Pitani ku nkhani yake

Pitani ku menyu yachiwiri

Pitani ku mitu ya nkhani

Mboni za Yehova

Chichewa

Buku Lapachaka la Mboni za Yehova la 2017

Azerbaijan

 NTCHITO YOLALIKIRA NDI KUPHUNZITSA PADZIKO LONSE

Europe

Europe
  • MAYIKO 47

  • CHIWERENGERO CHA ANTHU 744,482,011

  • OFALITSA 1,611,290

  • MAPHUNZIRO A BAIBULO 834,121

Anayankha Modekha

M’dziko la Georgia, bambo wina anafika pamalo ena omwe abale ankalalikira pogwiritsa ntchito kashelefu kamatayala. Bamboyo anayamba kuyankhula mokalipa kuti: “Sindingakuloleni kumalalikira pano! Kodi simukudziwa kuti dziko la Georgia ndi la chipembedzo cha Orthodox?” M’bale amene anaima pafupi ndi kashelefuko, anamufunsa modekha ngati anayamba wawerengapo mabuku athu. Bamboyo anayankha kuti: “Ayi, sindinawerengepo.”  Kenako m’baleyo anamuuza kuti angachite bwino atawerenga mabuku athu. Zimene m’baleyu anachitazi zinathandiza kuti mtima wa munthuyo ukhale pansi moti anatenga magazini. Patatha masiku angapo, bamboyu anabweranso ndipo anapepesa chifukwa cha zimene anachita zija. Ananena kuti magazini imene anatenga ija anawerengera mayi ake omwe ndi wosaona. Mfundo za m’magaziniyo zinamufika iyeyo pamtima komanso mayi akewo moti ankafuna atapezanso magazini ena. Panopa bamboyu amapita pamalo amene abalewa amalalikira kuti akatenge magazini atsopano.

Anapeza Njira Yabwino Yothetsera Nkhani

Tsiku lina, abale awiri a ku Azerbaijan ankalalikira ndipo anakumana ndi munthu wina yemwe anaima panja pa nyumba ina. Atayamba kumulalikira, munthuyo anati: “Ndikuona kuti kumvetsera zimene mukufuna kundiuza ndi tchimo.” Kenako anapisa m’thumba n’kutulutsa mpeni ndipo anati: “Munthu wina wakhala akundichitira zinthu zopanda chilungamo kwa nthawi yaitali. Ndiye ndatopa nazo moti ndikupita kukamupha kuti chilungamo chioneke.”

Abalewo anadabwa ndi zimenezi, komabe anauza munthuyo kuti: “Kupha munthu ndiye tchimo.”

Munthuyo anafunsa kuti: “Ndiye nditani?” Abalewo anamuwerengera lemba la Aroma 12:17-21 ndipo anamuuza kuti kubwezera ndi kwa Yehova. Anamuuzanso kuti sitiyenera kulola kuti ‘choipa chitigonjetse, koma tizigonjetsa choipa mwa kuchita chabwino.’ Kenako anamuuza kuti akakambirane nkhaniyo ndi munthuyo modekha. Anamuuzanso kuti ngati atavulaza kapena kupha munthuyo, chikumbumtima chake chizimuvutitsa. Atakhutira ndi zimene anamvazi, munthuyo anachoka.

Patatha ola limodzi, munthuyo anakumananso ndi abale aja ndipo anawauza kuti: “Ndikuchokera kwa munthu  yemwe ndimafuna kumupha uja ndipo takambirana mwamtendere. Ndikuthokoza kuti mwandithandiza kuti ndisapalamule.” Abalewo anamuuza kuti ndi Yehova amene wamuthandiza kuti asachite zomwe akananong’oneza nazo bondo.

Kashelefu Kamatayala Kanathandiza Kuti Mlongo Ayambirenso Kusonkhana

Mlongo wina wa ku Norway anasiya kusonkhana zaka zingapo zapitazo. Koma ulalikira wogwiritsa ntchito timashelefu tamatayala utayamba, mlongoyu ankadutsa pamalo ena pamene pankaikidwa kashelefu kena, akamapita kukagula zinthu.

Ngakhale kuti iye sankapita pamalowo kuti akalankhule ndi a Mboni, ankaona mabuku atasanjidwa bwino komanso maposita okongola. Iye ankachitanso chidwi chifukwa a Mboniwo ankavala bwino komanso ankaoneka ansangala. Zonsezi zinachititsa kuti mlongoyu ayambe kuganiza zobwereranso kwa Yehova.

