Pitani ku nkhani yake

Pitani ku menyu yachiwiri

Pitani ku mitu ya nkhani

Mboni za Yehova

Chichewa

Kodi Ndani Akuchita Chifuniro cha Yehova Masiku Ano?

Kodi Mukufuna Kuchita Zimene Yehova Amafuna?

Kodi Mukufuna Kuchita Zimene Yehova Amafuna?

Tikukuthokozani chifukwa chopatula nthawi yanu n’kuwerenga kabuku kano n’cholinga choti mutidziwe bwino ife a Mboni za Yehova, komanso kuti mudziwe mmene timachitira zinthu, ndiponso mmene gulu lathu limayendera. Tikukhulupirira kuti kabukuka kakuthandizani kuzindikira kuti ifeyo ndi anthu amene akuchita chifuniro cha Yehova masiku ano. Choncho tikukulimbikitsani kuti mupitirize kuphunzira zambiri zokhudza Mulungu, mupitirize kuuza achibale anu ndiponso anzanu onse zimene mukuphunzirazo, komanso mupitirize kusonkhana nafe nthawi zonse pamisonkhano yathu yachikhristu.—Aheberi 10:23-25.

Kupitiriza kuphunzira za Yehova kukuthandizani kuona kuti iye amakukondani kwambiri. Zimenezi zidzakulimbikitsani kuti muzichita zonse zimene mungathe pofuna kusonyeza kuti nanunso mumamukonda. (1 Yohane 4:8-10, 19) Koma kodi mungatani kuti muzisonyeza kuti mumakonda Mulungu pa moyo wanu watsiku ndi tsiku? N’chifukwa chiyani kutsatira mfundo zake zamakhalidwe abwino n’kofunika kwambiri pa moyo wanu? Ndipo n’chiyani chingakuthandizeni kuti mukhale ndi mtima wofuna kuchita chifuniro cha Mulungu pamodzi ndi ife? Munthu amene akukuphunzitsani Baibulo adzasangalala kwambiri kukuthandizani kufufuza mayankho a mafunso amenewa n’cholinga choti inuyo pamodzi ndi banja lanu ‘mupitirize kuchita zinthu zimene zingachititse Mulungu kukukondani, komanso kuti mudzalandire moyo wosatha.’​—Yuda 21.

Tikukulimbikitsani kuti mupitirizebe kupita patsogolo mwauzimu pophunzira mfundo zina za choonadi. Gwiritsani ntchito buku lotsatirali pochita zimenezi “Khalanibe M’chikondi cha Mulungu”