Pitani ku nkhani yake

Pitani ku menyu yachiwiri

Pitani ku mitu ya nkhani

Mboni za Yehova

Chichewa

Bwererani kwa Yehova

 GAWO 1

“Nkhosa Zosochera Ndidzazifunafuna”

“Nkhosa Zosochera Ndidzazifunafuna”

Tiyerekeze kuti nkhosa zikudya ndipo ina ikutsatira msipu wobiriwira mpaka yachoka pakati pa zinzake. Ndiyeno ili yokhayokha ndipo mdima ukuyamba. M’derali muli zilombo zoopsa ndipo palibe woiteteza. Kenako ikumva mawu a m’busa wake. Iye akuithamangira, n’kuinyamula ndipo akuifunditsa malaya ake kenako akupita nayo kunyumba.

BAIBULO limasonyeza mobwerezabwereza kuti Yehova ali ngati m’busa ameneyu. Iye amatiuza kuti: “Inetu ndidzafunafuna nkhosa zanga ndi kuzisamalira.”—Ezekieli 34:11, 12.

“Nkhosa Zimene Ndikuzisamalira”

Kodi nkhosa za Yehova ndi ndani? Ndi anthu amene amamukonda ndiponso kumulambira. Paja Baibulo limatiuza kuti: “Bwerani timuweramire ndi kumupembedza. Tiyeni tigwade pamaso pa Yehova amene ndiye Wotipanga. Pakuti iye ndi Mulungu wathu ndipo ife ndife anthu ake. Iye amatisamalira ngati nkhosa zimene akuweta.” (Salimo 95:6, 7) Atumiki a Yehova ali ngati nkhosa zimene zimafunitsitsa kutsatira m’busa wawo. Komabe nthawi zina amalakwitsa zinthu ndipo amakhala ngati ‘nkhosa zobalalika,’ “zotayika” ndiponso “zosochera.” (Ezekieli 34:12; Mateyu 15:24; 1 Petulo 2:25) Ngakhale zili choncho, Yehova amadziwa kuti nkhosazo zikhoza kubwerera.

 Kodi inuyo mumaonabe kuti Yehova ndi M’busa wanu? Tiyeni tikambirane zinthu zitatu zimene Yehova amachita posonyeza kuti ndi M’busa wathu.

Amatidyetsa. Paja Yehova ananena kuti: ‘Nkhosazo ndidzazidyetsera m’malo a msipu wabwino ndipo zizidzagona pansi m’malo abwino kwambiri.’ (Ezekieli 34:14) Yehova amatipatsa zinthu zambiri zimene zimatilimbikitsa ndiponso kutithandiza kukhala naye pa ubwenzi. Mwina inuyo mukukumbukira vidiyo, nkhani ya m’mabuku athu kapena nkhani imene inakambidwa pa msonkhano yomwe inakhala ngati ikuyankha pemphero lanu. Kodi umenewu si umboni woti Yehova amakukondani?

Amatiteteza ndi kutilimbikitsa. Yehova analonjeza kuti: “[Nkhosa] zomwazika ndidzazibweza. Yothyoka mwendo ndidzaimanga mwendo wothyokawo. Yodwala ndidzailimbitsa.” (Ezekieli 34:16) Yehova amalimbikitsa anthu amene afooka kapena kupanikizika ndi nkhawa. Iye amamanga mabala a atumiki ake amene avulazidwa mwina ndi Akhristu anzawo. Amabweza anthu amene asochera ndiponso kulimbikitsa amene akuvutika maganizo.

Amafunitsitsa kutisamalira. Yehova ananena kuti: “Ndidzapulumutsa nkhosazo kuchokera m’malo onse kumene zinabalalikira.” Ananenanso kuti: “Nkhosa zosochera ndidzazifunafuna.” (Ezekieli 34:12, 16) Yehova saona kuti nkhosa yosochera ndi yokanika. Iye amazindikira ina ikasowa ndipo amayamba kuifufuza. Akaipeza amasangalala kwambiri. (Mateyu 18:12-14) Paja amanena kuti atumiki ake onse ali ngati nkhosa zimene akuzisamalira. (Ezekieli 34:31) Dziwani kuti inuyo ndi mmodzi wa nkhosazo.

Yehova saona kuti nkhosa yosochera ndi yokanika. Iye amasangalala akapeza nkhosayo

‘Mubwezeretse Zonse Kuti Zikhale Ngati Kale’

Yehova amafuna kuti mubwerere kwa iye kuti mukhale osangalala. Paja amalonjeza nkhosa zake kuti: “Kudzagwa mvula yambiri yamadalitso.” (Ezekieli 34:26) N’kutheka kuti inuyo mwaonapo Yehova akukuthandizani kukhala osangalala.

Muzikumbukira zimene zinachitika mutayamba kuphunzira za Yehova. Mwachitsanzo, kodi munamva bwanji mutadziwa dzina la Mulungu ndiponso cholinga chake chokhudza anthu? Kapena kodi mukukumbukira nthawi yomwe munkasangalala pamodzi ndi abale ndi alongo pa misonkhano yathu? Nthawi yomwe munkalalikira, kodi munkamva bwanji mukathandiza munthu kuyamba kuphunzira za Yehova?

Mukhoza kuyambanso kukhala osangalala ngati kale. Paja atumiki akale a Yehova anati: “Inu Yehova, tibwezeni kwa inu ndipo ife tibwerera mwamsanga. Mubwezeretse zinthu zonse kuti zikhale ngati mmene zinalili kale.” (Maliro 5:21) Yehova anayankha pempheroli ndipo iwo anabwerera kwa iye kuti ayambenso kumutumikira mosangalala. (Nehemiya 8:17) Yehova angachitenso chimodzimodzi ndi inu.

Koma kunena zoona kubwerera kwa Yehova si kophweka. Choncho tiyeni tikambirane mavuto amene mungakumane nawo pobwerera ndiponso mmene mungawathetsere.