Iye anaonanso chizindikiro cha webusaiti yathu ya jw.org, ndipo anaganiza zopita pawebusaitiyi. Atalowa pawebusaitiyi anapeza mosavuta malo amene pali Nyumba ya Ufumu yapafupi komanso nthawi ya misonkhano. Anachitanso dawunilodi mabuku athu ndipo tsiku lina anapita ku Nyumba ya Ufumu ngakhale kuti ankakayikira. Kumeneko abale ndi alongo anamulandira bwino ndipo akulu anakonza zoti mlongo wina aziphunzira naye Baibulo. Pasanapite nthawi anapeza anzake ambiri mumpingo ndipo anayambanso kuchita zinthu zonse zokhudza kulambira. Panopa amasonkhana komanso kulalikira nthawi zonse ndipo akusangalala kuti ali pa ubwenzi wolimba ndi Yehova.

Analalikira Anzake a ku Sukulu Ali M’basi

Mtsikana wina dzina lake Ronja amakhala ku Norway ndipo ali ndi zaka 15. Tsiku lina ali m’basi ya sukulu, anakambirana ndi anyamata atatu nkhani yokhudza ngati zamoyo zinasintha kuchokera ku zinthu zina kapena ayi. Koma anyamatawo  anatsutsa zimene Ronja amakhulupirira ndipo izi zinachititsa kuti iye akhale ndi timantha. Ronja anaona kuti sanakonzekere bwino nkhaniyi choncho atafika kunyumba anafunsa mayi ake kuti amuthandize kupeza mfundo zosonyeza kuti kuli Mlengi.

Norway: Ronja akufotokozera anzake zimene amakhulupirira

Tsiku lotsatira alinso m’basi muja, Ronja anayamba kukambirananso ndi anyamata aja ndipo anagwiritsa ntchito mfundo zomwe anakonzekera. Koma anyamatawo anayamba kumunyoza. Kenako mnyamata wina anakuwa kuti: “M’basi muno mulibe amene amakhulupirira zoti kuli Mulungu! Tiyeni tivote, amene amakhulupirira kuti zamoyo zinachita kusintha kuchokera ku zinthu zina aimike manja! Amene akukhulupirira kuti zinachita kulengedwa aimike manja!” Ronja anadabwa kwambiri ataona kuti mnyamata wina amene anakhala naye pafupi anakweza dzanja n’kunena kuti, “Ine ndikukhulupirira kuti zamoyo zinachita kulengedwa.” Mnyamata winanso anakweza dzanja n’kunena kuti: “Inenso.” Kenako mtsikana wina anakwezanso  dzanja n’kunena kuti: “Inenso.” Izi zikusonyeza kuti pamene Ronja ankakambirana ndi anyamata aja, ana ena m’basimo ankamvetsera. Zimene Ronja anafotokoza zinawathandiza kuti ayambe kukhulupirira kuti kulidi Mlengi.

Bambo Wina Wosadziwa Kuwerenga Anapeza Buku

Tsiku lina azibambo awiri olankhula Chiarabu a ku Syria anafika ku ofesi ya nthambi ya ku Denmark. Atafika pamalo olandirira alendo, anauza alongo amene anali pamenepo kuti akufufuza a Mboni za Yehova. Alongowo atawauza kuti afika ku ofesi ya Mboni za Yehova, anasangalala kwambiri. Kodi azibambowa analondola bwanji? Iwo anapita kulaibulale ina ya m’deralo, ndipo anasonyeza anthu ogwira ntchito kumeneko chithunzi china chimene anajambula ndi foni yawo. Chithunzicho chinali cha tsamba loyamba la buku lachiarabu la Kodi Baibulo Limaphunzitsa Chiyani Kwenikweni? Ogwira ntchito palaibulaleyo ataona zomwe zinalembedwa patsambali, anawapatsa mapu a ku ofesi ya Mboni za Yehova.

Koma azibambo awiriwo sankadziwa bwinobwino Chidanishi choncho sankamvana bwino ndi alongowo. Ndiyeno alongowo anaitana m’bale amene amadziwa Chiarabu. Atafika n’kulankhula ndi azibambowo, zinaoneka kuti mmodzi anali ndi chidwi ndipo ankafuna kuphunzira Baibulo. Choncho m’baleyo anatenga nambala yake ya foni ndipo analonjeza kuti iye limodzi ndi m’bale wina wodziwanso Chiarabu, adzapita kukayamba kuphunzira naye Baibulo.

