Pitani ku nkhani yake

Pitani ku menyu yachiwiri

Pitani ku mitu ya nkhani

Mboni za Yehova

Chichewa

Buku Lapachaka la Mboni za Yehova la 2017

 GEORGIA | 1924-1990

Misonkhano Inawathandiza Kukhala Ndi Chikhulupiriro Cholimba

Misonkhano Inawathandiza Kukhala Ndi Chikhulupiriro Cholimba

Misonkhano yachikhristu inathandiza kwambiri kuti anthu amene anali atangophunzira kumene Baibulo akhale ndi chikhulupiriro cholimba. Anthu amene anali atangobatizidwa kumene, ankapereka nyumba zawo kuti muzichitikira misonkhano ngati mmenenso abale omwe anabatizidwa kalekale ankachitira. Amene ankafika pamisonkhanoyi ankalandiridwa bwino ndipo zimenezi zinachititsa kuti azikondana kwambiri.

Zikakhala kuti anthu angapo akufuna kubatizidwa, abale ankakonza zoti pachitike misonkhano yapadera ndipo ankachita zimenezi mwachinsinsi. Mu August 1973, abale anakonza zoti msonkhano ngati umenewu uchitikire kunja kwa mzinda wa Sokhumi, pafupi ndi nyanja ya Black Sea.  Koma anthu 35 amene ankayembekezera kubatizidwa pamsonkhanowu sanabatizidwe. Zimenezi zinachitika chifukwa msonkhanowo usanathe, apolisi anafika pamalowo n’kumanga abale ndi alongo ena kuphatikizapo M’bale Vladimir Gladyuk.

M’bale Vladimir komanso abale ndi alongo aja atangomasulidwa, anadziwitsa anthu amene ankafuna kubatizidwa aja kuti akonzekere kubatizidwa. Anthuwa anabatizidwa patapita masiku awiri kuchokera nthawi imene ubatizo woyamba uja unalephereka. M’bale Vladimir ananena kuti: “Tinkaona kuti Yehova ndi amene akutithandiza. Ubatizowo utangotha, tinapemphera kwa Yehova n’kumuthokoza chifukwa cha zimene anatichitira.”

Kuzunzidwa Kunathandiza Kuti Uthenga Wabwino Ufalikire

Patangotha masiku awiri kuchokera pamene anthu aja anabatizidwa, M’bale Vladimir Gladyuk anamangidwanso. Kenako m’baleyu, Mlongo Itta Sudarenko ndi Mlongo Natela Chargeishvili, anaweruzidwa kuti akakhale kundende kwa zaka zingapo. Zimenezi zinachititsa mantha ofalitsa ambiri. Komabe sanasiye kulalikira, kungoti ankachita zimenezi mosamala kwambiri.

Kuti apolisi asawatulukire, ofalitsa ankakalalikira m’matauni ena akutali m’malo molalikira m’tauni yawo. Choncho tinganene kuti kuzunzidwa kunachititsa kuti uthenga wabwino ulalikidwe m’madera ambiri.

Pa nthawi imene dziko la Georgia linali pansi pa ulamuliro wachikomyunizimu, ofalitsa omwe ankakhala m’mizinda ikuluikulu, ankalalikira m’misewu komanso m’mapaki. M’malo amenewa ankakumana ndi anthu omwe ankachokera m’matauni komanso m’midzi ina, omwe ankabwera kudzaona achibale awo komanso kudzagula katundu.

 Mlongo Babutsa Jejelava ndi mmodzi mwa anthu omwe ankakonda kulalikira m’chigawo chakumadzulo kwa dziko la Georgia. Iye anati: “Anthu sankandikayikira chifukwa ankadziwa kuti ndili ndi achibale m’madera osiyanasiyana. Pamene zaka ziwiri zinkatha, ndinali ndikuphunzira Baibulo ndi anthu oposa 20 ku Zugdid. Ndinkaphunziranso Baibulo ndi anthu enanso 5 m’tauni ya Chkhorotsku. Patapita nthawi, anthu onsewa anabatizidwa.”

