Mateyu 13:34, 35

MFUNDO YAIKULU: Munkhani yanu muziikamo mafanizo ochititsa chidwi komanso othandiza anthu kumvetsa mfundo zikuluzikulu.

MMENE MUNGACHITIRE:

  • Mafanizo azikhala osavuta kumva. Mofanana ndi Yesu, muzigwiritsa ntchito zinthu zing’onozing’ono pofotokoza zikuluzikulu komanso zinthu zosavuta pofotokoza zinthu zovuta. Musamatchule mfundo zambirimbiri zomwe zikhoza kusokoneza anthu. Zimene mukutchula mufanizo zizigwirizanadi ndi mfundo yamunkhani yanu kuti anthu asamachite kudzifunsa kuti, ‘Kodi pamenepa ndiye zikugwirizana bwanji?’

  • Muziganizira mfundo zothandiza kwa anthu. Zitsanzo zanu zizikhala zodziwika komanso zochititsa chidwi kwa anthu amene mukulankhula nawo. Musamagwiritse ntchito mafanizo amene angakhumudwitse kapena kuchititsa manyazi anthu.

  • Muzithandiza anthu kudziwa mfundo yaikulu. Zitsanzo zanu zizikhala pa mfundo zikuluzikulu osati zing’onozing’ono. Anthu azikumbukira mfundo yaikuluyo osati fanizo lokhalo.