Pitani ku nkhani yake

Pitani ku menyu yachiwiri

Pitani ku mitu ya nkhani

Mboni za Yehova

Chichewa

Buku Lapachaka la Mboni za Yehova la 2015

 ZIMENE ZACHITIKA M’CHAKA CHAPITACHI

Lipoti la Milandu

Lipoti la Milandu

ARMENIA Dzikoli Layamba Kupereka Ntchito Zina kwa Akhristu Amene Akana Usilikali

Armenia: Boma la dzikoli limapereka ntchito zina kwa abale amene akana usilikali. Abale ena amapatsidwa ntchitozi kumidzi yakutali ndipo apezerapo mwayi wolalikira mwakhama.

Mu 2013, boma la Armenia linavomereza zoti a Mboni za Yehova amene akana usilikali asamamangidwe koma azingopatsidwa ntchito zina. Nthambi ya m’dzikoli yanena kuti mu January 2014, abale 71 anapatsidwa ntchito zina m’malo mwa usilikali. Ena anapatsidwa ntchito ya ku Khitchini pomwe ena ya m’chipatala. Anthu amene  akuyang’anira ntchitozi ananena kuti abalewa amagwira bwino ntchito zinazo ngakhale kuti n’zovuta. Abale akuyamikira kwambiri mwayiwu ndipo akusangalala kugwira ntchito zosatsutsana ndi chikumbumtima chawo. * M’bale wina anati: “Tikuthokoza kwambiri Yehova. Watithandiza kuti tizigwira ntchito zosatsutsana ndi chikumbumtima chathu. Tilinso ndi ufulu wolambira Yehova bwinobwino.”

DOMINICAN REPUBLIC Poyamba Dzikoli Linkalola Tchalitchi Chakatolika Chokha Kumangitsa Ukwati

Mu 1954, dziko la Dominican Republic linasaina pangano loti Tchalitchi cha Katolika chokha n’chimene chizimangitsa maukwati. Panganolo linali loti ngati ukwati sumangitsidwa ndi Tchalitchichi ndiye kuti uyenera kumangitsidwa ndi akuluakulu a boma. Koma mu 2010, lamuloli linasinthidwa moti athu a zipembedzo zina apatsidwanso mphamvu zomangitsa ukwati. Panali maphunziro a anthu amene angafune kupatsidwa mwayi womangitsa ukwati. Ofesi ya nthambi inasankha akulu 30 kuti akachite nawo maphunzirowo. Anthu 2,000 anapempha kuti achite nawo maphunzirowo. Koma anthu 32 okha ndi amene anayenerera kupatsidwa mwayi womangitsa maukwati ndipo 30 anali abalewo.

 INDIA Sadzasiya Kulalikira Mopanda Mantha

Sundeep ndi Deepalakshmi Muniswamy

Pa January 27, 2014, bungwe lina loona za ufulu wa anthu ku Karnataka linanena kuti mkulu wa apolisi ku Old Hubli anaphwanya ufulu wa M’bale Sundeep Muniswamy. Linatero chifukwa chakuti apolisi sanathandize m’baleyu pamene anaukiridwa ndi gulu la anthu pa June 28, 2011. Bungweli  linati wapolisiyo ayenera kulangidwa chifukwa chosathandiza anthu. Linanenanso kuti M’bale Muniswamy ayenera kupepesedwa ndi ndalama zokwana madola 326 a ku United States. Linati ndalamazi ziyenera kuchokera ku malipiro a wapolisiyu.

M’bale Muniswamy anati iye ndi banja lake akuthokoza Yehova kuti chilungamo chachitika pa nkhaniyi ndipo sasiya kulalikira mopanda mantha. Nkhani ya m’baleyu yalimbikitsa kwambiri abale ndi alongo ndipo sakukayikira kuti Yehova aziwateteza. Nkhaniyi yakumbutsanso akuluakulu a boma kuti aziteteza ufulu wa Mboni za Yehova ku Karnataka. Koma pali mlandu wina wokhudza M’bale Muniswamy ndi mnzake umene udakali kukhoti.

