Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

 ZIMENE ZACHITIKA M’CHAKA CHAPITACHI

“Taona Zodabwitsa”

“Taona Zodabwitsa”

Munthu wosaona akubatizidwa

TSIKU lina Yesu atachiritsa munthu wolumala, ‘anthu onse anadabwa kwambiri, ndipo anayamba kutamanda Mulungu, mwakuti anagwidwa ndi mantha. Iwo anali kunena kuti: “Taona zodabwitsa lero!”’ (Luka 5:25, 26) Masiku ano Yehova akuchita zambiri kudzera mwa Mwana wake, kapolo wokhulupirika ndi wanzeru komanso atumiki ake padziko lonse. Tikaganizira zonsezi timanenanso kuti: “Taona zodabwitsa.”