Kodi zamoyo zinachita kulengedwa kapena zinangokhalapo zokha? Anthu ambiri ali ndi maganizo osiyanasiyana pa nkhaniyi. Koma kudziwa zoona zake n’kofunika kwambiri. Kabukuka kamayankha mafunso ngati awa:

  • Kodi dzikoli linapangidwa kuti muzikhala zamoyo?

  • Kodi tingaphunzire chiyani pa zinthu za m’chilengedwe?

  • Kodi zimene anthu amaphunzitsa zoti zamoyo zinachita kusintha kuchokera ku zinthu zina zili ndi umboni wake?

  • Kodi sayansi imasonyeza kuti nkhani ya m’Baibulo yokhudza kulenga zinthu si yoona?

  • Kodi zimene mumakhulupirira pa nkhaniyi zimakhudza bwanji moyo wanu?