Pitani ku nkhani yake

Pitani ku menyu yachiwiri

Pitani ku mitu ya nkhani

Mboni za Yehova

Chichewa

Buku Lapachaka la Mboni za Yehova la 2017

Fiji

 NTCHITO YOLALIKIRA NDI KUPHUNZITSA PADZIKO LONSE

Oceania

Oceania
  • MAYIKO 29

  • CHIWERENGERO CHA ANTHU 41,051,379

  • OFALITSA 98,574

  • MAPHUNZIRO A BAIBULO 67,609

Patatha Zaka 9, Aphunzitsi Ake Anabwera ku Chikumbutso

Kamtsikana kena ka ku Australia, dzina lake Olivia, kankaphunzira kusukulu yamkaka. Tsiku lina kamtsikanaka kanaitanira aphunzitsi ake aakazi ku Chikumbutso, koma sanabwere. Komabe chaka chilichonse kamtsikanaka kankaitanira aphunzitsiwo ku Chikumbutso ndipo anachita zimenezi kwa zaka 8. Kenako mu 2016, aphunzitsiwo  anakaimbira foni n’kukauza kuti apita ku Chikumbutso. Iwo anachita zimenezi chifukwa anaona kuti Olivia amawaganizira kwambiri. Choncho anabweradi limodzi ndi amuna awo. Amuna awowo ananena kuti akuikumbukira Nyumba ya Ufumuyo chifukwa pa nthawi yomwe inkamangidwa n’kuti iwowo akugwira ntchito kukhonsolo ya m’tauniyo. Anauzanso abale kuti ankachita chidwi kwambiri chifukwa anthu amene ankamanga Nyumba ya Ufumuyo ankagwira ntchito mwadongosolo. Iwo ndi akazi awo anasangalala kwambiri ndi mwambo wa Chikumbutso ndipo mwambowo utatha sanachoke msanga.

Australia: Patatha zaka 9 khama la Olivia linabala zipatso

Anawerenga Buku Maulendo Atatu

A Jacintu ndi akazi awo amakhala ku Timor-Leste ndipo iwo ndi achibale awo ndi Akatolika. Koma tsiku lina anadabwa kwambiri atamva kuti mwana wa achimwene awo wayamba Mboni. A Jacintu anaganiza zowerenga buku la Kodi Baibulo Limaphunzitsa Chiyani Kwenikweni? n’cholinga choti amusonyeza kuti zimene a Mboni amaphunzitsa n’zabodza. Koma atalimaliza, anauza akazi awo kuti: “Ndawerenga bukuli, koma ndi labwino kwambiri.”

Akazi awowo anati: “Mwaliwerenga mothamanga. Muliwerengenso mwachifatse.”

A Jacintu anachitadi zimenezi, ndipo anauzanso akazi awo kuti: “Ndikuonabe kuti bukuli ndi labwino kwambiri. Mfundo zake zonse n’zochokera m’Baibulo. Ngakhalenso zimene likunena zokhudza kulambira mizimu ya makolo n’zochokera m’Baibulo.”

Koma akazi awowo anati: “Muliwerengenso kachitatu, ulendo uno muzidula mizere m’ndime iliyonse. Musathamange. Muona kuti mfundo zake ndi zabodza.”

 A Jacintu anaphunziradi bukulo mwachifatse ndipo ankadula mizere m’ndime iliyonse. Atamaliza anauza akazi awo kuti: “Ayi ndithu, zimene bukuli likunena ndi zoona. Mwanayutu sanalakwitse kukhala wa Mboni.” Panopa a Jacintu akuphunzira Baibulo ndi a Mboni za Yehova.

Mwana Wawo Anawathandiza

Mlongo wina wa ku Guam, yemwenso ndi mpainiya analalikira mayi wa ku Pohnpei ndipo anamusonyeza vidiyo yakuti, N’chifukwa Chiyani Tiyenera Kuphunzira Baibulo? Mlongoyu analonjeza kuti adzapitakonso. Anapitakodi maulendo angapo koma sankamupeza mayiyo. Tsiku lina atafika anapeza mwana wamkazi wa mayiyo ndipo anamuonetsa vidiyo ya Kalebe. Mwanayo anasangalala kwambiri ndi vidiyoyo. Ndiyeno mlongoyo atapitanso ulendo wina, anapeza mayi aja ali pakhomo ndipo anamvetsera mwachidwi uthenga wa m’Baibulo. Mwana uja anali atawauza kuti akufuna kuti mayi akewo ndi iyeyo azipita kutchalitchi cha mayi  amene anamuonetsa vidiyo. Zikuoneka kuti izi n’zimene zinachititsa kuti mayiwo amvetsere mwachidwi. Choncho mlongo uja anamusonyeza mayiyo mmene timaphunzirira Baibulo ndipo anavomera kuti aziphunzira.

