UTHENGA wabwino unafalikira m’dziko la Georgia mosaonekera ngati mmene Yesu ananenera mufanizo la zofufumitsa. (Mat. 13:33) Mofanana ndi zofufumitsa, poyamba zotsatira za ntchito yathu yolalikira m’dzikoli sizinkaoneka bwinobwino. Koma kenako uthenga wabwino unafalikira ndipo unasintha miyoyo ya anthu ambiri.

Werengani nkhani yosangalatsayi ndiponso yolimbikitsa yonena za abale a m’dziko la Georgia. Abalewa anasonyeza chikondi, chikhulupiriro, kumvera, khama komanso kulimba mtima ‘pa nthawi yabwino ndi pa nthawi yovuta.’2 Tim. 4:2.