.​—Yohane 8:44.

 Angelo Enanso Anakhala Oipa

Patapita nthawi, angelo enanso anakhala oipa. Angelowa anaona akazi okongola padzikoli ndipo anafuna kuti agone nawo. Iwo anatsika ndipo anasintha matupi awo n’kukhala ngati anthu, ndiyeno anakwatira akaziwo. Zimenezi zinali zosagwirizana ndi cholinga cha Mulungu.​—Genesis 6:1, 2; Yuda 6.

Angelo oipa anabwera kudzagona ndi akazi padzikoli

Izi zinabweretsa mavuto ambiri kwa anthu. Ana amene akaziwo anabereka, anali zimphona kapena kuti anthu amphamvu kwambiri ndipo anali ankhanza. Pamapeto pake dziko lonse linadzadza ndi anthu achiwawa ndipo Yehova anaganiza zoti awononge anthu oipawo ndi chigumula. Nowa ndi banja lake lokha ndi amene anapulumuka chifukwa chakuti anali olungama.​—Genesis 6:4, 11; 7:23.

Angelo oipawa anavula matupi amene anavala aja n’kubwerera kumwamba ndipo sanafe nawo. Koma Mulungu anawapatsa chilango choti asakhalenso limodzi ndi angelo okhulupirika. Iye sanawalolenso kuvala matupi a anthu ndipo adzawonongedwa pa tsiku la chiweruzo.​—2 Petulo 2:4; Yuda 6.

 Satana Anathamangitsidwa Kumwamba

Satana ndi angelo ake oipa anagwetsedwa kuchokera kumwamba

Mu 1914 kunali nkhondo kumwamba. Baibulo limati: “Ndipo kumwamba kunabuka nkhondo: Mikayeli ndi angelo ake anamenyana ndi chinjoka. Chinjokacho ndi angelo ake chinamenya nkhondo, koma sichinapambane, ndipo malo awo sanapezekenso kumwamba. Choncho chinjokacho chinaponyedwa pansi, njoka yakale ija, iye wotchedwa Mdyerekezi ndi Satana, amene akusocheretsa dziko lonse lapansi kumene kuli anthu. Iye anaponyedwa kudziko lapansi, ndipo angelo akenso anaponyedwa naye limodzi.”

Kodi zotsatirapo zake zinali zotani? Baibulo limafotokoza kuti: “Pa chifukwa chimenechi, kondwerani kumwamba inu ndi inu okhala kumeneko.” Angelo anasangalala chifukwa Satana komanso angelo oipa anathamangitsidwa kumwamba. Nanga bwanji za anthu padziko lapansi? Baibulo limati: “Tsoka dziko lapansi ndi nyanja, chifukwa Mdyerekezi watsikira kwa inu, ndipo ali ndi mkwiyo waukulu podziwa kuti wangotsala ndi kanthawi kochepa.”​—Chivumbulutso 12:7-9, 12.

Satana ndi angelo ake oipa amasocheretsa anthu komanso kubweretsa mavuto padzikoli. Angelo oipawa ndi adani a Mulungu ndipo amadziwika ndi dzina lakuti ziwanda.