Abalewo atapitako, bamboyo anawauza kuti kunyumba kwawo kunali kusanafikepo a Mboni. Anawauzanso kuti buku lija analipeza m’bokosi lake lolandirira makalata ngakhale kuti bokosilo silinalembedwe kuti iye amalankhula Chiarabu. Popeza bamboyo anali wosadziwa kuwerenga, anapempha mnzake kuti amuwerengere bukulo ndipo analimaliza patangotha masiku atatu. Atamva zimene zinali m’bukuli, anazindikira kuti wapeza choonadi.

 Bamboyo anafunsa abalewo kuti: “N’chifukwa chiyani nthawi yonseyi kunyumba kwanga kuno sikumafika a Mboni? Zikanakhala bwino ndikanayamba kuphunzira Baibulo kalekale.” Bamboyu akupitiriza kuphunzira Baibulo ndi abalewo ndipo akusangalala kwambiri ndi zomwe akuphunzira. Iye akukhala m’dzikoli chifukwa anathawa kwawo ndipo amawasowa kwambiri achibale ake. Choncho kuphunzira Baibulo kumamuthandiza kuti asamakhale ndi nkhawa kwambiri.

Anayamba Kusangalala

Bambo wina wa ku Ukraine, dzina lake Dmitry, anali bwana pakampani ina yopanga fodya. Bamboyu atazindikira kuti kusuta kumawononga thanzi la munthu, anaganiza zosiya ntchito. Pasanathe miyezi itatu, mayi ake komanso apongozi ake aakazi anamwalira. Popeza ankawakonda, zinamukhudza kwambiri. Iye ankaganiza kuti abusa a kutchalitchi chake cha Orthodox amulimbikitsa komanso amuyankha mafunso omwe ankamuzunguza mutu, koma sanamuthandize. Mnzake wina anamuuza kuti munthu amene ali m’chipembedzo cha Orthodox “amavala mtanda pakhosi pake, koma mumtima mwake amakhala wosasangalala.” Zimene mnzakeyu ananena zinali zoona chifukwa ndi mmene bamboyu ankamvera. Bambo Dmitry ankaona kuti sadziwa chilichonse chokhudza Mulungu komanso Baibulo. Zimenezi zinawasokoneza mutu moti anayamba kupemphera kwa Mulungu kuti awathandize. Kenako anakumbukira kuti anamvapo za Mboni za Yehova. Atafufuza pa intaneti, anapeza webusaiti yathu ndipo anasangalala kwambiri ndi mfundo zimene anawerenga pawebusaitiyi zokhudza Baibulo. Ndiyeno anafufuza kumene kunali Nyumba ya Ufumu. Atafika ku Nyumba ya Ufumuyo, anakumana ndi m’bale amene ankalandira alendo. A Dmitry anauza m’baleyo kuti: “Ndikufuna munthu woti azindiphunzitsa Baibulo.” Panopa, bamboyu wakhala akuphunzira Baibulo kwa miyezi 6 ndipo amasonkhano nthawi zonse.

 Amachita Ulendo Wobwereza Pogwiritsa Ntchito Timakalata

A Paul ndi akazi awo a Faith amakhala ku Britain. Tsiku lina ali mu utumiki, anacheza ndi Mayi Susan ndipo anapangana tsiku loti adzakumanenso. Koma atapitako, sanawapeze. Banjali linatsatira malangizo amene ali mu Utumiki Wathu wa Ufumu wa November 2014 ndipo anasiya kakalata konena kuti adzabweranso tsiku lotsatira. Atapitanso, anapeza kuti Mayi Susan asiya kakalata pakhomo la nyumba. M’kakalatamo anafotokoza kuti satha kukumana nawo chifukwa anali atapita kukagula zinthu za ukwati wa mwana wawo wamkazi. Banjali linasiyanso kakalata kena konena kuti adzabweranso mlungu wotsatira. Pa ulendo umenewu anawapeza ndipo anayambitsa phunziro pogwiritsa ntchito buku la Baibulo Limaphunzitsa Chiyani.

Britain: A Paul ndi akazi awo akusiya kakalata panyumba ina

Koma popeza ukwati wa mwana wawo unali mlungu wotsatira, Mayi Susan anapempha kuti adzakumane ukwatiwo ukadutsa. A Paul ndi akazi awo atapitako, sanapeze mayiwo  choncho anangosiyanso kakalata kena kokhala ndi nambala yawo ya foni. Kenako analandira meseji yowapepesa yochokera kwa mayiwa. Iwo anati anasemphana chifukwa pa nthawiyo anali kwa aneba awo. Koma a Paul ndi a Faith atapitakonso anawapeza moti anayamba kuphunzira nawo Baibulo ndipo phunziroli likupitirira.

