Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

 Mutu 28

Kodi Pamalo Athu a pa Intaneti Pali Zinthu Zotani?

Kodi Pamalo Athu a pa Intaneti Pali Zinthu Zotani?

France

Poland

Russia

Yesu anauza ophunzira ake kuti: “Onetsani kuwala kwanu pamaso pa anthu, kuti aone ntchito zanu zabwino ndi kuti alemekeze Atate wanu wakumwamba.” (Mateyu 5:16) Kuti tikwanitse kuchita zimenezi, tikugwiritsa ntchito zinthu zamakono monga Intaneti. Pamalo athu a pa Intaneti a jw.org, pamapezeka nkhani zofotokoza zimene ife a Mboni za Yehova timakhulupirira komanso zimene timachita. Kodi pamalo athu amenewa palinso zinthu zotani?

Pamapezeka mayankho a m’Baibulo a mafunso amene anthu amakonda kufunsa. Mungapezepo mayankho a mafunso ofunika kwambiri amene anthu amakonda kufunsa. Mwachitsanzo, kapepala kakuti Kodi Mukufuna Kudziwa Choonadi?, komwe kamapezeka pa Intaneti m’zinenero zoposa 400, kamayankha mafunso 6 ofunika kwambiri. Mungapezeponso Baibulo la Dziko Latsopano m’zinenero zoposa 100 komanso mabuku angapo othandiza pophunzira Baibulo monga buku lakuti, Kodi Baibulo Limaphunzitsa Chiyani Kwenikweni? Ndiponso mungapezepo magazini atsopano a Nsanja ya Olonda ndi Galamukani! Mungawerenge kapena kumvetsera pa Intaneti mabuku ndi magazini amenewa. Mungathenso kuzichotsa pa Intaneti n’kuziika pa kompyuta kapena pachipangizo china kuti muzimvetsera kapena kuwerenga. Mukhozanso kusindikiza masamba ena ochepa a buku kapena magazini imene mwapeza pa Intaneti n’cholinga choti mukapatse munthu wina wachidwi m’chinenero chake. Palinso mavidiyo a m’zinenero zamanja zambiri. Komanso mungachotse masewero ndi nyimbo zabwino zomwe zili pa Intaneti n’kuziika poti mukhoza kumamvetsera mukapeza nthawi.

Pali nkhani zofotokoza bwino mmene mpingo wa Mboni za Yehova ulili. Chinanso chomwe chimapezeka pamalo athu a pa Intaneti ndi nkhani zaposachedwapa zokhudza Mboni za Yehova ndi mavidiyo osonyeza zinthu zokhudza ntchito yapadziko lonse komanso mmene timathandizirana pakagwa tsoka. Mungapezenso masiku amene misonkhano ikuluikulu idzachitike, komanso maadiresi kapena manambala a foni a maofesi osiyanasiyana a Mboni za Yehova.

Chifukwa cha zinthu ngati zimenezi tikuonetsa kuwala kwa choonadi ngakhale kumadera akutali kwambiri. Anthu padziko lonse lapansi ngakhale kumadera akutali ngati ku Antarctica, akuphunzira choonadi cha m’Baibulo. Tikupemphera kuti “mawu a Yehova apitirize kufalikira mofulumira” padziko lonse lapansi n’cholinga choti Mulungu alemekezedwe.​—2 Atesalonika 3:1.

  • Kodi webusaiti yathu ya jw.org ikuthandiza bwanji anthu kuphunzira choonadi cha m’Baibulo?

  • Kodi mungakonde kufufuza zinthu zotani pawebusaiti yathu?