KYRGYZSTAN Khoti Lalikulu M’dzikoli Lavomereza Kuti Akhristu Asamakakamizidwe Usilikali

Pa November 19, 2013, anthu amene amakana ntchito ya usilikali chifukwa cha chikumbumtima chawo anasangalala kwambiri. Khoti lalikulu linagamula mlandu wina wokhudza a Mboni za Yehova okwana 11. Linanena kuti zimene boma limachitira anthu okana usilikali n’zosemphana ndi malamulo. Boma linkanena kuti munthu akakana usilikali n’kumagwira ntchito zina ayenera kupereka ndalama zake kuti zikathandize asilikali. Linkanenanso kuti munthu akamaliza kugwira ntchito zinazo ayenera kulembedwa m’kaundula wa anthu amene angaitanidwe ku usilikali nthawi ina iliyonse. Khotilo linanena kuti kumeneku n’kuphwanya ufulu wa anthu amene akana usilikali. Chakumayambiriro kwa chaka cha 2014, khotili linalamula kuti chigamulochi chigwirenso ntchito pa milandu ya a Mboni za Yehova okwana 14  ndipo linanena kuti iwo alibe mlandu uliwonse. Gulu lathu lakhala likuyesetsa kwa zaka 7 kuti pakhale ufuluwu ndipo tsopano zatheka. Tikuyamikira kuti abale athu amakonda mtendere ndipo izi zalemekeza kwambiri dzina la Yehova komanso zathandiza kuti tikhale ndi ufulu wolambira ku Kyrgyz Republic.

Kyrgyzstan: Milandu ya abalewa inapita kukhoti lalikulu kwambiri ku Kyrgyzstan

NIGERIA “Yehova Anandithandiza”

A Mboni za Yehova ku Abia, amaopsezedwa kapena kuzunzidwa chifukwa chokana kulowa m’kagulu kamene kamachita zachiwawa kapena zamizimu. * Tsiku lina m’mawa kumayambiriro kwa November mu 2005, kagulu kena ka  m’mudzi wa Asaga Ohafia kanalowa m’nyumba ya M’bale Emmanuel Ogwo. Anatenga katundu wa m’baleyu ndi mkazi wake ati kuti akapezere ndalama zothandiza kagulu kawoko. Anangowasiyira zovala zimene anavala basi. Mu 2006, anthu anathamangitsa m’baleyu m’mudzi wawo. M’baleyu ndi mkazi wake anakakhala kwa m’bale wina m’mudzi wina. Chaka chotsatira, m’baleyu anabwerera kwawo koma ankakakamizidwabe kuti alowe gululo komanso sanabwezeredwe katundu wake.

Koma pa April 15, 2014, khoti lina linagamula kuti M’bale Ogwo ali ndi ufulu wolowa kapena kukana kulowa gulu lililonse kapena chipembedzo chilichonse. M’baleyu anabwezeredwa katundu wake ndipo masiku ano abale ndi alongo sazunzidwa chifukwa cha zimenezi. Panopa, abale ndi alongo a ku Asaga Ohafia amalalikira momasuka.

Pofotokoza zimene zinachitika khotilo litapereka chigamulochi, M’bale Ogwo anati: “Ndinasangalala koopsa. Mtima wonse unali mbee. Ndinkaona kuti Yehova wawina mlandu ndipo angelo ali nane. Yehova anandithandiza.”

RUSSIA Khoti Linagamula Kuti Asaletse Webusaiti ya jw.org

Nkhani za milandu zimene zachitika ku Russia “zathandiza kupititsa patsogolo uthenga wabwino m’malo moulepheretsa.” (Afil. 1:12) Ngakhale zili choncho akuluakulu a boma ena satifunirabe zabwino. Koma abale athu sakubwerera m’mbuyo ndipo Yehova akuwadalitsa.

Nkhani ina inachitika mumzinda wa Tver. Mu 2013 akuluakulu a boma ena anakasuma kukhoti kuti webusaiti ya jw.org iletsedwe m’dziko lonse la Russia. Khotili silinadziwitse a Mboni za Yehova nkhaniyi koma linangogamula kuti  webusaitiyi iletsedwedi. Abale atamva zimenezi anachita apilo nkhaniyi. Pa January 22, 2014, khoti lina lalikulu linasintha chigamulocho n’kuweruza nkhaniyi motikomera. Timayamikira kwambiri Yehova chifukwa choyankha mapemphero a abale ndi alongo padziko lonse. Panopa, abale athu ku Russia zikuwayendera ndithu chifukwa choti ali ndi mwayi woona zinthu pa webusaiti ya jw.org.

