Genesis 15:5

MFUNDO YAIKULU: Muzigwiritsa ntchito zinthu zooneka kuti anthu amvetse mfundo zikuluzikulu.

MMENE MUNGACHITIRE:

  • Muzisankha zinthu zimene zingathandizedi pophunzitsa. Mungagwiritse ntchito zithunzi, mapu, matchati kapena zinthu zina pofuna kutsindika mfundo zofunika osati timfundo ting’onoting’ono. Mukamaliza, anthu azikumbukira mfundo yaikuluyo osati zinthu zooneka zokhazo.

  • Zinthuzo zizikhala zoti aliyense atha kuziona.