Mlongo wina dzina lake June anati: “Ine ndi mwamuna wanga tinasiyana titakhala m’banja zaka 25. Ana anga anasiyanso kutumikira Yehova. Ndiyeno ndinayamba kudwaladwala. Izi zinachititsa kuti ndiyambenso matenda a maganizo. Ndinkaona kuti moyo wanga wasokonekera kwambiri moti sindingapirire. Choncho ndinasiya kupita ku misonkhano.”

ALIYENSE, ngakhale anthu a Mulungu, amakhala ndi nkhawa. Paja wamasalimo analemba kuti: ‘Malingaliro osautsa anandichulukira mumtima mwanga.’ (Salimo 94:19) Nayenso Yesu ananena kuti pa nthawi ya mapeto anthu adzavutika kutumikira Yehova chifukwa cha “nkhawa za moyo.” (Luka 21:34) Kodi inunso muli ndi nkhawa chifukwa cha mavuto azachuma, mavuto a m’banja kapena matenda? Ngati zili choncho, kodi Yehova angakuthandizeni bwanji?

“Mphamvu Yoposa Yachibadwa”

Sitingathetse nkhawa patokha. Mtumwi Paulo analemba kuti: “Timapanikizidwa mwamtundu uliwonse, koma osati kupsinjidwa moti n’kulephera kusuntha. Timathedwa nzeru, koma osati mochita kusoweratu pothawira. . . . Timagwetsedwa pansi, koma sitiwonongedwa.” Kodi n’chiyani chimatithandiza kupirira? Paulo ananena kuti ndi “mphamvu yoposa yachibadwa” yomwe imachokera kwa Yehova Mulungu.—2 Akorinto 4:7-9.

Kodi inuyo mukukumbukira nthawi imene “mphamvu yoposa yachibadwa” inakuthandizani? Mwachitsanzo, mwina nkhani ina inakulimbikitsani ndi kukukuthandizani kukonda kwambiri Yehova. Mwinanso chikhulupiriro chanu chinalimba kwambiri chifukwa chophunzitsa ena za Paradaiso. Misonkhano ndiponso kulalikira zimatipatsa mtendere wa mumtima ndiponso mphamvu yopirira nkhawa za moyo. Izi zimatithandiza kutumikira Yehova mosangalala.

“Talawani Ndipo Muona Kuti Yehova Ndi Wabwino”

Yehova amatiuza kuti tizifunafuna Ufumu choyamba ndiponso kuti nthawi zonse tizichita zinthu zokhudza kulambira. (Mateyu 6:33; Luka 13:24) Koma n’kutheka kuti pali zinthu zambiri zimene zimakupanikizani. Mwina mumatsutsidwa, mukudwala kapena muli ndi mavuto a m’banja. Mwinanso mumapanikizika ndi ntchito moti mumasowa nthawi yosonkhana kapena kulalikira. Kodi izi zimakuchititsani kuganiza kuti zimene Yehova amafuna kuti muzichita n’zosatheka?

Dziwani kuti Yehova amakumvetsani. Iye sangatipemphe kuchita zimene sitingakwanitse. Amadziwanso kuti pamatenga nthawi kuti maganizo a munthu amene wapanikizika akhale m’malo.—Salimo 103:13, 14.

Zimene zinachitikira Eliya zikhoza kutiphunzitsa zambiri pa nkhaniyi. Eliya atamva zoti akufuna kuphedwa, anasowa mtendere ndipo anathawira kuchipululu. Kodi Yehova anamukalipira n’kumuuza kuti abwerere ku ntchito yake? Ayi, sanatero. M’malomwake, anatumiza mngelo kawiri kuti akamudzutse n’kumupatsa chakudya. Koma panapita masiku 40 maganizo a Eliya asanakhalebe m’malo. Kodi Yehova anachitanso chiyani pofuna kumuthandiza? Choyamba, anamusonyeza kuti ali ndi mphamvu yomupulumutsa. Chachiwiri, anamulimbikitsa ndi “mawu achifatse apansipansi.”  Pomaliza, Yehova anamuthandiza kudziwa kuti pali anthu ena ambirimbiri amene akutumikira Mulungu mokhulupirika. Zitatero, Eliya anapeza mphamvu n’kuyambanso kutumikira mwakhama. (1 Mafumu 19:1-19) Kodi tikuphunzira chiyani pa nkhaniyi? Eliya atapanikizika chifukwa cha mantha, Yehova anamuthandiza moleza mtima ndiponso mokoma mtima. Mulungu sanasinthe. Inunso akhoza kukuthandizani ngati mmene anachitira ndi Eliya.

Si bwino kuyerekezera zimene munkachita kale ndi zimene mungakwanitse panopa. Tingayerekezere nkhaniyi ndi zimene katswiri wothamanga amachita. Ngati wasiya kuthamanga kwa miyezi ingapo kapena zaka, amakhala wosamala akamayambiranso. Amayamba pang’onopang’ono kuti apezenso mphamvu kenako n’kufika pamene anali poyamba. Kutumikira Mulungu kulinso ngati mpikisano wothamanga ndipo aliyense ayenera kukhala ndi zolinga. (1 Akorinto 9:24-27) Koma ndi bwino kukhala ndi zolinga zimene inuyo mungazikwanitse. Mwachitsanzo, mungakhale ndi cholinga choti mupezeke pa misonkhano yampingo. Ndiyeno mungapemphe Yehova kuti akuthandizeni kukwaniritsa cholingachi. Mukayamba kupezanso mphamvu mudzakhala ngati ‘mwalawa n’kuona kuti Yehova ndi wabwino.’ (Salimo 34:8) Yehova amaona kuti chilichonse chimene mumachita chifukwa chomukonda, kaya chichepe bwanji, ndi chamtengo wapatali.—Luka 21:1-4.

Yehova sangatipemphe kuchita zimene sitingakwanitse

“Msonkhanowo Unandilimbikitsa Kwambiri”

Kodi Yehova anathandiza bwanji mlongo amene tamutchula kumayambiriro uja kuti abwerere? Mlongoyu anati: “Ndinkapemphera kwambiri kwa Yehova kuti andithandize. Kenako mpongozi wanga anandiuza za msonkhano wadera wa m’tauni imene ndimakhala. Ndinaganiza zopita ku msonkhanowu tsiku limodzi. Nditapita ndinasangalala kwambiri kukhalanso limodzi ndi anthu a Yehova. Msonkhanowo unandilimbikitsa kwambiri. Panopa ndikutumikiranso Yehova mosangalala. Tsopano ndimadziwa kuti sindingapirire mavuto pandekha. Ndikuyamikira kwambiri kuti mpata wobwerera kwa Yehova unalipobe.”