Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

 GEORGIA

Ndinkaganiza Kuti Zinthu Zikundiyendera

Madona Kankia

Ndinkaganiza Kuti Zinthu Zikundiyendera
  • CHAKA CHOBADWA 1962

  • CHAKA CHOBATIZIDWA 1990

  • MBIRI YAKE Poyamba anali m’chipani chachikomyunizimu ku Georgia. Koma atakhala wa Mboni, anathandiza anthu ambiri kuphunzira choonadi. Mu 2015, anamaliza maphunziro a Sukulu ya Akhristu Olalikira za Ufumu ku Tbilisi.

NDINAKUMANA koyamba ndi a Mboni za Yehova mu 1989. Pa nthawiyi ndinali munthu wotchuka m’chipani chachikomyunizimu m’dera lathu ku Senaki. Ndinkakhala nawo pazokambirana za akuluakulu a chipani chachikomyunizimu zomwe zinkachitikira ku Georgia. Zokambirana zimenezi zinali zofanana ndi zimene aphungu a kunyumba ya malamulo amachita masiku ano. Ndinalinso pa chibwenzi ndi mnyamata wina moti ndinkaona kuti zinthu zikundiyendera kwambiri.

Makolo anga anandiphunzitsa kukonda Mulungu. N’chifukwa chake ndinkakhulupirirabe Mulungu, ngakhale kuti ndinali m’chipani chachikomyunizimu. Koma nditayamba kuphunzira Baibulo ndi a Mboni, ndinapeza mayankho a mafunso amene ankandizunguza mutu. Nditakhutira kuti zimene ndinkaphunzirazo zinali zoona, ndinadzipereka kwa Yehova. Zimenezi sizinasangalatse makolo anga, anzanga komanso chibwenzi changa chija.

 Nditayamba kusonkhana ndi a Mboni, achibale anga anasiya kundiona kuti ndine m’bale wawo. Zimene ndinayamba kukhulupirira zinachititsanso kuti ndisiye zandale. Kuti zimenezi zisandisokoneze, ndinaganiza zochoka kwathu, ndinathetsa chibwenzi chija komanso ndinasiya udindo umene ndinali nawo m’chipani. Nditabatizidwa, abale anga komanso anzanga anayamba kunditsutsa kwambiri. Choncho, popeza ndinali munthu wodziwika kwambiri m’dera lakwathu, ndinasamukira mumzinda wa Kutaisi ndipo ndili kumeneko, ndinayamba upainiya.

Anthu akandifunsa ngati sindidandaula kuti ndinakumana ndi mavuto ambiri chifukwa chokhala wa Mboni, ndimawayankha ndi mtima wonse kuti sindinong’oneza bondo mpang’ono pomwe. Ndimawauzanso kuti ndine munthu wosangalala kwambiri. Ngakhale kuti makolo anga sanasangalale nditakhala wa Mboni, ndimawayamikira kwambiri chifukwa anandiphunzitsa kukonda Mulungu komanso anthu ena. Zimenezi zinandithandiza kwambiri kuti ndipeze chinthu chamtengo wapatali pa moyo wanga.