Yehova Mulungu anauzira mneneri Yesaya kulosera kuti: “M’malo mwa mkuwa, ndidzabweretsa golide. M’malo mwa chitsulo, ndidzabweretsa siliva. M’malo mwa mtengo, ndidzabweretsa mkuwa ndipo m’malo mwa miyala, ndidzabweretsa chitsulo.” (Yes. 60:17) Lembali likusonyeza kuti zinthu wamba zikulowedwa m’malo ndi zinthu zamtengo wapatali. Izi zikuimira kupita patsogolo kwa gulu la Yehova. M’chaka chapitachi ulosiwu wakwaniritsidwa m’njira zambiri. Kunena zoona zinthu zakhala zikutiyendera bwino kwambiri m’nthawi yamapeto ino.—Mat. 24:3.