Pitani ku nkhani yake

Pitani ku menyu yachiwiri

Pitani ku mitu ya nkhani

Mboni za Yehova

Chichewa

Buku Lapachaka la Mboni za Yehova la 2015

 ZIMENE ZACHITIKA M’CHAKA CHAPITACHI

Msonkhano Waukulu Kwambiri wa Mboni za Yehova

Msonkhano Waukulu Kwambiri wa Mboni za Yehova

Msonkhano wapachaka wa Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania wa nambala 129, unachitika Loweruka pa October 5, 2013. Anthu okwana 257,294 ochokera m’mayiko 21 anapezekapo kapena kuonerera kudzera pa Intaneti, pa nthawi yomwe msonkhanowu unkachitika. Kenako msonkhanowu anauonetsanso pa vidiyo. Anthu onse amene anaonera msonkhanowu anali ochokera m’mayiko 31 ndipo analipo 1,413,676. Msonkhano wapachakawu unali waukulu kwambiri kuposa misonkhano ina yonse imene inachitikapo m’mbuyomu.

Kuyambira m’ma 1920, tinayamba kulumikiza misonkhano yathu pa telefoni komanso kuiulutsa pa wailesi n’cholinga choti anthu ambiri m’mayiko osiyanasiyana azitha kumvetsera misonkhanoyo. Koma masiku ano kuli Intaneti ndipo ikuthandiza kuti anthu a m’mayiko ndi madera osiyanasiyana, ngakhale akutali kwambiri, azitha kuona ndi kumvetsera  misonkhano pa nthawi imene ikuchitika kapena ikangotha kumene.

Panali ntchito yaikulu zedi yokonzekera kuti msonkhanowu udzaonetsedwe. Pa tsiku limene msonkhanowu unachitika komanso pa tsiku lotsatira, abale ena analumikiza makina oonetsera vidiyo pa Intaneti, ndipo ankayendetsa zonse ali ku ofesi ya ku Brooklyn, ku New York. Iwo anaonetsetsa kuti kwa masiku onse awiri, masana ndi usiku womwe, pali anthu amene akuyendetsa zinthu pamakina. Izi zinali choncho chifukwa msonkhanowu unaonetsedwa m’madera ndi mayiko osiyanasiyana ndipo nthawi inali yosiyananso kwambiri.