Pankafunika Mabuku Ambiri Achijojiya

Pasanapite nthawi yaitali, zinali zoonekeratu kuti ku Georgia kunkafunika mabuku ambiri. Ofalitsa akamachititsa maphunziro a Baibulo komanso akamachita maulendo obwereza, ankaona kuti mpofunika kukhala ndi mabuku a chinenero chimene anthuwo angamve bwinobwino. *

Mlongo Babutsa ananena kuti zinkakhala zovuta kwambiri kuchititsa phunziro la Baibulo popanda mabuku. Iye anati: “Baibulo komanso mabuku amene ndinali nawo anali a m’Chirasha. Choncho ndinkafunika kumamasulira zimene zili m’mabukuwo kuti munthu amene ndikum’phunzitsa Baibulo azimva.” Mlongoyu anayamba kumasulira nkhani za m’magazini athu m’Chijojiya ndipo pomasulirapo ankangogwiritsa ntchito dikishonale basi. Anamasuliranso buku lonse la Uthenga Wabwino wa Mateyu.

Abale ndi alongo olimba mtima ankasindikiza mabuku pogwiritsa ntchito makina aang’ono

Anthu ambiri ankasangalala kwambiri ndi nkhani zimene mlongoyu ankamasulira m’chinenero chawo moti ankakopera zinthuzo kuti aziziwerenga. Ndiye popeza zinali zovuta kupeza Baibulo la m’Chijojiya, anthu ena amene ankaphunzira Baibulo anayamba kukopera pamanja Mawu a Mulungu.

 “Ndinkakopera Baibulo Tsiku Lonse”

Mabuku amene anamasuliridwa m’Chijojiya ankaperekedwa kwa abale ndi alongo komanso anthu ena achidwi. Anthu ena akamaliza kuwerenga mabukuwo, ankawapereka kwa anthu ena kuti nawonso awerenge. Munthu aliyense ankapatsidwa masiku angapo kapena mlungu umodzi kuti awerenge buku kapena magazini. Kenako abale anapeza Baibulo la Malemba Achigiriki la Chijojiya chamakono. Banja lina litalandira Baibuloli linaganiza zolikopera pamanja.

Raul Karchava anali ndi zaka 13 zokha pamene bambo ake anamupempha kuti akopere Baibulo la Malemba Achigiriki pamanja. Iye anati: “Bambo anga anagula katoni ya makope komanso mabopeni ndi mapensulo a mitundu yosiyanasiyana. Ankaganiza kuti zimenezi zichititsa kuti ndikhale ndi chidwi  chogwira ntchitoyi. Ngakhale kuti poyamba ndinkachita mantha, ndinavomera kugwira ntchitoyi. Ndinkakopera Baibulo tsiku lonse. Ndikatopa ndinkapumako pang’ono n’cholinga choti ndiwongole manja.”

Magazini a Nsanja ya Olonda komanso kabuku ka Kuphunzira Malemba Tsiku ndi Tsiku m’Chijojiya zomwe anazikopera pamanja

Achibale a Raul anasangalala kwambiri atadziwa kuti abale alola kuti akhoza kukhalabe ndi Baibulolo kwa masabata ena angapo. Abalewa anachita zimenezi n’cholinga choti Raul amalize kugwira ntchitoyi. Pamene miyezi iwiri inkatha, anali atamaliza kukopera mabuku onse 27 a Malemba Achigiriki Achikhristu.

Ngakhale kuti anthu ena ankadzipereka kukopera mabuku pamanja, pankafunikabe mabuku ambiri chifukwa chiwerengero cha anthu amene ankaphunzira Baibulo chinkawonjezekabe. Kuti athandize anthu amenewa, abale ndi alongo ena  olimba mtima, anayamba kusindikiza mabuku athu m’nyumba zawo, n’kumawagawa kwa anthu ena. Ankachita zimenezi ngakhale kuti ankadziwa kuti akhoza kumangidwa.

Ntchito yolalikira m’chigawo chakumadzulo kwa dziko la Georgia inayamba kuyenda bwino kwambiri. Nanga bwanji m’chigawo chakum’mawa kwa dzikoli? Kodi kulikulu la dzikoli kunali ofalitsa amene akanathandiza anthu omwe ankafuna kudziwa choonadi ngati M’bale Vaso Kveniashvili tamutchula kale uja?

Uthenga Wabwino Unafika Kulikulu la Dzikoli

M’zaka za m’ma 1970, akuluakulu a boma la Soviet Union anayamba kuthamangitsa a Mboni za Yehova m’nyumba zawo. Ankachita zimenezi n’cholinga choti awaopseze. Ena mwa anthu amene anathamangitsidwa ndi M’bale Oleksii ndi Mlongo Lydia Kurdas, omwe anathawa kuchokera kwawo ku Ukrain n’kupita ku Georgia. Atafika m’dzikoli anakakhala kulikulu la dzikoli ku Tbilisi. Banja limeneli linakhala m’ndende kwa zaka zambiri chifukwa cha chikhulupiriro chawo.

