“Ochenjera Ngati Njoka Koma Oona Mtima Ngati Nkhunda”

Abale ndi alongo ankafunika kupeza mabuku ndi magazini pa nthawi ya bani koma zinali zovuta kwambiri. Abale ambiri ankagwidwa n’kutsekeredwa m’ndende kawirikawiri.

Mlongo wina dzina lake Juanita Borges anati: “Mu 1953, ndinaphunzira Baibulo ndipo ndinkadziwa kuti nthawi iliyonse ndikhoza kumangidwa chifukwa chokhala wa Mboni za Yehova. Ndiyeno tsiku lina mu November 1958, ndinapita kukaona mlongo wina dzina lake Eneida Suárez. Ndili komweko, apolisi anafika n’kutigwira poganiza kuti tikuchita msonkhano. Tinauzidwa kuti tikhala m’ndende miyezi itatu komanso aliyense alipire chindapusa cha ndalama zokwana mapeso 100 (pa nthawiyo ndalamazo zinali zofanana ndi madola 100 a ku United States).”

Apolisi anali ndi mapepala okhala ndi mayina ndiponso mfundo zina zofunika zokhudza abale ndi alongo athu.

Boma linachita chilichonse chimene likanatha kuti lilepheretse a Mboni kusonkhana koma sizinatheke. A Mboniwo ankayesetsa kukhala “ochenjera ngati njoka koma oona mtima ngati nkhunda.” (Mat. 10:16) Mlongo wina  dzina lake Andrea Almánzar anati: “Tinkafika ku misonkhano pa nthawi zosiyanasiyana. Tikamaliza tinkayenera kuchokanso pa nthawi zosiyana n’cholinga choti anthu asatikayikire. Choncho enafe tinkafika kunyumba usiku.”

M’bale wina dzina lake Jeremías Glass anabadwa pa nthawi imene bambo ake anali kundende. Iye anakhala wofalitsa ali ndi zaka 7 mu 1957. Abale ndi alongo ankasonkhana m’nyumba yawo ndipo iye akukumbukira zimene ankachita kuti anthu asawadziwe. M’baleyu anafotokoza kuti: “Aliyense amene ankasonkhana ankapatsidwa pepala lokhala ndi nambala imene inkasonyeza nthawi imene ayenera kuchoka pamalopo. Tikamaliza misonkhano, bambo anga ankandiuza kuti ndiime pakhomo kuti ndiziona manambala a anthuwo. Ndinkawauzanso kuti achoke awiriawiri komanso kuti adutse njira zosiyana pochoka.”

Tinkachitanso misonkhano yathu pa nthawi zimene anthu ambiri sakanadziwa. Mwachitsanzo, mlongo wina dzina lake Mercedes García anaphunzitsidwa Baibulo ndi amalume ake dzina lawo Pablo González. Amayi a mlongoyu anamwalira iye ali ndi zaka 7 ndipo pa nthawiyo bambo ake anali kundende. Iye anatsala ndi azichimwene ake atatu ndi azichemwali ake 6. Mercedes anabatizidwa ali ndi zaka 9 mu 1959. Pofuna kuti anthu asadziwe, abale anakonza zoti nkhani ya ubatizoyo ikambidwe m’bandakucha. Nkhaniyo inakambidwa kunyumba ya m’bale wina ndipo anthu anabatizidwa mumtsinje wa Ozama umene umadutsa mulikulu la dzikoli. Mercedes anati: “Pa nthawi ya 5:30 m’mawa tinali tikubwerera kunyumba koma anthu ena onse anali atangoyamba kumene kudzuka.”