TURKEY Dzikoli Silikuperekabe Ufulu Wokana Ntchito ya Usilikali

M’bale Bariş Görmezo wa ku Turkey anakhala m’ndende zaka 4 chifukwa chokana ntchito ya usilikali. Anazunzidwa kwambiri moti asilikali anamumenya ndi zibonga komanso mateche. Atafika kundende anazunzikanso. M’baleyu ndi wamtali moti sankakwana pabedi lakundende ndipo apolisi anamuuza kuti azingodzipinda pamabedi awiri. Mwamwayi mpingo unatumiza matiresi abwino oti azigonapo.

Mu 2008, M’baleyu ndi anzake ena atatu anakadandaula ku Khoti Loona za Ufulu wa Anthu ku Ulaya kuti akuphwanyiridwa ufulu wawo wokana usilikali chifukwa cha chikumbumtima chawo. Pa June 3, 2014, khotili linagamula mlanduwu mokomera abale anayiwa ndipo linalamula kuti boma la Turkey lilipire zinthu za abalewo zimene zawonongeka. * Aka n’kachitatu kuti khotili ligamule mlandu mokomera Mboni za Yehova ku Turkey pa nkhani zausilikalizi. Panopa palibe m’bale amene ali kundende koma tikudziwa kuti mavutowa adzatha pokhapokha ngati boma la Turkey litapereka ufulu wokana usilikali.

 Malipoti a Milandu Yakale

Azerbaijan: Abale akukumana ndi mavuto ambiri m’dzikoli. Mwachitsanzo apolisi amasokoneza misonkhano, boma limaletsa mabuku athu ena, abale amamangidwa chifukwa cholalikira ndiponso kuphwanyiridwa maufulu osiyanasiyana. Panopa boma likukanitsitsa kuti Mboni za Yehova zilembetse chipembedzo chawo. Zimenezi zachititsa kuti abale akadandaule maulendo 19 ku Khoti Loona za Ufulu wa Anthu Ulaya. Ngakhale pali mavutowa, zinthu zikutiyenderabe, moti chiwerengero cha ofalitsa chikuwonjezereka. Posachedwapa anthu anasangalala kwambiri Baibulo la Dziko Latsopano la Chiazebajani litatulutsidwa.

Eritrea: Abale athu m’dzikoli akutumikirabe Yehova mokhulupirika ngakhale kuti akuzunzidwa. Mayina a abalewa ndi, Paulos Eyassu, Isaac Mogos, ndi Negede Teklemariam ndipo akhala m’ndende zaka 20 kuyambira pa September 24, 1994. Pa April 14, 2014, boma la Eritrea linamanga anthu 150 pa mwambo wa Chikumbutso. Pa gululi panali ophunzira Baibulo, ana oti sanakwanitse zaka ziwiri ndiponso agogo azaka 85. Pa April 27, 2014, tsiku la nkhani ya padera, anthu 30 anamangidwanso. Koma ambiri anamasulidwa.

Kazakhstan: Bungwe loona za zipembedzo linaletsa mabuku athu okwana 14 kuti asamafike m’dzikoli. Abale akuletsedwanso kulalikira m’madera ena kupatulapo pamalo olambirira basi. Zimenezi zachititsa kuti abale pafupifupi 50 amangidwe. Pofuna kuteteza ufulu wolalikira paliponse, abale anakadandaula ku Komiti ya Bungwe la United Nations Yoona za Ufulu wa Anthu ndipo pali milandu 26 imene ikuyembekezera kugamulidwa.

^ ndime 1 Munthu amasankha yekha malinga ndi chikumbumtima chake kuti alowe usilikali kapena agwire ntchito zina.

^ ndime 1 M’timagulu timeneti nthawi zambiri mumakhala amuna am’mudzi umodzi.

^ ndime 2 Mlandu wa Buldu ndi Anzake ku Turkey pa June 3, 2014, nambala yake inali 14017/08.

Onaninso

MAFUNSO OFUNSIDWA KAWIRIKAWIRI

N’chifukwa Chiyani a Mboni za Yehova Salowerera Ndale?

Kodi iwo amasokoneza mtendere m’dziko?