Pitani ku nkhani yake

Pitani ku menyu yachiwiri

Pitani ku mitu ya nkhani

Mboni za Yehova

Chichewa

Buku Lapachaka la Mboni za Yehova la 2017

 GEORGIA

Anthu Ambiri Olankhula Chikadishi Akuphunzira Choonadi

Anthu Ambiri Olankhula Chikadishi Akuphunzira Choonadi

MAYI wina dzina lake Gulizar anati: “Ndimathokoza Yehova chifukwa cholola kuti ndizimva uthenga wabwino m’chinenero changa.”

A Gulizar anasonkhana ndi a Mboni za Yehova kwa zaka 8, koma anabatizidwa atachita msonkhano wa m’chinenero chawo cha Chikadishi. Mayi ameneyu ndi mmodzi mwa anthu achikadi omwe aphunzira Baibulo ku Georgia zaka zingapo zapitazi. Tiyeni tione zinthu zina zokhudza anthu a mtundu umenewu.

 Anthu a mtundu wachikadi akhala akupezeka ku Middle East kuyambira kale kwambiri. Akatswiri ena amaganiza kuti anthu a mtunduwu anachokera ku mtundu wakale wa Amedi, womwe umatchulidwa m’Baibulo. (2 Maf. 18:11; Mac. 2:9) Chinenero chawo chili m’gulu la zinenero za Chiirani.

Masiku ano, anthu ambiri achikadi akupezeka m’mayiko osiyanasiyana monga ku Armenia, Iran, Iraq, Syria komanso Turkey. M’dziko la Georgia muli Akadi pafupifupi 20,000. Anthuwa amaopa Mulungu kwambiri komanso amakonda zopemphera.

Ku Georgia kuli ofalitsa okwana 500 achikadi ndipo kuli mipingo itatu yachikadishi. N’zosangalatsa kwambiri kuti m’chaka cha 2014, ku Tbilisi kunachitika msonkhano woyamba wa m’Chikadishi. Pamsonkhanowu panali alendo ochokera ku Armenia, Germany, Turkey ndi Ukraine.