Mlaliki 12:13, 14

MFUNDO YAIKULU: Mawu anu omaliza azithandiza anthu kuvomereza zimene aphunzira n’kuyamba kuzigwiritsa ntchito.

MMENE MUNGACHITIRE:

  • Mawu omaliza azikhala ogwirizana ndi mutu wa nkhani yonse. Muzibwereza mfundo zikuluzikulu komanso mutu wa nkhani.

  • Limbikitsani anthu kutsatira zimene aphunzira. Auzeni anthu zoyenera kuchita komanso zifukwa zochitira zinthuzo. Mawu anu omaliza azikhala ochokera mumtima ndipo muziwanena motsimikiza.

  • Mawu omaliza azikhala achidule komanso osavuta. Musatchule mfundo ina yatsopano. Mawu ake angokhala ochepa koma othandiza anthu kudziwa zoyenera kuchita.