Pitani ku nkhani yake

Pitani ku menyu yachiwiri

Pitani ku mitu ya nkhani

Mboni za Yehova

Chichewa

Buku Lapachaka la Mboni za Yehova la 2017

Dera lamapiri la Svaneti

 GEORGIA

Mfundo Zachidule Zokhudza Dziko la Georgia

Mfundo Zachidule Zokhudza Dziko la Georgia

Anthu amasangalala akamakolola zipatso za mphesa

Mmene Dzikoli Lilili: Kuli mapiri akuluakulu omwe amaoneka oyera pamwamba pake chifukwa cha sinowo [kapena kuti chipale chofewa]. Mapiri ena ndi aatali kufika mamita 4,500. Dzikoli linagawidwa m’zigawo ziwiri, chigawo chakum’mawa komanso chakumadzulo. M’zigawo zimenezi muli madera osiyanasiyana ndipo dera lililonse lili ndi nyengo, chikhalidwe, nyimbo, magule komanso zakudya zake.

Anthu: Ambiri mwa anthu okwana 3.7 miliyoni omwe amakhala m’dziko la Georgia ndi nzika za dzikoli.

Chipembedzo: Anthu ambiri m’dzikoli ali m’chipembedzo cha Orthodox. Anthu 10 pa 100 alionse ndi Asilamu.

Chinenero: Chinenero cha anthu a ku Georgia ndi chosiyana kwambiri ndi zinenero za anthu a m’mayiko ena omwe anayandikana ndi dzikoli. Zikuoneka kuti afabeti ya m’dzikoli inayamba kale kwambiri chisanafike chaka cha 1 C.E.

 Ntchito Zawo: Anthu ambiri ndi alimi. Koma chaposachedwapa, dzikoli linayambanso kudalira kwambiri ntchito zokopa alendo.

Nyengo: Kum’mawa kwa dzikoli si kotentha kwambiri. Koma m’mbali mwa nyanja ya Black Sea, m’chigawo chakumadzulo kwa dzikoli, ndi kotentha ndipo kumakhala zipatso zambiri monga malalanje, mandimu ndi zina.

Akukolola zipatso za mphesa m’dera la Kakheti

 Chakudya: Anthu a m’dzikoli amakonda kudya buledi m’mawa, masana komanso madzulo. Anthu ambiri amaphika okha buledi ndipo amagwiritsa ntchito mauvuni opangidwa ndi dongo. Amakonda supu wophikidwa ndi zinthu zosiyanasiyana komanso amamuthira zokometsera. Anthu a ku Georgia akhalanso akupanga vinyo kwa zaka zambiri. M’madera akumidzi amasunga vinyo m’mitsuko ikuluikulu kuti apese. Mabanja ambiri amalima mphesa ndipo amapanga vinyo wawo. Ku Georgia kuli mitundu ya mphesa pafupifupi 500.

Akupanga buledi