Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

 DOMINICAN REPUBLIC

Ufulu Wosayembekezereka Kenako N’kuletsedwanso

Ufulu Wosayembekezereka Kenako N’kuletsedwanso

Ufulu Wosayembekezereka

Manuel Hierrezuelo anaphedwa pa nthawi imene ankafunsidwa mafunso ndi akuluakulu a boma

Pa nthawi yonse ya bani, banja la a Johnson ndi la a Brandt linakhalabe m’dziko la Dominican Republic. M’bale Johnson anati: “Tsiku lina ine ndi M’bale Brandt tinaitanidwa kuti tikafunsidwe mafunso. Izi zisanachitike, akuluakulu a boma anaitana M’bale Manuel Hierrezuelo kuti akamufunsenso.” Koma Manuel anaphedwa pa nthawi yomufunsayo moti anamwalira ali wokhulupirika kwa Mulungu. Ndiye kodi abale awiri amene anaitanidwawa zinawathera bwanji? M’bale Johnson anati: “Titafika ankatifunsa mafunso payekhapayekha ndipo ankajambula zonse zimene tinkanena. Kenako anatisiya. Koma patangotha miyezi iwiri, tinamva mu nyuzipepala kuti Trujillo akufuna achotse lamulo loletsa ntchito ya Mboni za Yehova.”

Lamulo loletsali lisanakhazikitsidwe mu 1950, m’dzikoli munali ofalitsa 261. Koma pamene ankalichotsa mu 1956, munali ofalitsa 522. Abale anasangalala kwambiri kumva kuti tsopano azilalikira momasuka pambuyo pa zaka 6 zimene ankamangidwa, kuletsedwa kulalikira komanso kusakidwasakidwa.

Zinthu zitangosintha, abale ndi alongo anayambiratu kupanga dongosolo la ntchito yolalikira. Iwo anafufuza malo oti azisonkhana, analemba mapu atsopano a magawo komanso anakonza mafaelo atsopano a mipingo. Iwo anasangalala kwambiri chifukwa ankatha kuodetsa mabuku n’kumalandira bwinobwino. Ufulu umene anapatsidwawu anaugwiritsa ntchito bwino.  Iwo ankalalikira kwambiri moti pamene miyezi itatu inkatha, mu November 1956, ofalitsa anali atafika 612.

Atsogoleri Achipembedzo Ankalimbana ndi Mboni

Chikalata chimene wansembe wina analemba chofotokoza zoyenera kuchita kuti mabuku athu asamafike m’dzikoli

Koma nthawi yomweyo atsogoleri a tchalitchi cha Katolika anayamba kuipitsa mbiri ya Mboni. Iwo anapezerapo mwayi pa pangano limene Trujillo anachita ndi Papa ndipo anamukakamiza kuti asalole a Mboni m’dzikoli. Wansembe wina analemba chikalata chopita kwa nduna yoona za m’dzikolo. M’chikalatacho anapempha kuti boma limuthandize “pochenjeza anthu a m’dzikoli chifukwa akhoza kusokonezedwa kwambiri ndi gulu loopsa la Mboni za Yehova.”

Wansembeyo ananena kuti ankafuna “kulepheretsa ntchito yokopa anthu imene a Mboni za Yehova amagwira.” Iye anapemphanso kuti mabuku athu  aletsedwe m’dzikolo, makamaka buku lakuti The Truth Shall Make You Free ndiponso magazini a Nsanja ya Olonda.

Ntchito Yathu Inaletsedwanso

Akuluakulu a boma amene ankagwirizana ndi atsogoleri achipembedzowa anayambanso kulimbana ndi Mboni. Mu June 1957, munthu wina waudindo waukulu mu chipani cholamula analembera kalata pulezidenti. Iye anati: “A Mboni za Yehova akusokoneza anthu ndipo akuwachititsa kuti asamakonde dziko lathu. Panopa ndikukonza zoti pakhale misonkhano imene ingathandize kuthana ndi zimene akuchitazi.”

Pofotokoza zotsatira za kalatayi, buku lina linati: “Mu June, July ndi August 1957, nyuzipepala zinalemba mfundo zambirimbiri zimene akuluakulu a boma ankanena polimbana ndi Mboni. Ankanena kuti iwo ndi ‘oukira boma komanso osokoneza kwambiri.’ Zinthu zinafika poipa pamene wansembe wina analankhula pa wailesi ya Trujillo n’kunena kuti a Mboni ndi oukira boma ndipo anthu ake ndi ‘osokoneza, odziwa kukopa anthu, zigawenga komanso adani achinyengo.’ Ndiyeno chikalata china chimene chinasainidwa ndi mabishopu awiri akuluakulu chinapempha ansembe kuti ateteze anthu awo n’cholinga choti asasokonezedwe ndi ‘mabodza oopsa’ a Mboniwo.

Zimene achipembedzo ndi abomawa ankafuna zinathekadi. Mu July, boma la Dominican Republic linaletsanso ntchito ya Mboni za Yehova. Pasanapite nthawi, abale athu anayamba kumenyedwa ndiponso kuzunzidwa ndi apolisi. Abale okwana 150 anamangidwa.