CHOONADI chokhudza chiyani? Cha mafunso ofunika kwambiri amene anthu amafuna kudziwa mayankho ake. Mwina nanunso munafunsapo mafunso ngati awa:

  • Kodi Mulungu amatiganiziradi?

  • Kodi nkhondo ndi kuvutika zidzathadi?

  • Kodi chimachitika n’chiyani munthu akamwalira?

  • Kodi akufa adzauka?

  • Kodi ndingatani kuti Mulungu aziyankha mapemphero anga?

  • Kodi ndingatani kuti ndikhale ndi moyo wosangalala?

Kodi mungapeze kuti mayankho ake? Pali mabuku ambirimbiri amene amayesa kuyankha mafunso amenewa. Koma mabuku ambiri amatsutsana. Ena amagwira ntchito nthawi yochepa ndipo kenako amalembedwanso kapena kulowedwa m’malo ndi mabuku ena.

Koma pali buku lina limene lili ndi mayankho odalirika. Bukuli limanena zoona zokhazokha. Popemphera kwa Mulungu, Yesu Khristu anati: “Mawu anu ndiwo choonadi.” (Yohane 17:17) Mawu amenewo ndi Baibulo. Pamasamba otsatirawa, pali mayankho omveka bwino ndiponso olondola a mafunso amene ali pamwambawo.

Kodi Mulungu Amatiganiziradi?

CHIFUKWA CHAKE ANTHU AMAFUNSA FUNSOLI: Tikukhala m’dziko limene anthu ambiri ndi ankhanza ndiponso opanda chilungamo. Zipembedzo zambiri zimaphunzitsa kuti ndi cholinga cha Mulungu kuti tizivutika.

ZIMENE BAIBULO LIMAPHUNZITSA: Mulungu sindiye amachititsa zinthu zoipa. Lemba la Yobu 34:10 limati: “N’kutali ndi Mulungu kuchita choipa, ndi Wamphamvuyonse kuchita chosalungama.” Mulungu amakonda anthu ndipo amawafunira zabwino. N’chifukwa chake Yesu anatiphunzitsa kupemphera kuti: “Atate wathu wa kumwamba . . . Ufumu wanu ubwere. Chifuniro chanu chichitike, monga kumwamba, chomwechonso pansi pano.” (Mateyo 6:9, 10) Mulungu amatiganizira kwambiri motero kuti wachita zambiri kuti akwaniritse cholinga chake.​—Yohane 3:16.

Onaninso Genesis 1:26-28; Yakobe 1:13 ndi 1 Petulo 5:6, 7.

 Kodi Nkhondo ndi Kuvutika Zidzathadi?

CHIFUKWA CHAKE ANTHU AMAFUNSA FUNSOLI: Anthu ambiri akupitirizabe kufa ndi nkhondo. Tonsefe timakhudzidwa mtima tikaona anthu akuvutika.

ZIMENE BAIBULO LIMAPHUNZITSA: Mulungu amalonjeza za nthawi imene adzakhazikitsa mtendere padziko lonse lapansi. Mu Ufumu wake, umene ndi boma la kumwamba, anthu “sadzaphunziranso nkhondo.” M’malo mwake, iwo “adzasula malupanga awo akhale zolimira.” (Yesaya 2:4) Mulungu adzathetseratu kupanda chilungamo ndi kuvutika. Baibulo limalonjeza kuti: “[Mulungu] adzapukuta msozi uliwonse m’maso mwawo, ndipo imfa sidzakhalaponso. Sipadzakhalanso kulira, kapena kubuula, ngakhale kupweteka. Zakalezo [monga kupanda chilungamo ndi kuvutika kwa masiku ano] zapita.”​—Chivumbulutso 21:3, 4.

Onaninso Salmo 37:10, 11; 46:9 ndi Mika 4:1-4.

Kodi Chimachitika N’chiyani Munthu Akamwalira?

CHIFUKWA CHAKE ANTHU AMAFUNSA FUNSOLI: Zipembedzo zambiri zimaphunzitsa kuti mzimu wa munthu umakhalabe ndi moyo munthuyo akafa. Anthu ena amakhulupirira kuti mizimu ya makolo amene anamwalira ingathandize kapena kuvulaza amoyo. Enanso amakhulupirira kuti Mulungu amalanga anthu oipa mwa kuwaponya kumoto wosatha.

ZIMENE BAIBULO LIMAPHUNZITSA: Munthu akafa, wafa basi. Satha kumva, kuona, kulankhula, kapena kuganiza. Lemba la Mlaliki 9:5 limati: “Akufa sadziwa kanthu bi.” Popeza akufa sadziwa kapena kumva chilichonse, sangathe kuvulaza kapena kuthandiza amoyo.​—Salmo 146:3, 4.

Onaninso Genesis 3:19 ndi Mlaliki 9:6, 10.

 Kodi Akufa Adzauka?

CHIFUKWA CHAKE ANTHU AMAFUNSA FUNSOLI: Palibe munthu amene amafuna kufa. Ndipo timafuna kusangalala ndi moyo pamodzi ndi anthu amene timawakonda. Mwachibadwa timafuna kuonananso ndi okondedwa athu amene anamwalira.

