ANTHU ambiri akubwera m’gulu la Yehova, choncho pakufunika kumanga zinthu monga Nyumba za Ufumu, Malo a Misonkhano, malo a sukulu zophunzitsa Baibulo, maofesi a omasulira mabuku ndiponso zinthu zina. Chifukwa cha zimenezi, Bungwe Lolamulira linakhazikitsa Dipatimenti Yoona za Mapulani ndi Zomangamanga Padziko Lonse (WDC), mu October 2013. Dipatimentiyi imayang’anira ntchito zomangamanga padziko lonse kuti zizigwiridwa bwino popanda kuwononga ndalama zambiri. Dipatimentiyi ili kulikulu lathu ku Brooklyn, New York ndipo imayang’aniridwa ndi Komiti Yoona za Ntchito Yofalitsa Mabuku ya Bungwe Lolamulira.

 Ndiye palinso Dipatimenti Yoona za Mapulani ndi Zomangamanga M’mayiko Angapo. Dipatimentiyi ili pansi pa dipatimenti imene taitchula ija ndipo yakhazikitsidwa ku ofesi ya nthambi ya ku Australia, ku Germany, ku South Africa ndi ku United States. Dipatimentiyi imayang’anira ntchito zomanga m’mayiko angapo ndipo ili ndi cholinga choti ntchito yomanga Nyumba za Ufumu iziyenda mwamsanga. Poyamba, m’mayiko ena munali makomiti oyang’anira ntchitoyi ndipo m’mayiko osauka munali pulogalamu yapadera yothandiza kumanga Nyumba za Ufumu. Koma panopa Dipatimenti Yoona za Mapulani ndi Zomangamanga M’mayiko Angapo iziyang’anira ndiponso kuthandiza kuti ntchito zomangamanga ziziyenda mwamsanga.

Pa nthambi iliyonse palinso Dipatimenti Yoona za Mapulani ndi Zomangamanga yomwe imayang’anira zinthu m’dzikolo. Dipatimentiyi imadziwitsa abale a mu Komiti ya Nthambi mmene ntchito yomanga Nyumba za Ufumu ndiponso Malo a Misonkhano ikuyendera. Chosangalatsa n’chakuti izi zathandiza kuti nthambi iliyonse izitha kupeza yokha atumiki a nthawi zonse ogwira ntchito zomangamanga kuti azithandiza abale kumanga Nyumba za Ufumu ndi Malo a Misonkhano.

Pofika mu April 2014, panali ntchito zomangamanga zikuluzikulu zokwana 270. Zina mwa ntchitozi zinali zomanga maofesi 90 a omasulira mabuku, Malo a Misonkhano 35 ndiponso ntchito zina m’maofesi a nthambi zokwana 130. Ndiye palinso ntchito yomanga kapena kukonza Nyumba za Ufumu zoposa 14,000.

Tikusangalala kuti Yehova wagwirizanitsa anthu ake ndipo akugwira ntchito ya zomangamanga mosaganizira kusiyana kwa mayiko, zikhalidwe kapena zilankhulo. Izitu zikulemekeza kwambiri dzina lake. M’bale Dan  Molchan wa mu Komiti Yoona za Atumiki a pa Beteli anati: “Tidakali ndi ntchito yambiri choncho timayamikira kwambiri mapemphero komanso zopereka za abale ndi alongo athu zimene zikuthandiza pa ntchitoyi. Timayamikiranso kwambiri abale ndi alongo amene amadzipereka kuti athandize pa ntchito ya zomangamangayi.”