Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

 DOMINICAN REPUBLIC

Ubwenzi wa Trujillo ndi Tchalitchi cha Katolika

Ubwenzi wa Trujillo ndi Tchalitchi cha Katolika

KODI zinthu zinali bwanji pakati pa Trujillo ndi tchalitchi cha Katolika? Katswiri wina wounika za ndale anati: “Trujillo anali pulezidenti kuyambira mu 1930 mpaka mu 1961. Pa nthawi yonseyi, boma la Dominican Republic linkagwirizana kwambiri ndi tchalitchichi. Pulezidenti woponderezayu ankakonda tchalitchichi ndipo akuluakulu a tchalitchi ankamuikira kumbuyo.”

Mu 1954, Trujillo anapita ku Rome n’kukasaina pangano ndi Papa. Munthu wina amene anali mnzake wa pulezidentiyu analemba kuti: “M’dziko lino la Dominican Republic, tchalitchi cha Katolika chili pambuyo pa ulamuliro wa Trujillo ndipo panganoli lathandiza kuti chizimuikira kumbuyo kwambiri. Atsogoleri a tchalitchi chimenechi amalimbikitsa ulamuliro wake ndipo amachita zimenezi motsogoleredwa ndi mabishopu akuluakulu monga Ricardo Pittini ndi Octavio Beras.”

 Mnzake wa Pulezidenti uja ananenanso kuti: ‘Papa amayesetsa kupeza mpata woti apereke moni kwa Trujillo. . . . Mu 1956, ku Ciudad Trujillo kunachitika msonkhano wa Chikatolika ndipo iye [Trujillo] ndi amene anapereka ndalama zoyendetsera msonkhanowu. Amene ankaimira Papa pa msonkhanowu anali Francis Cardinal Spellman ndipo anabweretsa uthenga wa mafuno abwino wochokera kwa Papayo. Spellman anachoka ku New York ndipo atafika m’dzikoli, pulezidentiyu ndi amene anapita kukamulandira mwaulemu. Anahagana kwambiri moti zithunzi zawo zinali patsamba loyamba la nyuzipepala ya tsiku lotsatira.’

Mu 1960, magazini ina inalemba kuti: “Trujillo adakagwirizanabe ndi tchalitchi cha Katolika. Bishopu wamkulu dzina lake Ricardo Pittini ndi wazaka 83 ndipo panopa saona. Koma zaka 4 zapitazo, anasainira kalata yopita ku nyuzipepala yotchuka ya ku New York ndipo anatamanda kwambiri Trujillo. Ananena kuti ‘pulezidenti “woponderezayu” amakondedwa komanso kulemekezedwa ndi anthu ake.’”

Koma pambuyo poikira kumbuyo ulamuliro wankhanza wa Trujillo kwa zaka 30, akuluakulu a tchalitchi cha Katolika anayamba kusintha maganizo. Munthu wina analemba kuti: “Anthu odana ndi ulamuliro woponderezawu anayamba kuchuluka. Kenako anthu ankafuna kuthandiza kuti m’dzikoli mukhale demokalase. Choncho akuluakulu a tchalitchichi anakakamizika kuti asinthe maganizo n’kusiya kuikira kumbuyo Trujillo.”

Ndiyeno mu 2011, tchalitchichi chinakakamizika kuti chipepese anthu a ku Dominican Republic. Kalata imene akuluakulu ake analemba inatuluka munyuzipepala ina ndipo inati: ‘Tikupepesa kwambiri chifukwa choti tinkalakwitsa. Tinkachita zosemphana ndi zimene timakhulupirira, ntchito yathu komanso udindo umene tapatsidwa. Tikupempha kuti anthu onse m’dzikoli atimvetse komanso atikhululukire.’