Dominican Republic

Japan

Haiti

Pakachitika tsoka, nthawi yomweyo a Mboni za Yehova amayamba kukonza zoti athandize abale awo amene akhudzidwa. Zimenezi zimasonyeza kuti tili ndi chikondi chenicheni. ( Yohane 13:34, 35; 1 Yohane 3:17, 18) Koma kodi timathandiza abale athu m’njira zotani?

Timapereka ndalama. Ku Yudeya kutagwa njala yaikulu, Akhristu oyambirira a ku Antiokeya anatumiza ndalama zoti athandizire abale awo auzimu. (Machitidwe 11:27-30) Ifenso tikamva kuti abale athu m’mayiko ena ali pa mavuto, timapereka zopereka kudzera m’mipingo yathu n’cholinga choti zikathandizire pogula zinthu zofunikira kwa anthu amene akuvutikawo.​—2 Akorinto 8:13-15.

Timathandiza pogwira ntchito zina zofunika. Akulu amene ali kudera kumene kwachitika tsoka, amafufuza aliyense wa mumpingo mwawo kuti atsimikizire kuti alipo komanso kuti ndi wotetezeka. Komiti yopereka chithandizo ingayang’anire ntchito yopereka chakudya, madzi abwino akumwa, zovala, pogona komanso thandizo la mankhwala. A Mboni za Yehova amene amadziwa ntchito zosiyanasiyana amadzipereka pogwiritsa ntchito ndalama zawo kuti akathandize pa ntchito yokonza nyumba za abale awo komanso Nyumba za Ufumu zomwe zawonongeka. Pakachitika tsoka, sizimavuta kupeza thandizo kapena anthu amene angadzipereke kuthandiza anthu omwe ali m’mavuto. Zili choncho chifukwa nthawi zambiri timagwirira ntchito limodzi komanso ndife gulu logwirizana. Ngakhale kuti timathandiza “abale ndi alongo athu m’chikhulupiriro,” timathandizanso wina aliyense mosaganizira za chipembedzo chake.​—Agalatiya 6:10.

Timalimbikitsana pogwiritsa ntchito Malemba. Anthu amene akhudzidwa ndi tsoka amafunika kulimbikitsidwa kwambiri. Pa nthawi ngati imeneyi timalimbikitsidwa ndi Yehova yemwe ndi “Mulungu amene amatitonthoza m’njira iliyonse.” (2 Akorinto 1:3, 4) Anthu amene akuvutika, timawauza malonjezo amene ali m’Baibulo ndipo timawalimbikitsa powauza kuti posachedwapa Ufumu wa Mulungu uthetsa mavuto onsewa.​—Chivumbulutso 21:4.

  • N’chifukwa chiyani a Mboni amathandiza mwamsanga pakachitika tsoka?

  • Kodi anthu amene akhudzidwa ndi tsoka tingawauze uthenga wotonthoza uti wa m’Baibulo?