“Ngati Nkhosa Zopanda M’busa”

A Terence ndi woyang’anira dera ndipo akazi awo ndi a Stella. Anthuwa amakhala ku Papua New Guinea ndipo nthawi ina anapita kudera la Inakor, komwe kulibe ofalitsa. A Terence anati: “M’mawa tisanadzuke, tinangomva kugogoda. Titatuluka tinaona kuti kwabwera anthu ambiri ndipo tinayamba kuwalalikira, kuyambira 6 koloko mpaka 12 koloko. Kenako tinasiya kaye n’kupita kukasamba  ndipo titamaliza, tinapeza anthu enanso ambiri akutidikirira. Choncho tinayambanso kuwalalikira, kuyambira 2 koloko mpaka pakati pa usiku.” Tsiku lotsatira banjali linaganiza zochoka m’mawa kwambiri n’kupita kudera lina. Koma anthu atabwera n’kuona kuti achoka, anawatsatira kumene anapitako. A Terence anati: “Atatipeza, tinayamba kuwalalikira mpaka masana. Titabwerera kumene tinafikira kuja, tinapeza anthu enanso akutidikirira. Zoterezi zinkachitika masiku onse amene tinakhala kuderali. Anthuwa anali ‘ngati nkhosa zopanda m’busa.’”Mat. 9:36.

Anthu a ku Papua New Guinea akusangalala ataona kuti a Terence ndi akazi awo akubwera

Dokotala Anapatsidwa Mphatso

Mlongo Agnès ndi mpainiya ndipo amakhala ku New Caledonia. Tsiku lina anapita kuchipatala chifukwa ankamva kupweteka mkono. Pamene dokotala ankathandiza mlongoyu, anafotokoza kuti waona anthu ambiri akuvutika ndipo amakayikira ngati Mulungu alidi wachikondi. Mlongoyu anapemphera chamumtima ndipo anathokoza Yehova pomupatsa mwayi woti auze mayiyo zoona zokhudza nkhaniyi. Kenako anaonetsa dokotalayo kapepala kakuti, Kodi Mavuto Amene Tikukumana Nawowa Adzathadi? Anamuwerengeranso lemba la Chivumbulutso 21:3, 4.

Dokotalayo anati: “Sindikudziwa ngati lemba lomwe mwawerengali lachokeradi m’Baibulo. Chifukwa ine ndili ndi Kabaibulo kongokhala ndi Uthenga Wabwino basi.” Dokotalayu atadziwa kuti Mlongo Agnès ndi wa Mboni ananena kuti anakumanapo ndi a Mboni za Yehova kwawo ku Chile.

Mlongoyu atamva zimenezi anakumbukira kuti lipoti la ku Chile linaulutsidwa pa JW Broadcasting. Choncho pamene ankapitanso kuchipalatako, anatenga tabuleti kuti akamuonetse dokotalayo lipotilo. Dokotalayo anasangalala kwambiri ataona Beteli ya ku Chile komanso Malo a Msonkhano. Kenako Mlongo Agnès anati: “Ndakubweretseraninso  Baibulo lonse kuti muwerenge lemba la Chivumbulutso 21:3, 4 lomwe ndinakuwerengerani mlungu watha uja.” Dokotalayo atamva zimenezi anaimirira pampando pomwe anakhala n’kukumbatira mlongoyo ndipo anati: “Zikomo kwambiri chifukwa cha mphatso ziwirizi. Mwandionetsa vidiyo komanso mwandibweretsera Baibulo.”

New Caledonia: Dokotala anasangalala kwambiri

Pa ulendo wotsatira, Mlongo Agnès anapititsira dokotalayu buku lakuti, Kodi Baibulo Limaphunzitsa Chiyani Kwenikweni? Komanso anamufotokozera zimene zinayambitsa mavuto. Dokotalayo anati akupita kwawo ku Chile kutchuti ndipo atenga bukulo kuti akaliwerenge.