Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

 GEORGIA

Ndinkafunitsitsa Nditasintha Zochita Zanga

Davit Samkharadze

Ndinkafunitsitsa Nditasintha Zochita Zanga
  • CHAKA CHOBADWA 1967

  • CHAKA CHOBATIZIDWA 1989

  • MBIRI YAKE Anatumikirapo monga woyang’anira dera. Kuyambira mu 2013, wakhala akuphunzitsa masukulu osiyanasiyana ophunzitsa Baibulo.

MU 1985, ndili ndi zaka 18, boma la Soviet Union linandiuza kuti ndikamenye nawo nkhondo. Kunena zoona sindinkafuna kumenya nawo nkhondo chifukwa ndinkaona kuti asilikali amakonda kuchita zinthu zankhanza komanso zopanda chilungamo. Pansi pamtima ndinkati, ‘Sindikufuna kukhala ngati anthu amenewa.’ Kenako ndinapitabe kukamenya nkhondo koma ndinkaona kuti ndikulephera kuchita zinthu zabwino zomwe ndinkafuna kuchita. Kunena zoona, ndinkafunitsitsa nditasintha zochita zanga.

Nditamaliza kugwira ntchito ya usilikali, ndinabwereranso kwathu. Tsiku lina chakumadzulo titamaliza kuchita phwando limene tinakonza, ndinapempha Mulungu kuti andithandize kusintha moyo wanga. Tsiku lotsatira pamene ndinkapita kuntchito, ndinadzera kunyumba kwa azakhali anga, omwe anali a Mboni za Yehova. Nditalowa m’nyumba, ndinapeza anthu akuchita Phunziro la Buku la Mpingo. Anthuwo anandilandira bwino, moti ndinaganiza zokhala pansi kuti ndimve zimene ankakambirana.

Atandipempha kuti ndiziphunzira Baibulo, ndinavomera ndipo patangotha miyezi 6, ndinabatizidwa. Ndimaona kuti Yehova anandithandiza kuti ndikhale munthu wabwino, chinthu chomwe sindikanakwanitsa pandekha.