ZIMENE BAIBULO LIMAPHUNZITSA: Anthu ambiri amene anamwalira adzaukitsidwa. Yesu analonjeza kuti “onse ali m’manda a chikumbutso . . . adzatuluka.” (Yohane 5:28, 29) Mogwirizana ndi zimene Mulungu anafuna pachiyambi, anthu oukitsidwawo adzapatsidwa mwayi wokhala ndi moyo m’paradaiso padziko lapansi. (Luka 23:43) Panthawi imeneyo, anthu omvera adzakhala ndi moyo wathanzi ndiponso wosatha. Baibulo limati: “Olungama adzalandira dziko lapansi, nadzakhala momwemo kosatha.”​—Salmo 37:29.

Onaninso Yobu 14:14, 15; Luka 7:11-17 ndi Machitidwe 24:15.

Kodi Ndingatani Kuti Mulungu Aziyankha Mapemphero Anga?

CHIFUKWA CHAKE ANTHU AMAFUNSA FUNSOLI: M’zipembedzo zonse anthu amapemphera. Komabe ambiri amaona kuti mapemphero awo sayankhidwa.

ZIMENE BAIBULO LIMAPHUNZITSA: Yesu anatiphunzitsa kuti mapemphero athu asamakhale ongoloweza. Iye anati: “Popemphera, usanene zinthu mobwerezabwereza.” (Mateyo 6:7) Ngati tikufuna kuti Mulungu aziyankha mapemphero athu, tiyenera kupemphera m’njira imene iye amavomereza. Kuti tichite zimenezi, tiyenera kudziwa chifuniro cha Mulungu ndi kupemphera mogwirizana ndi chifunirocho. Lemba la 1 Yohane 5:14 limati: “Chilichonse chimene tingapemphe mogwirizana ndi chifuniro [cha Mulungu], amatimvera.”

Onaninso Salmo 65:2; Yohane 14:6, 14 ndi 1 Yohane 3:22.

Kodi Ndingatani Kuti Ndikhale ndi Moyo Wosangalala?

CHIFUKWA CHAKE ANTHU AMAFUNSA FUNSOLI: Anthu ambiri amakhulupirira kuti angakhale osangalala ngati ali ndi ndalama, ngati ali otchuka kapena okongola. Choncho, amafunafuna zinthu zimenezi komabe sakhala osangalala.

ZIMENE BAIBULO LIMAPHUNZITSA: Yesu anatchula njira yopezera chisangalalo pamene anati: “Osangalala ali iwo amene amazindikira zosowa zawo zauzimu.” (Mateyo 5:3) Kuti munthu akhaledi ndi moyo wosangalala, afunika kuthetsa njala yake yauzimu yofuna kudziwa choonadi cha Mulungu ndi cholinga chake potilenga. Chimenechi ndicho chosowa chathu chachikulu. Choonadi chimenecho chimapezeka m’Baibulo. Kudziwa choonadi chimenechi kungatithandize kuzindikira zinthu zofunika ndi zosafunika. Tikamatsogoleredwa ndi choonadi cha m’Baibulo pa zosankha ndi zochita zathu, timakhala ndi moyo wosangalala.​—Luka 11:28.

Onaninso Miyambo 3:5, 6, 13-18 ndi 1 Timoteyo 6:9, 10.

 Apa tangoonapo mafunso 6 okha amene Baibulo limayankha. Kodi mukufuna kudziwa zambiri kuposa pamenepa? Ngati nanunso ‘mumazindikira zosowa zanu zauzimu,’ ndiye kuti muli ndi mafunso ambiri. Mwina mungafunenso kudziwa mayankho a mafunso monga akuti: ‘Ngati Mulungu amatiganizira, n’chifukwa chiyani walola zinthu zoipa ndi mavuto kupitirizabe? Kodi ndingatani kuti banja langa likhale losangalala?’ Baibulo limayankha bwino kwambiri mafunso amenewa ndi enanso ambiri.

Koma anthu ambiri masiku ano safuna kuwerenga Baibulo. Amaona kuti ndi buku lalikulu kwambiri ndiponso lovuta kumva. Kodi kapena mungafune thandizo kuti mupeze mayankho m’Baibulo? Mboni za Yehova zili ndi njira ziwiri zimene zingakuthandizireni.

Njira yoyamba ndi buku la Zimene Baibulo Limaphunzitsa. Bukuli linapangidwa kuti lithandize anthu otanganidwa kupeza mayankho omveka bwino a m’Baibulo. Njira yachiwiri ndi yophunzira Baibulo panyumba panu kwaulere. Wa Mboni za Yehova amene amakhala kufupi ndi kwanu ndiponso wodziwa kuphunzitsa Baibulo, angamabwere ku nyumba kwanu kapena malo ena amene mungasankhe, kuti muziphunzira Baibulo kwa nthawi yochepa mlungu uliwonse. Anthu ambirimbiri padziko lonse athandizidwa kwambiri mwa njira imeneyi. Ambiri afika ponena kuti: “Ndapeza choonadi!”

Palibenso chinthu chofunika kwambiri kuposa kudziwa choonadi cha m’Baibulo, chifukwa chimatimasula ku miyambo yosiyanasiyana ndi mantha osayenera. Chimatipatsa chiyembekezo, cholinga pamoyo ndiponso chimwemwe. Yesu anati: “Mudzadziwa choonadi, ndipo choonadi chidzakumasulani.”​—Yohane 8:32.