Banjali likuona kuti njira yolalikira pogwiritsa ntchito timakalata ndi yothandiza kwambiri. Iwo anati: “Anthu ambiri amene timawasiyira kakalata amatiimbira foni. Kunena zoona, njirayi ndi yothandizadi.”

Chikhulupiriro Chake Chinathandiza Nesi

Mu August, 2014, m’bale wina anagonekedwa m’chipatala china ku Hungary. M’baleyu anali ndi vuto loti mtsempha umodzi umene umapititsa magazi kumapapo unatsekeka. N’zomvetsa chisoni kuti pasanapite nthawi yaitali, anamwalira. Mkazi wa malemuyu analemba zokhudza nesi wina yemwe anawathandiza kwambiri pa nthawi imene ankadwazika matendawo. Nesiyo dzina lake linali Tünde.

Mlongoyu anati: “Mu 2015, ine ndi mwana wanga tinapita ku Msonkhano Wachigawo wakuti, ‘Tsanzirani Yesu.’ Tsiku lomaliza la msonkhanowu ndili pamalo oimika magalimoto, kunabwera mayi wina n’kudzandikumbatira ndipo anayamba kulira. Mayiyu anali nesi amene ankasamalira mwamuna wanga uja ndipo pa nthawiyi n’kuti patatha chaka. Iye anafotokoza kuti tsiku lililonse nesi aliyense amapatsidwa wodwala woti azimusamalira. Ndiye nesiyu ankapemphera m’mawa uliwonse kuti auzidwe kuti azisamalira mwamuna wanga. Ndipo ankasangalala kuti pemphero lakeli linkayankhidwa.”

Mlongoyu anatinso: “Nesiyu anati ankaona kuti mwamuna wanga anali ndi chikhulupiriro ndiponso khalidwe labwino. Komanso ankasonyeza kuti anali ndi chiyembekezo. Izi ndi zimene zinathandiza nesiyu kuti ayambe kuphunzira Baibulo ndi Mboni za Yehova.”

 Mlongoyu ananenanso kuti: “Nesiyu akuti amafunitsitsa kuti adzalandire mwamuna wanga akadzaukitsidwa. Akufuna kudzamuuza kuti chikhulupiriro chake cholimba komanso khalidwe lake labwino linamuthandiza kuti adziwe Yehova komanso zimene walonjeza.”

Ankalalikira Madalaivala

Bulgaria: Akulalikira kwa madalaivala

Chifukwa choti anthu ankachita zionetsero komanso kutseka misewu, nthawi zina malo ochitira chipikisheni, omwe ali m’malire a dziko la Greece ndi Bulgaria, ankatsekedwa. Izi zinkachititsa kuti pakhale mizere yaitali kwambiri ya magalimoto odikira kuti adutse pamalo amenewa. Abale a mpingo wina wa ku Bulgaria anaona kuti uwu ndi mwayi wawo kuti agawire mabuku athu kwa madalaivala a magalimotowo. Abalewo anapita kumalowa ndipo anatenga mabuku, timabuku, magazini komanso timapepala. Zinthuzi zinali za m’zinenero zosiyanasiyana zokwana 12. Madalaivala ambiri a mathiraki anali otopa komanso okhumudwa komabe ankavomera kucheza ndi abalewa. Abalewo ankawamvetsera mokoma mtima ndipo ankawalimbikitsa ndi uthenga wa m’Baibulo. Dalaivala wina anafunsa kuti: “Kodi ndinu a Mboni eti?” Abalewo atavomera, dalaivalayo anati: “Ndinadziwa. A Mboni za Yehova okha ndi amene amalalikira ngati mmene mukuchitiramu.” Dalaivala wina wa ku Austria ananena kuti: “Koma a Mboni mumayesetsa! Mpaka mwafika kuno? Mukugwira ntchito yotamandika kwabasi. Pitirizani kuthandiza anthu ndi kuwalimbikitsa.” Dalaivala winanso anati: “Poyamba sindinkafuna kuwerenga mabuku anu. Koma zimene mwandipatsazi ndiwerenga.” M’bale wina atalalikira dalaivala wina, dalaivalayo anayamba kulira. Iye ananena kuti poyamba anali wa Mboni koma anasiya zaka zambiri zapitazo. Abalewo anamulimbikitsa kuti awerenge zimene anamupatsazo ndipo akabwerera kwawo, akayambirenso kusonkhana.