Pitani ku nkhani yake

Pitani ku menyu yachiwiri

Pitani ku mitu ya nkhani

Mboni za Yehova

Chichewa

Kodi Ndani Akuchita Chifuniro cha Yehova Masiku Ano?

 Mutu 7

Kodi Misonkhano Yathu Imachitika Bwanji?

Kodi Misonkhano Yathu Imachitika Bwanji?

New Zealand

Japan

Uganda

Lithuania

Pamisonkhano ya Akhristu oyambirira, ankaimba nyimbo, kupemphera, kuwerenga komanso kukambirana Malemba, ndipo sipankachitika miyambo iliyonse yamakolo. (1 Akorinto 14:26) Masiku ano, misonkhano ya Mboni za Yehova imachitikanso chimodzimodzi.

Timalandira malangizo othandiza ochokera m’Baibulo. Pa mapeto pa mlungu, mpingo uliwonse umasonkhana kuti umvetsere nkhani ya m’Baibulo ya mphindi 30. Nkhaniyi imatithandiza kudziwa mmene tingagwiritsire ntchito Malemba pa moyo wathu komanso imatithandiza kuona mmene malembawo akugwirizanira ndi zimene zikuchitika panopa. Pa nthawiyi, tonse timayenera kutsegula Baibulo lathu n’kumawerenga limodzi ndi munthu amene akukamba nkhaniyo. Nkhaniyo ikatha, timakhala ndi Phunziro la “Nsanja ya Olonda,” lomwe limachitika kwa ola limodzi. Phunziro limeneli limachitika pogwiritsira ntchito magazini yophunzirira ya Nsanja ya Olonda, ndipo aliyense mu mpingo amakhala ndi mwayi wopereka ndemanga zake. Phunziro limeneli limatithandiza kugwiritsa ntchito malangizo a m’Baibulo pa moyo wathu. Mlungu uliwonse mipingo yonse ya Mboni za Yehova yoposa 110,000 padziko lonse, imaphunzira nkhani yofanana.

Timathandizidwa kuti tikhale aphunzitsi aluso. Tsiku lina mlungu womwewo timachita misonkhano itatu. Msonkhano woyamba ndi Phunziro la Baibulo la Mpingo, lomwe limakhala la mphindi 30. Msonkhano umenewu umachitika pokambirana mafunso ndi mayankho ndipo umatithandiza kumvetsa bwino mfundo za m’Malemba komanso maulosi a m’Baibulo. Msonkhano wachiwiri ndi Sukulu ya Utumiki wa Mulungu, ya mphindi 30. Sukuluyi imayamba ndi kukambirana mfundo za m’Baibulo zochokera m’gawo lina limene anthu onse mumpingo amakhala atawerenga kale. Kenako, anthu amene analembetsa m’sukuluyi amakamba nkhani zawo zazifupi. Munthu amene akutsogolera sukulu amaona zimene wokamba nkhani akufunika kukonza n’cholinga chomuthandiza kuti aziwerenga bwino komanso kuphunzitsa mwaluso. (1 Timoteyo 4:13) Pamapeto pake timakhala ndi Msonkhano wa Utumiki, womwe umakhala wa mphindi 30. Pamsonkhanowu pamakhala nkhani, zitsanzo komanso kufunsa anthu mafunso, zomwe zimatithandiza kukhala aluso pophunzitsa ena Baibulo.

Mukadzabwera kumisonkhano yathu, sitikukayikira kuti mudzasangalala ndi maphunziro apamwamba ochokera m’Baibulo.​—Yesaya 54:13.

  • Kodi mungayembekezere kudzaphunzira zotani kumisonkhano ya Mboni za Yehova?

  • Pa misonkhano yathu ya mlungu ndi mlungu, kodi ndi msonkhano uti umene mungakonde kudzapezekapo?