Pitani ku nkhani yake

Pitani ku menyu yachiwiri

Pitani ku mitu ya nkhani

Mboni za Yehova

Chichewa

Buku Lapachaka la Mboni za Yehova la 2017

 GEORGIA

“Zinthu Zonse N’zotheka kwa Mulungu”

Natela Grigoriadis

“Zinthu Zonse N’zotheka kwa Mulungu”
  • CHAKA CHOBADWA 1960

  • CHAKA CHOBATIZIDWA 1987

  • MBIRI YAKE Mlongo Natela atangobatizidwa, anathandiza kwambiri kuti ntchito yosindikiza mabuku iziyenda bwino pa nthawi imene kuchita zimenezi kunali koletsedwa. Popeza anali bwana wa bizinezi yaikulu, anathandiza kuti tizipeza zipangizo zosindikizira mabuku athu.

CHAKUMAPETO kwa zaka za m’ma 1980, wochititsa Phunziro la Nsanja ya Olonda yekha ndi amene ankakhala ndi magazini, ndipo nthawi zambiri magaziniyi inkakhala yochita kukopera pamanja. Tsiku lina ndinapita pamene panali M’bale Genadi Gudadze, yemwe anali mmodzi wa akulu a mpingo wathu n’kumupempha kuti tiyambe kusindikiza magazini athu.

Pa nthawiyi abale ankasindikiza mabuku ochepa pogwiritsa ntchito chipangizo chosindikizira mabuku chomwe anapanga okha. Kuti azisindikiza magazini nthawi zonse, ankafunika kupeza chipangizo china chabwino, munthu wodziwa kutaipa, chotaipira komanso mapepala okwanira. Koma kupeza zinthu zimenezi sinali nkhani yamasewera, chifukwa pankafunika kukalembetsa kuboma komanso panali bungwe lina lomwe linkagwira anthu amene ankasindikiza mabuku popanda chilolezo.

Tsiku lina ndinapeza chipangizo chotaipira kwa mnzanga wina yemwe ankatha kugula zipangizo zomwe boma linasiya kuzigwiritsa ntchito. Mchemwali wanga ankadziwa kutaipa ndipo anavomera kuti akhoza kutithandiza. Abale anakonza chipangizo china  chosindikizira mabuku ndiponso anapeza malo oti azikagulako mapepala. Zinthu zonse zinayenda bwino moti pasanapite nthawi, tinasindikiza magazini yoyamba ya Nsanja ya Olonda yachijojiya.

Koma kenako tinakumana ndi vuto lina. Tsiku lina M’bale Genadi anandiuza kuti: “M’pofunika tipeze malo ena ogula mapepala.” M’baleyu anali ataona mapepala mu ofesi ina ya boma, koma analephera kugula chifukwa pamalowo panali apolisi. Ndiyeno tinadzifunsa kuti, ‘Kodi tipange bwanji kuti tigule mapepala amenewa?’ Ineyo ndinkakonda kunena kuti, “Zimenezi sizingatheke.” Koma M’bale Genadi anayankha kuti, “Musadzanenenso kuti, ‘Zimenezi sizingatheke.’ ‘Zinthu zonse n’zotheka kwa Mulungu.’”Mat. 19:26.

Ndinaganizira mawu amenewa pamene ndinkapita ku ofesi ija tsiku lotsatira. Ngakhale kuti ndinkachita mantha, Yehova anandithandiza kuti ndikumane ndi mayi wina, yemwe ananena kuti atumiza pempho langa loti tigule mapepala ku ofesi ya bwana wamkulu. Bwana wamkuluyo anali mwamuna wake. Kungochokera nthawi imeneyo tinayamba kugula mapepala ku ofesi imeneyi ndipo sitinakumanenso ndi vuto la kusowa kwa mapepala osindikizira mabuku.