Larisa Kessaeva (Gudadze) m’zaka za m’ma 1970

Banjali litafika kumeneku linalalikira a Zaur Kessaev ndi akazi awo a Eteri omwe ankakondanso zopemphera. Mwana wa a Kessaev, yemwe anali ndi zaka 15 dzina lake Larisa, anafotokoza zomwe zinachitika atakumana koyamba ndi a Oleksii ndi akazi awo a Lydia. Iye anati: “Tinayesetsa kuwauza kuti chipembedzo chomwe chimaphunzitsa zolondola ndi cha Orthodox. Koma titakambirana kwa maulendo angapo, mfundo zinatithera koma iwowo sanasiye kutifotokozera zimene Baibulo limanena.”

Larisa ananenanso kuti: “Tikapita kutchalitchi, ndinkakonda kuwerenga Malamulo Khumi omwe analembedwa pakhoma pakati pa mafano awiri. Ndiyeno tsiku lina chakumadzulo, banja lija linabweranso ndipo linatiwerengera Ekisodo 20:4, 5. Ndinadabwa kwambiri ndi zomwe ndinamva. Tsiku limenelo tulo sindinatione chifukwa ndinkangoganiza kuti,  ‘Kodi n’zoonadi kuti kulambira mafano n’kusamvera lamulo la Mulungu?’”

Kuti apeze yankho la funso limeneli, m’mawa kutangocha, Larisa anadzuka n’kupita kutchalitchi kuja ndipo anakawerenganso lamulo lakuti, “Usadzipangire fano kapena chifaniziro cha chinthu chilichonse . . . Usaziweramire.” Pa nthawi imeneyi ndi pamene anazindikira tanthauzo la lamulo limeneli. Patapita nthawi, Larisa ndi makolo ake anabatizidwa ndipo ndi amene anali Mboni zoyambirira ku Tbilisi.

Chilungamo Chimene Ankafuna Chinachitika

Patapita zaka 20 atakumana ndi a Mboni, a Vaso Kveniashvili anakumana ndi munthu wina yemwe ankasonkhana ndi a Mboni za Yehova ku Tbilisi. A Vaso anasangalala kwambiri kukumananso ndi a Mboni patapita nthawi yaitali.

Patadutsa zaka 24 kuchokera pamene anakumana ndi a Mboni, a Vaso Kveniashvili anakhala a Mboni za Yehova

Poyamba, abale ndi alongo ankawakayikira moti sankafuna kuti azisonkhana nawo chifukwa ankadziwa kuti anali chigawenga. Abale ena ankaganiza kuti a Vaso ndi kazitape wa  boma la Soviet Union. Choncho kwa zaka 4, abale sanalole kuti a Vaso azisonkhana nawo.

Abalewa atatsimikizira kuti a Vaso analibe cholinga chilichonse choipa, anawalola kuti azisonkhana ndipo kenako anabatizidwa n’kukhala a Mboni. A Vaso anasangalala kwambiri chifukwa anayamba kulambira “Mulungu amene amaweruza mwachilungamo,” yemwe anayamba kumufunafuna kuyambira ali wamng’ono. (Yes. 30:18) A Vaso anapitirizabe kutumikira Yehova mokhulupirika mpaka pamene anamwalira mu 2014.

Pamene chaka cha 1990 chinkafika, uthenga wabwino unali ukulalikidwa m’zigawo zonse za dziko la Georgia. M’dzikoli munali ofalitsa pafupifupi 900 ndipo ankaphunzira Baibulo ndi anthu okwana 942. Zimene ofalitsawa anachita zinathandiza kuti chiwerengero cha ofalitsa chiwonjezeke kwambiri.

^ ndime 12 Pa nthawi imene dzikoli linkalamuliridwa ndi boma lachikomyunizimu, Mabaibulo ankasowa kwambiri. Izi zinkachitika ngakhale kuti mabuku ena a m’Baibulo anali atamasuliridwa kale m’Chijojiya. Mabukuwa anamasuliridwa m’zaka za m’ma 400 C.E.—Onani bokosi la mutu wakuti, “Baibulo la M’Chijojiya.”